Yeremiya 27:1-22

  • Goli la Babulo (1-11)

  • Zedekiya anauzidwa kuti azimvera mfumu ya Babulo (12-22)

27  Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti akanene mawu akuti:  “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira komanso magoli ndipo uzivale mʼkhosi mwako.  Kenako uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya Aamoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene abwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda.  Ukatero, uwalamule kuti akauze ambuye awo kuti: “Mukauze ambuye anu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti,  ‘Ine ndi amene ndinapanga dziko lapansi, anthu ndi nyama zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu ndiponso dzanja langa lotambasula. Ndipo dziko lapansili ndalipereka kwa amene ndikufuna.*+  Tsopano ndapereka mayiko onsewa mʼmanja mwa mtumiki wanga, Mfumu Nebukadinezara+ ya ku Babulo. Ndamupatsanso ngakhale nyama zakutchire kuti zimutumikire.  Mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo, mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pa nthawi imeneyo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamupangitsa kuti akhale kapolo wawo.’+  ‘Ngati mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu udzakane kutumikira Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo komanso kukana kuika khosi lake mʼgoli la mfumu ya Babulo, ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga,+ njala komanso mliri* mpaka nditauwononga wonse pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadinezara,’ akutero Yehova.  ‘Choncho musamvere aneneri, anthu ochita zamaula, olota maloto, ochita zamatsenga ndi obwebweta amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Simudzatumikira mfumu ya Babulo.” 10  Chifukwa anthu amenewa akulosera zabodza kwa inu, mukawamvera mudzatengedwa mʼdziko lanu nʼkupita dziko lakutali ndipo ine ndidzakubalalitsani moti mudzawonongedwa. 11  Koma mtundu wa anthu umene udzaike khosi lake mʼgoli la mfumu ya Babulo nʼkuitumikira, ndidzaulola kuti ukhalebe* mʼdziko lawo ndipo udzalima minda nʼkumakhala mʼdzikolo,’ akutero Yehova.”’” 12  Mfumu Zedekiya+ ya ku Yuda ndinaiuzanso mawu amenewa kuti: “Ikani makosi anu mʼgoli la mfumu ya Babulo nʼkuitumikira. Mutumikire mfumuyo ndi anthu ake kuti mukhalebe ndi moyo.+ 13  Kodi iweyo ndi anthu ako muferenji ndi lupanga,+ njala+ ndi mliri+ ngati mmene Yehova wanenera kuti ndi zimene zidzachitikire mtundu umene sudzatumikira mfumu ya Babulo? 14  Musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zabodza.+ 15  ‘Ine sindinawatume,’ akutero Yehova, ‘koma iwo akulosera zabodza mʼdzina langa. Mukawamvera ndidzakubalalitsani ndipo ndidzawononga inuyo limodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inu.’”+ 16  Ndiyeno ndinauza ansembe ndi anthu onsewo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya zamʼnyumba ya Yehova zibwezedwa posachedwapa kuchokera ku Babulo!”+ chifukwa iwo akulosera zabodza kwa inu.+ 17  Musawamvere. Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+ Kodi mzindawu ukhale bwinja chifukwa chiyani? 18  Koma ngati iwo ndi aneneri ndipo akulankhula mawu a Yehova, iwo apemphe kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba kuti ziwiya zimene zinatsala mʼnyumba ya Yehova, mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babulo.’ 19  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zokhudza zipilala,+ thanki ya madzi,*+ zotengera zamawilo+ ndi ziwiya zimene zatsala mumzindawu, 20  zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo sanatenge pamene ankatenga Yekoniya mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+ 21  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena zokhudza ziwiya zimene zinatsala mʼnyumba ya Yehova, mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu kuti: 22  ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo+ ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukire,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzazitenga nʼkuzibwezeretsa pamalo ano.”’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndikuona kuti ndi woyenerera.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “upumule.”
Imeneyi ndi thanki yakopa yapakachisi.