Yeremiya 2:1-37

  • Isiraeli anasiya Yehova nʼkuyamba kulambira milungu ina (1-37)

    • Isiraeli ali ngati mtengo wa mpesa wachilendo (21)

    • Zovala zake zathimbirira ndi magazi (34)

2  Yehova anandiuza kuti:  “Pita, ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukumbukira bwino mmene unkadziperekera* uli wachinyamata,+Chikondi chimene unkasonyeza pa nthawi imene ndinakulonjeza kuti ndidzakukwatira,+Mmene unanditsatirira mʼchipululu,Mʼdziko losadzalidwa kalikonse.+   Isiraeli anali wopatulika kwa Yehova,+ ndipo anali zipatso zoyambirira pa zokolola zake.”’ ‘Aliyense wofuna kumumeza akanakhala ndi mlandu. Tsoka likanamugwera,’ akutero Yehova.”+   Tamverani mawu a Yehova, inu a mʼnyumba ya YakoboKomanso inu nonse mafuko a mʼnyumba ya Isiraeli.   Yehova wanena kuti: “Kodi makolo anu anandipeza ndi vuto lotani+Kuti asochere nʼkupita kutali ndi ine,Nʼkuyamba kutsatira mafano opanda pake,+ iwonso nʼkukhala anthu opanda pake?+   Iwo sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova,Amene anatitulutsa mʼdziko la Iguputo,+Amene anatitsogolera mʼchipululu,Mʼdziko la zipululu+ ndi mayenje,Mʼdziko lachilala+ ndi lamdima wandiweyani,Mʼdziko limene simudutsa munthu aliyenseKomanso mmene simukhala anthu?’   Kenako ndinakulowetsani mʼdziko la minda ya zipatso,Kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino zamʼdzikolo.+ Koma inu munalowa mʼdziko langa nʼkuliipitsa.Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+   Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Amene ankaphunzitsa Chilamulo sankandidziwa,Abusa anandipandukira,+Aneneri ankalosera mʼdzina la Baala,+Ndipo ankatsatira milungu yopanda phindu.   ‘Choncho ndipitiriza kukuimbani mlandu,’+ akutero Yehova,‘Ndipo ndidzaimbanso mlandu ana a ana anu.’ 10  ‘Koma wolokerani kuzilumba za ku Kitimu+ kuti muone. Tumizani anthu ku Kedara+ ndipo muganizire bwinobwinoNʼkuona ngati zoterezi zinayamba zachitikapo kumeneko. 11  Kodi pali mtundu uliwonse wa anthu umene unasinthapo milungu yawo nʼkuyamba kulambira milungu imene kulibeko? Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zopanda phindu.+ 12  Yangʼanitsitsani zimenezi modabwa, inu kumwamba,Ndipo munjenjemere ndi mantha aakulu kwambiri,’ akutero Yehova, 13  ‘Chifukwa anthu anga achita zinthu ziwiri zoipa: Iwo andisiya ine kasupe wa madzi amoyo,+Ndipo akumba* zitsime zawo,Zitsime zongʼambika zimene sizingasunge madzi.’ 14  ‘Kodi Isiraeli ndi mtumiki wanga kapena ndi kapolo wobadwira mʼnyumba mwanga? Nanga nʼchifukwa chiyani anthu anamugwira nʼkupita naye kudziko lina? 15  Mikango yamphamvu* yamubangulira.+Yamutulutsira mawu amphamvu. Yachititsa kuti dziko lake likhale chinthu chochititsa mantha. Mizinda yake aiyatsa moto, moti simukukhalanso munthu aliyense. 16  Anthu a ku Nofi*+ ndi ku Tahapanesi+ anawononga dziko lako.* 17  Kodi mavuto amenewa sunadzibweretsere wekha,Posiya Yehova Mulungu wako+Pa nthawi imene ankakutsogolera panjira? 18  Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuna kuyenda mʼnjira ya ku Iguputo+Kuti ukamwe madzi amumtsinje wa Sihori?* Nʼchifukwa chiyani ukufuna kuyenda mʼnjira yopita kudziko la Asuri+Kuti ukamwe madzi amumtsinje wa Firate? 19  Uphunzirepo kanthu pa kuipa kwako,Ndipo kusakhulupirika kwako kukudzudzule. Udziwe ndi kuzindikira kuti kusiya Yehova Mulungu wako+Nʼchinthu choipa komanso chowawa.Iwe wasonyeza kuti sumandiopa,’+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa. 20  ‘Ine ndinaphwanya goli lako kalekale+Nʼkudula zingwe zimene anakumangira. Koma iwe unanena kuti: “Ine sindikutumikirani,” Ndipo unkagona chagada paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira+Nʼkumachita uhule pamenepo.+ 21  Ine ndinakudzala ngati mtengo wa mpesa wofiira,+ wabwino kwambiri umene unamera kuchokera ku mbewu yabwino kwambiri.Ndiye wandisinthira bwanji nʼkukhala mphukira zachabechabe za mtengo wa mpesa wachilendo?’+ 22  ‘Ngakhale utasambira soda ndiponso sopo wambiri,Zolakwa zako ndidzazionabe ngati zinthu zothimbirira,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 23  Unganene bwanji kuti, ‘Sindinadziipitse. Sindinatsatire mafano a Baalaʼ? Ganizira bwinobwino mmene ukuyendera mʼchigwa. Ganizira zimene wachita. Uli ngati ngamila yaingʼono yaikazi yothamanga kwambiri,Imene ikuthamanga kupita uku ndi uku popanda cholinga, 24  Uli ngati bulu wamʼtchire amene anazolowera kukhala mʼchipululu,Amene amanunkhiza pofunafuna amuna chifukwa cha chilakolako chake champhamvu. Ndi ndani amene angamubweze nthawi yoti akweredwe ikakwana? Abulu amphongo amene akumufunafuna sadzavutika kuti amupeze. Nyengo yoti* akweredwe ikakwana adzamupeza. 25  Samala kuti phazi lako lisakhale lopanda nsapatoKomanso kuti usachite ludzu. Koma iwe unanena kuti, ‘Zimenezo ayi!+ Ine ndili mʼchikondi ndi alendo*+Ndipo ndiwatsatira.’+ 26  Anthu a mʼnyumba ya Isiraeli achita manyazi,Ngati mmene wakuba amachitira akagwidwa,Iwowo, mafumu awo ndi akalonga awo,Ansembe awo ndiponso aneneri awo.+ 27  Iwo amauza mtengo kuti, ‘Ndinu bambo anga,’+ Ndipo mwala amauuza kuti, ‘Ndinu amene munandibereka.’ Koma ine andifulatira ndipo sanandisonyeze nkhope yawo.+ Koma tsoka likadzawagwera adzanena kuti,‘Bwerani mudzatipulumutse!’+ 28  Kodi milungu yako imene unapanga ija ili kuti?+ Imeneyo ibwere kwa iwe ngati ingathe kukupulumutsa pa nthawi ya tsoka,Chifukwa iwe Yuda, milungu yako yachuluka mofanana ndi mizinda yako.+ 29  ‘Kodi nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kundiimba mlandu? Nʼchifukwa chiyani nonsenu mwandipandukira?’+ akutero Yehova. 30  Ndalanga ana anu aamuna koma sizinathandize.+ Iwo sanalole kulandira chilango.*+Lupanga lanu linapha aneneri anu,+Ngati mkango wolusa. 31  Inu anthu anga, ganizirani mawu a Yehova. “Kodi ine ndakhala ngati chipululu kwa IsiraeliKapena ngati dziko lamdima wandiweyani? Nʼchifukwa chiyani anthu angawa anena kuti, ‘Tikungoyendayenda mmene tikufunira. Sitibweranso kwa inuʼ?+ 32  Kodi namwali angaiwale zinthu zake zodzikongoletsera?Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wapachifuwa?* Komatu anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+ 33  Mkazi iwe wachita zinthu mwaluso pofunafuna amuna oti akukonde. Wadziphunzitsa kuchita zinthu zoipa.+ 34  Ngakhale zovala zako zathimbirira ndi magazi a anthu osauka omwe ndi osalakwa,+Ngakhale kuti anthuwo sindinawapeze akuthyola nyumba kuti abe,Ndaona kuti magazi awo ali pazovala zako zonse.+ 35  Koma iwe ukunena kuti, ‘Ine ndilibe mlandu uliwonse. Ndithudi mkwiyo wake wandichokera.’ Tsopano ndikukupatsa chiweruzoChifukwa ukunena kuti, ‘Sindinachimwe.’ 36  Nʼchifukwa chiyani ukuona mopepuka kusakhulupirika kwako? Udzachitanso manyazi ndi Iguputo,+Ngati mmene unachitira manyazi ndi Asuri.+ 37  Pa chifukwa chimenechi, udzayenda manja ako ali kumutu,+Chifukwa Yehova wakana amene umawadaliraNdipo iwo sadzakuthandiza kuti zinthu zikuyendere bwino.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndikukumbukira bwino chikondi chokhulupirika chimene unkasonyeza.”
Kapena kuti, “agoba.” Nʼkutheka kuti achita zimenezi pamiyala.
Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Kapena kuti, “ku Memfisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakudya paliwombo.”
Umenewu ndi mtsinje umene unatuluka mumtsinje wa Nailo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwezi woti.”
Kapena kuti, “ndi milungu yachilendo.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Kapena kuti, “lamba wovala pa tsiku laukwati.”