Yeremiya 17:1-27
17 “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.
Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi mʼmitima yawoNdi panyanga za maguwa awo ansembe.
2 Pamene ana awo aamuna akumbukira maguwa awo ansembe ndi mizati yawo yopatulika*+Pafupi ndi mtengo wamasamba ambiri obiriwira, pamwamba pa zitunda zazitali,+
3 Pamapiri amene ali mʼmadera akumidzi.
Katundu wanu ndi chuma chanu chonse ndidzazipereka kwa adani anu kuti azitenge.+Ndidzapereka malo anu okwezeka chifukwa cha tchimo limene lachitika mʼmadera anu onse.+
4 Mwa kufuna kwanu, mudzataya cholowa chimene ndinakupatsani.+
Ndipo ndidzakuchititsani kuti mutumikire adani anu mʼdziko limene simukulidziwa.+Chifukwa mwayatsa mkwiyo wanga ngati moto.*+
Moto wake udzayakabe mpaka kalekale.”
5 Yehova wanena kuti:
“Wotembereredwa ndi munthu amene amakhulupirira munthu mnzake.+Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za munthu,+Komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.
6 Iye adzakhala ngati mtengo umene uli pawokhawokha mʼchipululu.
Zabwino zikadzafika sadzatha kuziona,Koma adzakhala mʼmalo ouma amʼchipululu,Mʼdziko la nthaka yamchere, kumene sikungakhale munthu aliyense.
7 Munthu amene amakhulupirira Yehova komanso amene amadalira Yehova,Ndi amene amadalitsidwa.+
8 Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi,Umene mizu yake imakafika mumtsinje.
Ngakhale dzuwa litawotcha kwambiri iye sadzamva kutentha,Koma nthawi zonse masamba ake adzakhala obiriwira.+
Ndipo pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa,Kapena kusiya kubala zipatso.
9 Mtima ndi wopusitsa* kwambiri kuposa chinthu chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+
Ndi ndani angaudziwe?
10 Ine Yehova ndimafufuza mtima,+Ndimafufuza maganizo a mkati mwa mtima wa munthu,*Kuti munthu aliyense ndimuchitire zinthu mogwirizana ndi zochita zake,Komanso mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+
11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo,*+Ali ngati nkhwali imene imasonkhanitsa mazira amene sinaikire.
Chuma chakecho chidzatha asanakwanitse hafu ya zaka za moyo wake,Ndipo pamapeto pake adzadziwika kuti ndi wopusa.”
12 Mpando waulemerero wa Mulungu ndi wokwezeka kuyambira pa chiyambi,Ndipo ndi malo athu opatulika.+
13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli,Onse amene akukusiyani adzachita manyazi.
Anthu onse okupandukirani mayina awo adzalembedwa pafumbi,+Chifukwa asiya Yehova, amene ndi kasupe wa madzi opatsa moyo.+
14 Ndichiritseni inu Yehova, ndipo ndidzachiradi.
Ndipulumutseni ndipo ndidzapulumukadi,+Chifukwa ine ndimatamanda inu.
15 Taonani! Ena akunena kuti:
“Nʼchifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe?+
Tsopanotu akwaniritsidwe.”
16 Koma ine sindinaleke kukutsatirani monga mʼbusa wanu,Kapena kulakalaka tsiku latsoka.
Inu Mulungu, mukudziwa bwino zimene pakamwa panga panalankhula,Chifukwa ndinalankhula pamaso panu.
17 Musakhale chinthu chochititsa mantha kwa ine.
Inu ndinu malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.
18 Anthu amene amandizunza achite manyazi,+Koma musalole kuti ineyo ndichite manyazi.
Anthuwo agwidwe ndi mantha aakulu,Koma musalole kuti ine ndigwidwe ndi mantha aakulu.
Agwetsereni tsoka,+Ndipo muwaphwanye komanso kuwawononga mpaka atheretu.*
19 Yehova wandiuza kuti: “Pita ukaime pageti la ana a anthu, pamene mafumu a Yuda amalowera ndi kutulukira komanso ukaime pamageti onse a mu Yerusalemu.+
20 Ndipo ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mafumu a Yuda ndi anthu nonse amene mukukhala mu Yuda komanso inu nonse amene mukukhala mu Yerusalemu, amene mumalowera pamageti awa.
21 Yehova wanena kuti: “Samalani kuti musanyamule katundu aliyense kapena kulowa naye pamageti a Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+
22 Musamatulutse katundu aliyense mʼnyumba zanu pa tsiku la Sabata ndipo musamagwire ntchito iliyonse.+ Muziona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika mogwirizana ndi zimene ndinalamula makolo anu.+
23 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu ndipo anaumitsa mtima wawo nʼkukana* kundimvera komanso kulandira malangizo.”’+
24 ‘“Koma mukandimvera mosamala,” akutero Yehova, “ndipo mukapanda kulowa ndi katundu pamageti a mzindawu pa tsiku la Sabata komanso mukamaona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika popewa kugwira ntchito iliyonse pa tsikuli,+
25 mafumu ndi akalonga amene amakhala pampando wachifumu wa Davide+ nawonso adzalowa pamageti a mzindawu. Adzalowa atakwera magaleta ndi mahatchi, mafumuwo ndi akalonga awo, anthu a mu Yuda komanso anthu amene akukhala mu Yerusalemu+ ndipo mumzindawu mudzakhala anthu mpaka kalekale.
26 Anthu adzabwera kuchokera mʼmizinda ya Yuda, mʼmadera ozungulira Yerusalemu, mʼdziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ mʼdera lamapiri komanso kuchokera ku Negebu.* Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani* ndi nsembe zoyamikira.+
27 Koma ngati simudzandimvera nʼkusiya kuona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika komanso mukadzanyamula katundu nʼkulowa naye pamageti a Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ine ndidzawotcha ndi moto mageti a mzindawu. Motowo udzawotcha nsanja zokhala ndi mipanda yolimba za Yerusalemu+ ndipo sudzazimitsidwa.”’”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “Chifukwa mwayatsidwa ndi mkwiyo wanga ngati moto.”
^ Kapena kuti, “wachinyengo.”
^ Mabaibulo ena amati, “ndipo ndi wosachiritsika.”
^ Kapena kuti, “Ndimafufuza mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso.”
^ Kapena kuti, “amapeza chuma koma osati mwachilungamo.”
^ Kapena kuti, “komanso muwawononge kuwirikiza kawiri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anaumitsa khosi lawo.”
^ Kapena kuti, “kuchokera kumʼmwera.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.