Yeremiya 14:1-22

  • Chilala, njala ndi lupanga (1-12)

  • Aneneri abodza adzawonongedwa (13-18)

  • Yeremiya anavomereza kuti anthuwo anali ochimwa (19-22)

14  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala ndi awa:+   Yuda akulira maliro+ ndipo mageti ake agwa. Agwa pansi nʼkumalira momvetsa chisoni,Ndipo anthu a ku Yerusalemu akulira.   Anthu awo olemekezeka amatuma antchito awo kuti akatunge madzi. Antchitowo amapita kuzitsime koma sapezako madzi. Amabwerako ndi ziwiya zopanda kanthu. Iwo achita manyazi ndipo akhumudwa,Moti aphimba mitu yawo.   Alimi ataya mtima ndipo aphimba mitu yawoChifukwa chakuti mʼdzikomo simunagwe mvula+Ndipo nthaka yangʼambikangʼambika.   Ngakhale mbawala yaikazi yasiya mwana wake wobadwa kumene mʼthengoChifukwa kulibe msipu.   Abulu amʼtchire angoima mʼmapiri opanda kanthu. Akupuma mwawefuwefu ngati mimbulu.Maso awo achita mdima chifukwa kulibe msipu.+   Ngakhale kuti machimo athu akuchitira umboni kuti ndife olakwa,Inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.+ Chifukwa zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika nʼzambiri,+Ndipo takuchimwirani.   Inu chiyembekezo cha Isiraeli, Mpulumutsi wake+ pa nthawi yamavuto,Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdzikoli?Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wapaulendo amene waima kuti agone usiku umodzi wokha?   Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru,Ndiponso ngati munthu wamphamvu amene sangathe kupulumutsa anthu ake? Komatu inu Yehova muli pakati pathu,+Ndipo ife timadziwika ndi dzina lanu.+ Musatisiye. 10  Ponena za anthu awa Yehova wanena kuti: “Iwo amakonda kumangoyendayenda+ ndipo samatha kudziletsa kuti asamayendeyende.+ Choncho Yehova sakusangalala nawo.+ Tsopano iye akumbukira zolakwa zawo ndipo awalanga chifukwa cha machimo awo.”+ 11  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Usapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.+ 12  Akamasala kudya, ine sindimvetsera kuchonderera kwawo.+ Akamapereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zambewu, ine sindisangalala nazo+ ndipo ndiwawononga ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.”*+ 13  Nditamva zimenezi ndinanena kuti: “Mayo ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Simudzawonongedwa ndi lupanga ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni mʼmalo ano.’”+ 14  Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+ 15  Choncho Yehova wanena kuti: ‘Ponena za aneneri amene akulosera mʼdzina langa ngakhale kuti sindinawatume, amenenso akunena kuti lupanga kapena njala sizidzafika mʼdziko lino, ine ndikuti aneneri amenewo adzaphedwa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ 16  Anthu amene akuwauza maulosi awowo, adzafa ndi njala komanso lupanga ndipo mitembo yawo idzatayidwa mʼmisewu ya Yerusalemu. Sipadzakhala wowaika mʼmanda,+ iwowo, akazi awo, ana awo aamuna kapena ana awo aakazi chifukwa ndidzawatsanulira tsoka limene akuyenera kulandira.’+ 17  Anthu awa uwauze kuti,‘Maso anga atulutse misozi usiku ndi masana ndipo asasiye,+Chifukwa mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe ndi namwali, waphwanyidwa kotheratu+Ndipo ali ndi bala lalikulu kwambiri. 18  Ndikapita kunja kwa mzinda,Ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+ Ndipo ndikalowa mumzinda,+Ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala. Aneneri komanso ansembe, onse apita kudziko lachilendo limene sakulidziwa.’”+ 19  Kodi Yuda mwamukaniratu, kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+ Nʼchifukwa chiyani mwatilanga chonchi moti sitingathenso kuchira?+ Timayembekezera mtendere, koma palibe chabwino chilichonse chimene chachitika.Timayembekezera kuchiritsidwa, koma tikungoona zinthu zochititsa mantha.+ 20  Inu Yehova, ife tikuvomereza zinthu zoipa zimene tachitaKomanso kulakwa kwa makolo athu,Chifukwa takuchimwirani.+ 21  Koma chifukwa cha dzina lanu, musatikane.+Musachititse manyazi mpando wanu wachifumu waulemerero. Kumbukirani pangano limene munachita ndi ife ndipo musaliphwanye.+ 22  Kodi pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse limene lingagwetse mvula?Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi? Kodi si inu nokha, Yehova Mulungu wathu, amene mumachititsa zimenezi?+ Chiyembekezo chathu chili mwa inuChifukwa inu nokha ndi amene mumachita zonsezi.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “matenda.”