Yeremiya 26:1-24

  • Yeremiya anaopsezedwa kuti aphedwa (1-15)

  • Yeremiya anapulumutsidwa (16-19)

    • Ananena zimene Mika ananena mu ulosi wake (18)

  • Mneneri Uliya (20-24)

26  Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya mawu akuti:  “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire mʼbwalo la nyumba ya Yehova ndipo ukanene zimene zidzachitikire anthu onse amʼmizinda ya Yuda amene akubwera kudzalambira* panyumba ya Yehova. Ukawauze zonse zimene ndakulamula ndipo usachotsepo mawu ngakhale amodzi.  Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa. Ndipo ndidzasintha maganizo anga okhudza tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.+  Ukawauze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ngati simundimvera potsatira chilamulo changa chimene* ndakupatsani,  komanso kumvera mawu a atumiki anga omwe ndi aneneri, amene ndikuwatumiza kwa inu mobwerezabwereza,* omwe inu simunawamvere,+  ine ndidzachititsa kuti nyumba iyi ikhale ngati Silo.+ Ndidzawononga mzindawu ndipo mitundu yonse yapadziko lapansi idzaugwiritsa ntchito ngati chitsanzo potemberera.’”’”+  Choncho ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akulankhula mawu amenewa mʼnyumba ya Yehova.+  Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira nʼkunena kuti: “Ukuyenera kufa basi.  Nʼchifukwa chiyani wanenera mʼdzina la Yehova kuti, ‘Nyumba iyi idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uwu udzawonongedwa moti simudzapezeka aliyense wokhalamoʼ?” Ndiyeno anthu onse anabwera mʼnyumba ya Yehova nʼkuzungulira Yeremiya. 10  Akalonga a Yuda atamva mawu amenewa, anachoka kunyumba ya mfumu nʼkupita kunyumba ya Yehova ndipo anakakhala pakhomo lapageti latsopano la nyumba ya Yehova.+ 11  Ansembe ndi aneneri anauza akalongawo ndi anthu onse kuti: “Munthuyu akuyenera kuphedwa+ chifukwa wanenera zoti mzindawu udzakumana ndi tsoka monga mmene mwamvera ndi makutu anu.”+ 12  Kenako Yeremiya anauza akalonga onse ndi anthu onsewo kuti: “Yehova ndi amene anandituma kuti ndidzanene mawu onse amene mwamva okhudza nyumbayi ndi mzindawu.+ 13  Choncho panopa sinthani njira zanu komanso zochita zanu ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake okhudza tsoka limene wanena kuti akugwetserani.+ 14  Koma ineyo, ndili mʼmanja mwanu. Ndichiteni zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino ndi zoyenera. 15  Koma mudziwe kuti mukandipha, inuyo, mzindawu ndi anthu onse amene akukhala mumzindawu mukhala ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Ndithudi, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onse amene mwamvawa.” 16  Kenako akalonga ndi anthu onse anauza ansembe ndi aneneri kuti: “Munthu uyu sakuyenera kuphedwa chifukwa walankhula nafe mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.” 17  Kuwonjezera pamenepo, akuluakulu ena amʼdzikolo anaimirira nʼkuyamba kuuza anthu onse amene anasonkhana kuti: 18  “Mika+ wa ku Moreseti nayenso ankanenera mʼmasiku a Mfumu Hezekiya+ ya ku Yuda. Iye ankauza anthu onse a ku Yuda kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ziyoni adzalimidwa ngati munda,Yerusalemu adzakhala mabwinja,+Ndipo phiri la nyumba ya Mulungu* lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.”’+ 19  Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova komanso kupempha Yehova kuti amukomere mtima?* Atatero, kodi Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawabweretsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu. 20  Panalinso munthu wina amene ankanenera mʼdzina la Yehova. Iyeyu anali Uliya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-yearimu.+ Iye ananeneratu zimene zidzachitikire mzindawu mofanana ndi mawu a Yeremiya. 21  Ndiyeno Mfumu Yehoyakimu,+ asilikali ake onse amphamvu ndi akalonga onse anamva mawu amene Uliya ananena. Zitatero mfumu inakonza zoti imuphe.+ Uliya atamva zimenezo, nthawi yomweyo anachita mantha ndipo anathawira ku Iguputo. 22  Kenako Mfumu Yehoyakimu inatumiza Elinatani,+ mwana wa Akibori ndi amuna ena ku Iguputo. 23  Iwo anagwira Uliya nʼkubwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inapha Uliya ndi lupanga+ nʼkutaya mtembo wake mʼmanda a anthu wamba.” 24  Koma Ahikamu,+ mwana wa Safani+ anateteza Yeremiya, nʼchifukwa chake sanaperekedwe kwa anthu kuti amuphe.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kudzagwada.”
Kapena kuti, “potsatira malangizo anga amene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndikudzuka mʼmawa nʼkuwatumiza.”
Kapena kuti, “Ndipo phiri pamene pali kachisi.”
Kapena kuti, “komanso kuyesa kufewetsa nkhope ya Yehova.”