Yeremiya 1:1-19

  • Yeremiya anasankhidwa kuti akhale mneneri (1-10)

  • Masomphenya a mtengo wa amondi (11, 12)

  • Masomphenya a mphika (13-16)

  • Yeremiya analimbikitsidwa kuti agwire ntchito yake (17-19)

1  Awa ndi mawu a Yeremiya* mwana wa Hilikiya, mmodzi wa ansembe a ku Anatoti,+ mʼdera la Benjamini.  Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova mʼmasiku a Yosiya+ mwana wa Amoni,+ mfumu ya Yuda, mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya.  Yeremiya analandiranso mawuwo mʼmasiku a Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda mpaka kumapeto kwa chaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, komanso mpaka pamene anthu a mu Yerusalemu anatengedwa kupita ku ukapolo mʼmwezi wa 5.+  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:   “Ndisanakuumbe mʼmimba, ndinkakudziwa,*+Ndipo usanabadwe,* ndinakusankha* kuti ugwire ntchito yopatulika.+ Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”   Koma ine ndinati: “Ayi musatero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Ine sinditha kulankhula+ chifukwa ndine mwana.”+   Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana,’ Chifukwa ukuyenera kupita kwa anthu onse kumene ndidzakutume,Ndipo ukanene zonse zimene ndakulamula.+   Usachite mantha ndi maonekedwe awo,+Chifukwa ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,’+ akutero Yehova.”  Kenako Yehova anatambasula dzanja lake nʼkukhudza pakamwa panga.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Ndaika mawu anga mʼkamwa mwako.+ 10  Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kudzala.”+ 11  Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani Yeremiya?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nthambi ya mtengo wa amondi.”* 12  Yehova anandiuza kuti: “Waona bwino, chifukwa ndili maso ndipo ndine wokonzeka kukwaniritsa mawu anga.” 13  Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti: “Ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphika wa kukamwa kwakukulu umene ukuwira* ndipo wafulatira kumpoto koma kukamwa kwake kwaloza kumʼmwera.” 14  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Tsoka lidzachokera kumpotoNdipo lidzagwera anthu onse okhala mʼdzikoli.+ 15  Yehova wanena kuti, ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto.+Iwo adzabwera ndipo aliyense adzakhazikitsa mpando wake wachifumu,Pakhomo la mageti a Yerusalemu.+Iwo adzaukira mpanda wake wonseNdi mizinda yonse ya Yuda.+ 16  Ndipo ine ndidzapereka zigamulo zanga pa anthu anga chifukwa cha zoipa zawo zonse,Chifukwa iwo andisiya+Ndipo akupereka nsembe zofukiza kwa milungu ina+Komanso akugwadira ntchito za manja awo.’+ 17  “Koma iwe ukonzekere kugwira ntchito,*Ndipo upite ukawauze zonse zimene ndakulamula. Usachite nawo mantha,+Kuti ndisakupangitse kuchita nawo mantha kwambiri. 18  Chifukwa lero ndakupanga kuti ukhale mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,Chipilala cha chitsulo ndi makoma akopa* kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+Kuti mafumu a Yuda, akalonga ake,Ansembe ake ndi anthu amʼdzikoli asakugonjetse.+ 19  Iwo adzamenyana nawe ndithu,Koma sadzakugonjetsa,Chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe+ kuti ndikupulumutse.’”

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza kuti “Yehova Amakweza.”
Kapena kuti, “ndinakusankha.”
Kapena kuti, “ndinakupatula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “usanatuluke mʼmimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nthambi ya wochititsa kukhala maso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene aukupizira,” kusonyeza kuti moto umene uli pansi pa mphikawo ukuyaka kwambiri.
Mʼchilankhulo choyambirira, “umange mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “amkuwa.”