Yeremiya 15:1-21
15 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Ngakhale Mose ndi Samueli akanaima pamaso panga,+ anthu awa sindikanawakomera mtima. Achotse pamaso panga. Asiye apite.
2 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Tipite kuti?’ uwayankhe kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Amene akuyenera kufa ndi mliri afe ndi mliri!
Amene akuyenera kufa ndi lupanga afe ndi lupanga!+
Amene akuyenera kufa ndi njala yaikulu afe ndi njala yaikulu!
Amene akuyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!”’+
3 “‘Ndidzawabweretsera masoka okwanira 4,’*+ akutero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, mbalame zamumlengalenga komanso zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga.+
4 Ndidzawasandutsa chinthu chochititsa mantha kwa maufumu onse apadziko lapansi,+ chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+
5 Ndi ndani adzakusonyeze chifundo, iwe Yerusalemu?Ndi ndani adzakumvere chisoni,Ndipo ndi ndani adzapatuke kuti afunse za moyo wako?’
6 ‘Iwe wandisiya,’ akutero Yehova.+
‘Ukupitiriza kubwerera nʼkundisiya.*+
Choncho ndidzakutambasulira dzanja langa nʼkukuwononga.+
Ndatopa ndi kukumvera chisoni.*
7 Ndidzawapeta kuti auluzike ndi mphepo pamageti amʼdzikoli.
Ndidzawaphera ana awo.+
Ndidzawononga anthu anga,Chifukwa akukana kusiya kuyenda mʼnjira zawo.+
8 Akazi awo amasiye adzachuluka kwambiri pamaso panga kuposa mchenga wakunyanja.
Ndidzawabweretsera wowononga masana, adzawononga amayi ndi anyamata.
Ndidzawachititsa kuti asokonezeke komanso kugwidwa ndi mantha mwadzidzidzi.
9 Mkazi amene wabereka ana 7 wafooka,Ndipo akupuma movutikira.
Kwa iye dzuwa lalowa masanasana,Iye wachita manyazi ndipo wathedwa nzeru.’*
Ndipo anthu awo otsala omwe ndi ochepaNdidzawapereka kwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,’ akutero Yehova.”+
10 Tsoka ine, chifukwa inu mayi anga munabereka ine,+Munthu amene nthawi zonse ndimakangana ndi dziko lonse komanso kulimbana nalo.
Sindinakongole kanthu kapena kukongoza wina aliyense,Koma anthu onse akunditemberera.
11 Yehova anandiuza kuti: “Ndithu ndidzakuchitira zinthu zabwino.Ndithu ndidzakuthandiza pa nthawi ya tsoka,Ndidzakuthandiza pa nthawi yamavuto.
12 Kodi munthu angathe kuthyolathyola chitsulo?Kodi angathe kuthyolathyola chitsulo chakumpoto ndi kopa?*
13 Chuma chanu komanso zinthu zanu zamtengo wapatali ndidzazipereka kwa adani anu kuti azitenge.+Adzazitenga popanda malipiro chifukwa cha machimo anu onse amene munachita mʼdziko lanu lonse.
14 Ndidzazipereka kwa adani anuKuti azitenge nʼkupita nazo kudziko limene simukulidziwa.+
Chifukwa mkwiyo wanga wayatsa moto,Ndipo motowo ukukuyakirani.”+
15 Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga.Ndikumbukireni ndi kundiyangʼana.
Mundibwezerere anthu amene akundizunza.+
Musalole kuti ndiwonongeke chifukwa chakuti mukuwalezera mtima.
Dziwani kuti ndikunyozedwa chifukwa cha inu.+
16 Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya.+Mawu anu anakondweretsa komanso kusangalatsa mtima wanga,Chifukwa ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba.
17 Sindikhala pansi ndi gulu la anthu okonda zosangalatsa nʼkumasangalala nawo.+
Ndimakhala ndekha chifukwa dzanja lanu lili pa ine,Popeza mwandidzaza ndi mkwiyo.*+
18 Nʼchifukwa chiyani ululu wanga sukutha ndiponso bala langa silikupola?
Balali silikumva mankhwala.
Kodi mukhala ngati chitsime chosathandizaChimene munthu sangachidalire?
19 Choncho Yehova wanena kuti:
“Ukabwerera, ine ndidzakukonda,Ndipo udzapitiriza kunditumikira.*
Ukasiyanitsa zinthu zamtengo wapatali ndi zinthu zopanda phindu,Udzakhala ngati pakamwa panga.*
Anthuwo adzayenera kubwera kwa iwe,Koma iwe sudzapita kwa iwo.”
20 “Ndakuchititsa kuti ukhale ngati mpanda wakopa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+
Iwo adzamenyana nawe ndithu,Koma sadzakugonjetsa,+Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse komanso kukulanditsa,” akutero Yehova.
21 “Ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu oipaNdipo ndidzakuwombola mʼmanja mwa anthu ankhanza.”
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “ziweruzo zamitundu 4.” Mʼchilankhulo choyambirira, “mabanja 4.”
^ Mabaibulo ena amati, “Ukupitiriza kuyenda chafutambuyo.”
^ Kapena kuti, “Ndatopa ndi kusintha maganizo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Dzuwa lachita manyazi ndipo lathedwa nzeru.”
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Kapena kuti, “uthenga wachiweruzo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo udzaima pamaso panga.”
^ Kapena kuti, “Udzakhala wondilankhulira.”