Yeremiya 13:1-27

  • Lamba wa nsalu amene anawonongeka (1-11)

  • Mitsuko ya vinyo idzaphwanyidwa (12-14)

  • Yuda amene sangathenso kusintha adzatengedwa kupita ku ukapolo (15-27)

    • “Kodi Mkusi angasinthe khungu lake?” (23)

13  Yehova anandiuza kuti: “Pita ukagule lamba wansalu ndipo ukamumange mʼchiuno mwako, koma usakamuviike mʼmadzi.”  Choncho ndinakagula lambayo mogwirizana ndi mawu a Yehova ndipo ndinamumanga mʼchiuno mwanga.  Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kachiwiri kuti:  “Tenga lamba wagula uja, amene wamumanga mʼchiuno ndipo unyamuke nʼkupita kumtsinje wa Firate. Kumeneko ukamubise mumngʼalu wamʼphanga.”  Choncho ndinapita nʼkukabisa lambayo pafupi ndi mtsinje wa Firate mogwirizana ndi zimene Yehova anandilamula.  Koma patapita masiku ambiri Yehova anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kumtsinje wa Firate ndipo ukatenge lamba amene ndinakulamula kuti ukabise kumeneko.”  Choncho ndinapita kumtsinje wa Firate ndipo ndinakumba pamalo amene ndinabisapo lambayo nʼkumutenga. Koma ndinaona kuti anali atawonongeka moti sakanagwiranso ntchito iliyonse.  Kenako Yehova anandiuzanso kuti:  “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi lamba ameneyu, ndidzawononga kunyada kwa Yuda ndiponso kunyada kwakukulu kwa Yerusalemu.+ 10  Anthu oipawa, amene akukana kumvera mawu anga,+ amene mouma khosi amatsatira zofuna za mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina, akuitumikira komanso kuigwadira, adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’ 11  ‘Mofanana ndi mmene lamba amagwirira mʼchiuno mwa munthu, ine ndinachititsa nyumba yonse ya Isiraeli ndi nyumba yonse ya Yuda kundimamatira,’ akutero Yehova. ‘Ndinachita zimenezi kuti iwo akhale anthu anga,+ atchukitse dzina langa,+ anditamande ndi kukhala chinthu changa chokongola. Koma iwo sanandimvere.’+ 12  Ukawauzenso uthenga wakuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo.”’ Ukakawauza zimenezi akakufunsa kuti, ‘Kodi ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo?’ 13  Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikuledzeretsa anthu onse amʼdzikoli,+ mafumu amene akukhala pampando wachifumu wa Davide, ansembe, aneneri ndi anthu onse amene amakhala mu Yerusalemu. 14  Ndipo ndidzawombanitsa munthu ndi mnzake, abambo chimodzimodzinso ana,” akutero Yehova.+ “Sindidzawakomera mtima, kuwamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo. Palibe chimene chidzandilepheretse kuti ndiwawononge.”’+ 15  Tamverani ndipo mutchere khutu. Musadzikweze chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi. 16  Perekani ulemerero kwa Yehova Mulungu wanuAsanabweretse mdima,Komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa. Mudzayembekezera kuwala,Koma iye adzabweretsa mdima waukulu,Ndipo adzachititsa kuti mdimawo ukhale wandiweyani.+ 17  Ndipo mukakana kumvera,Ndidzalira mobisa chifukwa cha kunyada kwanu. Ndidzagwetsa misozi yambiri ndipo misozi idzatsika kuchokera mʼmaso mwanga+Chifukwa nkhosa za Yehova+ zagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina. 18  Uza mfumu ndi mayi a mfumu kuti,+ ‘Khalani pamalo apansi,Chifukwa chisoti chanu chaulemerero chidzagwera pansi kuchoka kumutu kwanu.’ 19  Mizinda yakumʼmwera yatsekedwa* ndipo palibe amene angaitsegule. Anthu onse a mu Yuda atengedwa kupita ku ukapolo. Onse atengedwa kupita ku ukapolo popanda wotsala.+ 20  Kweza maso ako kuti uone anthu amene akubwera kuchokera kumpoto.+ Kodi ziweto zimene anakupatsa, nkhosa zako zokongola zija zili kuti?+ 21  Kodi udzanena chiyani chilango chako chikadzabweraKuchokera kwa anzako apamtima, amene unkagwirizana nawo kuchokera pa chiyambi?+ Kodi sudzamva zowawa za pobereka ngati za mkazi amene akubereka mwana?+ 22  Ndipo ukadzanena mumtima mwako kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+ Udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako chifukwa cha kuchuluka kwa machimo ako+ Ndipo zidendene zako zazunzidwa. 23  “Kodi Mkusi* angasinthe khungu lake, kapena kodi kambuku angasinthe mawanga ake?+ Ngati angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti inunso amene munaphunzitsidwa kuchita zinthu zoipa,Mungathe kuchita zinthu zabwino. 24  Choncho ndidzakumwazani ngati mapesi amene akuuluzidwa ndi mphepo yochokera mʼchipululu.+ 25  Zimenezi ndi zimene zidzakuchitikire. Limeneli ndi gawo limene ndakupatsa,” akutero Yehova,“Chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukukhulupirira zinthu zabodza.+ 26  Choncho ndidzakuvula siketi yako nʼkukuphimba nayo kumaso,Ndipo anthu adzaona maliseche ako.+ 27  Chigololo chimene ukuchita,+ kumemesa* kwako,Khalidwe lako lonyansa* la uhule, zonsezi zidzaonekera. Ndaona khalidwe lako lonyansa+Mʼmapiri komanso kuthengo. Tsoka kwa iwe Yerusalemu! Kodi ukhalabe wodetsedwa mpaka liti?”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mizinda yakumʼmwera yazunguliridwa ndi adani.”
Kapena kuti, “munthu wa ku Itiyopiya.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Kapena kuti, “lochititsa manyazi.”