Yeremiya 12:1-17

  • Kudandaula kwa Yeremiya (1-4)

  • Zimene Yehova anayankha (5-17)

12  Inu Yehova, ndikabweretsa dandaulo langa kwa inu,Komanso ndikamalankhula ndi inu nkhani zokhudza chilungamo, mumasonyeza kuti ndinu wolungama.+ Koma nʼchifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino,+Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu amene amachita zachinyengo amakhala opanda nkhawa?   Munawadzala ndipo iwo anazika mizu. Akula ndipo abala zipatso. Amakutchulani pafupipafupi, koma mtima wawo uli kutali* kwambiri ndi inu.+   Koma inu Yehova, mukundidziwa bwino+ ndipo mumandiona.Mwafufuza mtima wanga ndipo mwapeza kuti ndine wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,Ndipo muwaike padera poyembekezera tsiku limene adzaphedwe.   Kodi dzikoli likhalabe lofota mpaka liti?Kodi zomera zamʼmunda uliwonse zikhalabe zouma mpaka liti?+ Chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu amʼdzikoli akuchita,Zilombo zakutchire ndi mbalame zawonongedwa. Chifukwa anthuwo akuti: “Iye sakuona zimene zidzatichitikire.”   Ngati ukutopa pothamanga ndi anthu oyenda pansi,Ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?+ Ukhoza kuona kuti ndiwe wotetezeka mʼdziko lamtendere,Koma kodi udzatani ukadzakhala mʼnkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano?   Chifukwa ngakhale abale ako enieni, anthu a mʼnyumba ya bambo ako,Akuchitira zinthu zachinyengo.+ Iwo akunenera zinthu zoipa mofuula. Usawakhulupirire,Ngakhale atamalankhula zinthu zabwino kwa iwe.   “Nyumba yanga ndaisiya.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka mʼmanja mwa adani ake.+   Cholowa changa chakhala ngati mkango kwa ine munkhalango. Wokondedwa wanga wandibangulira. Nʼchifukwa chake ndadana naye.   Cholowa changa chili ngati mbalame yanthenga zamitundu yosiyanasiyana imene imadya nyama.Mbalame zina zodya nyama zaizungulira nʼkuiukira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zamʼtchire,Bwerani kuti mudzadye.+ 10  Abusa ambiri awononga munda wanga wa mpesa.+Apondaponda malo omwe ndi cholowa changa.+ Malo omwe ndi cholowa changa chosiririka awasandutsa bwinja moti palibe aliyense amene akukhalamo. 11  Cholowa changacho chasanduka chipululu, Ndipo chafota.*Chawonongeka pamaso panga,+ Dziko lonse lakhala bwinja,Koma palibe aliyense amene zikumukhudza.+ 12  Anthu owononga adutsa mʼnjira zonse zodutsidwadutsidwa zamʼchipululu,Chifukwa lupanga la Yehova likuwononga anthu kuchokera kumalekezero a dziko kukafika kumalekezero ena a dziko.+ Ndipo palibe munthu aliyense amene ali pamtendere. 13  Afesa tirigu koma akolola minga.+ Agwira ntchito yotopetsa koma osapeza phindu lililonse. Iwo adzachita manyazi ndi zokolola zawoChifukwa mkwiyo waukulu wa Yehova udzawayakira.” 14  Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula mʼdziko lawo+ ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo. 15  Koma ndikadzawazula, ndidzawachitiranso chifundo moti ndidzabwezeretsa aliyense wa iwo pacholowa chake ndi pamalo ake. 16  Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzayesetsa kuphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ ngati mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga. 17  Koma akadzakana kumvera, ine ndidzazulanso anthu a mtundu umenewo. Ndidzawazula nʼkuwawononga,” akutero Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mmene akumvera mumtima mwawo.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zawo zili kutali.”
Mabaibulo ena amati, “chikundilirira.”