Yeremiya 3:1-25

  • Isiraeli anapanduka kwambiri (1-5)

  • Isiraeli ndi Yuda anachita tchimo la chigololo (6-11)

  • Anawalimbikitsa kuti alape (12-25)

3  Anthu amafunsa kuti: “Ngati mwamuna wathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo akachokadi nʼkukakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamunayo angabwererenso kwa mkaziyo?” Kodi dzikoli silaipitsidwa kale kwambiri?+ Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+Ndiye kodi pano ukufuna ubwererenso kwa ine?   Yangʼana pamwamba pa mapiri ndipo uone. Kodi ndi pamalo ati pamene amuna sanakugonerepo? Unkakhala mʼmbali mwa njira nʼkumawadikiriraNgati munthu wongoyendayenda* mʼchipululu. Ukupitiriza kuipitsa dzikoliNdi uhule wako komanso kuipa kwako.+   Choncho mvula yamvumbi yaletsedwa kuti isagwe,+Ndipo mvula yomalizira siinagwe. Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+   Koma tsopano ukundiitana kuti:‘Bambo anga, inu ndinu mnzanga wapamtima kuyambira pa unyamata wanga.+   Kodi mukhala wokwiya mpaka kalekale,Kapena kusunga chakukhosi nthawi zonse?’ Izi ndi zimene mwanena,Koma mukupitiriza kuchita zoipa zilizonse mmene mungathere.”+  Mʼmasiku a Mfumu Yosiya,+ Yehova anandiuza kuti: “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita? Akupita kuphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira kuti akachite uhule kumeneko.+  Ngakhale kuti anachita zonsezi, ine ndinamupempha mobwerezabwereza kuti abwerere kwa ine,+ koma iye sanabwerere. Ndipo Yuda ankangoyangʼana zimene mchemwali wake wachinyengoyo ankachita.+  Nditaona zimenezo, ndinathamangitsa Isiraeli wosakhulupirikayo ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa anachita chigololo.+ Koma Yuda mchemwali wake, amene ndi wachinyengo, sanachite mantha. Nayenso anayamba kuchita uhule.+  Iye ankaona kuti kuchita uhulewo si vuto moti anapitiriza kuipitsa dzikolo ndipo ankachita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+ 10  Ngakhale kuti anachita zonsezi, mchemwali wake Yuda amene ndi wachinyengo sanabwerere kwa ine ndi mtima wake wonse, koma anangobwerera mwachiphamaso,’ akutero Yehova.” 11  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Isiraeli amene ndi wosakhulupirika wasonyeza kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Yuda amene ndi wachinyengo.+ 12  Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto:+ ‘Yehova wanena kuti:+ “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya+ chifukwa ndine wokhulupirika,” akutero Yehova. “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. 13  Koma vomerezani kuti ndinu olakwa chifukwa mwapandukira Yehova Mulungu wanu. Munapitiriza kuchita chiwerewere ndi anthu achilendo* pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira. Koma simunamvere mawu anga,” akutero Yehova.’” 14  “Bwererani inu ana opanduka,” akutero Yehova. “Ine ndakhala mbuye wanu* weniweni. Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mʼbanja lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+ 15  Ndidzakupatsani abusa amene amachita zinthu zogwirizana ndi zofuna zanga+ ndipo adzakuthandizani kuti mudziwe zinthu zambiri ndiponso kuti mukhale omvetsa zinthu. 16  Masiku amenewo Mudzaberekana ndipo mudzakhala ambiri mʼdzikoli,” akutero Yehova.+ “Iwo sadzanenanso kuti, ‘Likasa la pangano la Yehova!’ Sadzaliganiziranso mʼmitima yawo, kulikumbukira kapena kulilakalaka ndipo sadzapanganso likasa lina. 17  Pa nthawi imeneyo mzinda wa Yerusalemu adzautchula kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsa pamodzi ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso khosi nʼkumatsatira mitima yawo yoipayo. 18  Mʼmasiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli.+ Onse pamodzi adzabwera kuchokera mʼdziko lakumpoto nʼkulowa mʼdziko limene ndinapereka kwa makolo anu kuti likhale cholowa chawo.+ 19  Ine ndinkaganiza kuti, ‘Mosangalala ndinakuika pakati pa ana aamuna nʼkukupatsa dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri pakati pa mitundu ya anthu!’*+ Ndinkaganizanso kuti uzindiitana kuti, ‘Bambo anga!’ ndiponso kuti sudzasiya kunditsatira. 20  ‘Ndithudi, mofanana ndi mkazi amene amasiya mwamuna wake mwachinyengo, inunso a mʼnyumba ya Isiraeli mwandichitira zachinyengo,’+ akutero Yehova.” 21  Pamwamba pa mapiri pamveka phokoso,La kulira ndi kuchonderera kwa Aisiraeli,Chifukwa akhotetsa njira zawoNdipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+ 22  “Bwererani, inu ana opanduka. Ndidzachiritsa mtima wanu wopandukawo.”+ “Ife tabwerera! Tabwera kwa inu,Chifukwa inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ 23  Ndithudi, tinkangodzinamiza tokha pochitira milungu ina zikondwerero zaphokoso mʼzitunda ndi mʼmapiri.+ Kunena zoona chipulumutso cha Isiraeli chimachokera kwa Yehova Mulungu wathu.+ 24  Koma chinthu chochititsa manyazi chadya* zinthu zonse zimene makolo athu anazipeza movutikira kuyambira tili anyamata.+Chadya nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo,Ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. 25  Tiyeni tigone pansi mwamanyazi,Ndipo manyazi athuwo atiphimbe,Chifukwa tachimwira Yehova Mulungu wathu,+Ifeyo pamodzi ndi makolo athu kuyambira tili achinyamata mpaka pano,+Ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mluya.”
Kapena kuti, “ndi milungu yachilendo.”
Mabaibulo ena amati, “mwamuna wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa asilikali a mitundu ya anthu.”
Kapena kuti, “Koma mulungu wochititsa manyazi wadya.”