Yeremiya 24:1-10

  • Nkhuyu zabwino komanso zoipa (1-10)

24  Kenako Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandionetsa madenguwo pambuyo poti Nebukadinezara* mfumu ya Babulo watenga Yekoniya*+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri komanso anthu osula zitsulo,* kuchoka ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+  Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwino kwambiri ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Koma dengu lina linali ndi nkhuyu zoipa kwambiri. Zinali zoipa kwambiri moti munthu sakanatha kuzidya.  Kenako Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Yeremiya?” Ndipo ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nkhuyu. Nkhuyu zabwino, nʼzabwino kwambiri koma nkhuyu zoipa, nʼzoipa kwambiri. Ndi zoipa kwambiri moti munthu sangadye.”+  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amene anatengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo, amene ndinawachotsa mʼdziko lino nʼkuwatumiza kudziko la Akasidi ali ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawaona kuti ndi anthu abwino.  Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzachititsa kuti abwerere mʼdziko lino.+ Ndidzachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo sindidzawawononga. Ndidzawadzala ndipo sindidzawazula.+  Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo+ chifukwa adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+  Koma mofanana ndi nkhuyu zoipa zija, zimene ndi zoipa kwambiri moti munthu sangathe kudya,+ Yehova wanena kuti: “Ndi mmenenso ndidzaonere Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake, anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira mʼdzikoli komanso anthu okhala mʼdziko la Iguputo.+  Ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yonse padziko lapansi achite mantha akadzaona tsoka limene ndidzawabweretsere.+ Anthu adzawanyoza, adzawaona kuti ndi chitsanzo cha anthu amene akumana ndi tsoka, adzawaseka komanso kuwatemberera+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsire.+ 10  Ndidzawatumizira lupanga,+ njala ndi mliri,*+ mpaka adzatheratu mʼdziko limene ndinapereka kwa iwowo ndi makolo awo.”’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Amadziwikanso ndi dzina lakuti Yehoyakini ndi Koniya.
Mabaibulo ena amati, “anthu omanga makoma achitetezo.”
Kapena kuti, “matenda.”