Yeremiya 28:1-17

  • Yeremiya anatsutsana ndi mneneri wabodza Hananiya (1-17)

28  Ndiyeno mʼchaka chomwecho, chaka cha 4, mʼmwezi wa 5, kumayambiriro kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, wa ku Gibiyoni,+ anauza Yeremiya mʼnyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti:  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+  Zaka ziwiri zisanathe, ndibwezeretsa pamalo ano ziwiya zonse zamʼnyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anatenga kuno nʼkupita nazo ku Babulo.’”+  “‘Ndipo Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, ndiponso anthu onse a mu Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo+ ndiwabwezeretsa kuno, chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya Babulo,’ akutero Yehova.”  Kenako mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anaimirira mʼnyumba ya Yehova.  Mneneri Yeremiya anayankha kuti: “Zikhale momwemo!* Yehova achitedi zimenezo! Yehova akwaniritse mawu ako amene walosera. Achite zimenezo pobwezeretsa pamalo ano ziwiya zamʼnyumba ya Yehova ndi anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo!  Komabe, tamvera uthenga uwu umene ndikufuna kukuuza pamaso pa anthu onse.  Aneneri akalekale amene analipo ineyo ndisanakhalepo komanso iweyo usanakhalepo ankalosera za nkhondo, masoka ndi miliri yoti igwere* mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu.  Ngati mneneri walosera zokhudza mtendere zinthuzo nʼkuchitikadi, mʼpamene zimadziwika kuti Yehova anamutumadi mneneriyo.” 10  Hananiya atamva zimenezo anatenga goli limene linali mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nʼkulithyola.+ 11  Kenako Hananiya anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndathyolera goli ili, zaka ziwiri zisanathe,+ ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu.’” Zitatero, mneneri Yeremiya anachokapo. 12  Mneneri Hananiya atathyola goli limene linali mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anauza Yeremiya kuti: 13  “Pita ukauze Hananiya kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wathyola magoli amtengo+ koma mʼmalomwake padzakhala magoli achitsulo.” 14  Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndidzaika magoli achitsulo pamakosi a mitundu ya anthu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndipo akuyenera kudzamutumikira.+ Nebukadinezara ndidzamupatsanso ngakhale nyama zakutchire.”’”+ 15  Kenako mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zabodza.+ 16  Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndikukuchotsera moyo wako. Chaka chomwe chino iweyo ufa, chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova.’”+ 17  Choncho mneneri Hananiya anamwalira chaka chomwecho, mʼmwezi wa 7.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame!”
Kapena kuti, “matenda oti agwere.”