Yeremiya 23:1-40

  • Abusa abwino komanso oipa (1-4)

  • Tidzakhala otetezeka mu ulamuliro wa “mfumu yolungama” (5-8)

  • Aneneri abodza anadzudzulidwa (9-32)

  • “Katundu wolemera” wa Yehova (33-40)

23  “Tsoka abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa zapamalo anga odyetsera ziweto!” akutero Yehova.+  Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Munapitiriza kuzimwaza ndipo simunazisamalire.”+ “Tsopano ndikulangani chifukwa cha zochita zanu zoipa,” akutero Yehova.  “Kenako ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera mʼmayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+  Ndidzapatsa nkhosazo abusa amene adzaziwete moyenerera.+ Sizidzaopanso kanthu kapena kuchita mantha ndipo palibe imene idzasowe,” akutero Yehova.  “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+  Mʼmasiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Isiraeli adzakhala motetezeka.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala: Yehova Ndi Chilungamo Chathu.”+  “Koma masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene sadzalumbiranso kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo.’+  Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a mʼnyumba ya Isiraeli nʼkuwabweretsa kuno kuchokera mʼdziko lakumpoto komanso kuchokera mʼmayiko onse kumene ndinawabalalitsiraʼ ndipo adzakhala mʼdziko lawo.”+  Ponena za aneneriwo ndikuti: Mtima wanga wasweka mkati mwanga. Mafupa anga onse akunjenjemera. Ndili ngati munthu woledzeraKomanso ngati munthu amene wagonjetsedwa ndi vinyo,Chifukwa cha Yehova komanso chifukwa cha mawu ake oyera. 10  Dzikoli ladzaza ndi anthu achigololo.+Chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+Ndipo malo amʼchipululu odyetserako ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. 11  “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa.*+ Ndipo ngakhale mʼnyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ akutero Yehova. 12  “Choncho njira zawo zidzakhala zoterera komanso zamdima.+Adzakankhidwa ndipo adzagwa. Chifukwa ndidzawagwetsera tsokaMʼchaka chimene ndidzawalange,” akutero Yehova. 13  “Ndaona zinthu zonyansa mwa aneneri a ku Samariya.+ Iwo akulosera mʼdzina la BaalaNdipo akusocheretsa anthu anga, Aisiraeli. 14  Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa. Iwo akuchita chigololo+ ndiponso akuchita zinthu mwachinyengo.+Akulimbikitsa* anthu ochita zoipaNdipo sakusiya zinthu zoipa zimene akuchita. Kwa ine, onsewo ali ngati Sodomu+Ndipo anthu okhala mumzindawu ali ngati Gomora.”+ 15  Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wadzudzula aneneriwo kuti: “Ndiwadyetsa chitsamba chowawaNdipo ndiwapatsa madzi apoizoni kuti amwe.+ Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko wafalikira mʼdziko lonse.” 16  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa inu.+ Iwo akungokupusitsani.* Iwo akulankhula masomphenya amumtima mwawo,+Osati ochokera mʼkamwa mwa Yehova.+ 17  Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti,‘Yehova wanena kuti: “Inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense amene amatsatira mtima wake woipawo akumuuza kuti,‘Tsoka silidzakugwerani.’+ 18  Ndi ndani amene waimirira pagulu la anthu amene Yehova amawakondaKuti azindikire ndi kumva mawu ake? Ndi ndani amene watchera khutu kuti amvetsere mawu ake? 19  Taonani! Mkwiyo wa Yehova udzawomba ngati mphepo yamkuntho.Udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu pamitu ya anthu oipa.+ 20  Mkwiyo wa Yehova sudzabwereraMpaka atachita ndi kukwaniritsa zofuna za mtima wake. Zinthu zimenezi mudzazimvetsa bwino mʼmasiku otsiriza. 21  “Ine sindinatumize aneneriwo, koma anathamanga. Ine sindinalankhule nawo, koma analosera.+ 22  Koma ngati akanaima pagulu la anthu amene ndimawakonda,Akanachititsa kuti anthu anga amve mawu angaNdipo akanawachititsa kuti abwerere nʼkusiya kuyenda mʼnjira zawo zoipa komanso kusiya zochita zawo zoipa.”+ 23  Yehova wanena kuti: “Kodi ine ndimakhala Mulungu pamene ndili pafupi basi, osati pamenenso ndili patali?” 24  “Kodi pali munthu amene angabisale pamalo obisika amene ine sindingamuone?”+ akutero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene sindingachione?”+ akutero Yehova. 25  “Ndamva aneneri amene akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa akunena kuti, ‘Ndalota maloto! Ndalota maloto!’+ 26  Kodi maganizo onena zabodza apitiriza kukhala mumtima mwa aneneriwa mpaka liti? Iwo ndi aneneri amene amanena chinyengo chochokera mumtima mwawo.+ 27  Iwo akufuna kuchititsa kuti anthu anga aiwale dzina langa pogwiritsa ntchito maloto amene aneneriwo amauzana, mofanana ndi mmene makolo awo anaiwalira dzina langa chifukwa cha Baala.+ 28  Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, azinena zoona polankhula mawu angawo.” “Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?” akutero Yehova. 29  Yehova wanena kuti: “Kodi mawu anga safanana ndi moto?+ Kodi safanana ndi hamala imene imaphwanya thanthwe?”+ 30  “Choncho ine ndidzalanga aneneriwo chifukwa aliyense wa iwo akuba mawu anga kwa mnzake,” akutero Yehova.+ 31  Yehova wanena kuti: “Ine ndidzalanga aneneri amene akugwiritsa ntchito lilime lawo nʼkumanena kuti, ‘Awa ndi mawu ochokera kwa Mulungu!’”+ 32  “Ine ndidzalanga aneneri amene akulota maloto abodza, amene akunena malotowo nʼkusocheretsa anthu anga chifukwa cha mabodza awo komanso kudzitama kwawo,” akutero Yehova.+ “Koma ine sindinawatume kapena kuwalamula kuti achite zimenezo. Choncho zochita zawo sizidzapindulitsa anthu awa ngakhale pangʼono,”+ akutero Yehova. 33  “Ndipo anthu awa komanso mneneri kapena wansembe akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga* wa Yehova ukuti chiyani?’ uwayankhe kuti, ‘“Anthu inu ndinu katundu wolemera! Ndipo ndidzakutayani,”+ akutero Yehova.’ 34  Mneneri, wansembe kapena aliyense amene akunena kuti, ‘Uthenga uwu ndi katundu wolemera wa Yehova!’ ndidzalanga munthuyo ndi anthu a mʼnyumba yake. 35  Aliyense wa inu akufunsa mnzake ndi mʼbale wake kuti, ‘Kodi Yehova wayankha kuti chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?’ 36  Koma musanenenso kuti uthenga wa Yehova ndi katundu wolemera, chifukwa katundu wolemera ndi mawu a aliyense wa inu ndipo mwasintha mawu a Mulungu wathu wamoyo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 37  Mneneri umufunse kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani? 38  Mukapitiriza kunena kuti, “Uthenga uwu ndi katundu wolemera wa Yehova!” Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti mukunenabe kuti, ‘Mawu a Yehova ndi katundu wolemera,’ ngakhale kuti ndinakuuzani kuti ‘Musamanene kuti: “Mawu a Yehova ndi katundu wolemera!”’ 39  tamverani, ine ndikunyamulani nʼkukutayani kutali ndi ine. Ndidzachita zimenezi kwa inuyo ndi mzinda umene ndinapatsa inu ndi makolo anu. 40  Ndidzachititsa kuti mukhale ndi manyazi mpaka kalekale ndipo mudzanyozeka mpaka kalekale. Zimenezi sizidzaiwalika.”’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene ndidzachititsa kuti mʼbanja la Davide mutuluke mbadwa yolungama.”
Kapena kuti, “onse ndi ampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amalimbitsa manja a.”
Kapena kuti, “Iwo akukuchititsani kuti muziyembekezera zinthu zabodza.”
Kapena kuti, “uthenga wolemera.” Mawu ake a Chiheberi ali ndi matanthauzo awiri awa: “Uthenga wolemera wochokera kwa Mulungu” kapena “chinthu cholemera.”