Kalata ya Yakobo 1:1-27
1 Ine Yakobo,+ kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikulembera mafuko 12 amene anamwazikana mʼmadera osiyanasiyana.
Landirani moni!
2 Abale anga, muzisangalala kwambiri pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana,+
3 chifukwa monga mukudziwira, chikhulupiriro chanu chikakhalabe cholimba pamene mukuyesedwa, mumaphunzira kukhala opirira.+
4 Koma lolani kuti kupirirako kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda cholakwa pa mbali iliyonse, kapena kuti mukhale ndi makhalidwe onse abwino.+
5 Choncho ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu+ ndipo adzamupatsa,+ chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.*+
6 Koma azipempha ndi chikhulupiriro,+ asamakayikire ngakhale pangʼono,+ chifukwa amene akukayikira ali ngati funde lapanyanja limene limatengeka ndi mphepo nʼkumawindukawinduka.
7 Munthu wotero asayembekezere kuti adzalandira kanthu kuchokera kwa Yehova.*
8 Iye ndi wokayikakayika+ ndipo zochita zake zonse zimasinthasintha.
9 Mʼbale wonyozeka asangalale* chifukwa walemekezedwa ndi Mulungu,+
10 ndipo wachuma asangalale chifukwa waphunzira kukhala wodzichepetsa,+ chifukwa mofanana ndi duwa lakutchire, iye adzafota.
11 Dzuwa likatuluka limatentha kwambiri nʼkufotetsa zomera ndipo maluwa a zomerazo amathothoka moti kukongola kwake kumatha. Mofanana ndi zimenezi munthu wachumayo adzafa ali mkati mofunafuna chuma.+
12 Wosangalala ndi munthu amene akupirira mayesero,+ chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto* ya moyo,+ imene Yehova* analonjeza onse amene akupitiriza kumukonda.+
13 Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Chifukwa Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.
14 Koma munthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako chake chimene chimamukopa* ndi kumukola.+
15 Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabereka tchimo. Ndipo tchimo likachitika, limabweretsa imfa.+
16 Abale anga okondedwa, musasocheretsedwe.
17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba.+ Imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zakuthambo,+ amene sasintha ngati mthunzi umene umasunthasuntha.+
18 Mwakufuna kwake, iye anatibereka pamene tinakhulupirira mawu ake omwe ndi choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira pa zolengedwa zake.+
19 Abale anga okondedwa, dziwani izi: Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule+ komanso asamafulumire kukwiya,+
20 chifukwa munthu amene wakwiya sachita zinthu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu.+
21 Choncho siyani khalidwe lililonse lonyansa ndipo chotsani zoipa zilizonse* zimene zatsalira mwa inu.+ Modzichepetsa vomerezani kuti mawu amene angathe kukupulumutsani adzalidwe mwa inu.
22 Komabe muzichita zimene mawu amanena,+ osati kungomva chabe, nʼkumadzipusitsa ndi maganizo abodza.
23 Chifukwa ngati munthu amangomva mawu koma osachita,+ amafanana ndi munthu amene akudziyangʼanira nkhope yake pagalasi.
24 Iye amadziyangʼana nʼkuchokapo ndipo nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani.
25 Koma amene amayangʼanitsitsa mulamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu ndipo amapitiriza kuliyangʼanitsitsa, adzakhala wosangalala ndi zimene akuchita+ chifukwa chakuti si munthu amene amangomva nʼkuiwala, koma amene amachita zimene wamvazo.
26 Ngati munthu akuganiza kuti amalambira Mulungu,* koma satha kulamulira lilime lake,+ akudzipusitsa* ndipo kulambira kwake nʼkopanda phindu.
27 Kulambira* koyera komanso kosadetsedwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ amene akukumana ndi mavuto*+ komanso kupewa kuti dzikoli likuchititseni kukhala ndi banga.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amapereka popanda kupezera aliyense zifukwa.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzitamandire.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “chimamukopa ngati nyambo.”
^ Mabaibulo ena amati, “zoipa zambirimbiri.”
^ Kapena kuti, “ndi wopembedza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “akupusitsa mtima wake.”
^ Kapena kuti, “Chipembedzo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasautso awo.”