Yeremiya 33:1-26

  • Analonjezedwa kuti adzabwerera mwakale (1-13)

  • Tidzakhala otetezeka mu ulamuliro wa “mfumu yolungama” (14-16)

  • Pangano limene anachita ndi Davide komanso ansembe (17-26)

    • Pangano lokhudza masana ndi usiku (20)

33  Yeremiya adakali mʼBwalo la Alonda+ momwe anamutsekera, Yehova analankhula naye kachiwiri kuti:  “Yehova amene anapanga dziko lapansi, Yehova amene anawumba dzikoli nʼkulikhazikitsa mwamphamvu, Mulungu amene dzina lake ndi Yehova, wanena kuti,  ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani. Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba zamumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda, zimene zagwetsedwa chifukwa cha malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso lupanga la adani.+  Wanenanso mawu okhudza anthu amene akubwera kudzamenyana ndi Akasidi komanso zokhudza malo amene adzaza ndi mitembo ya anthu amene ndawapha chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu, omwe kuipa kwawo kwachititsa kuti mzindawu ndiubisire nkhope yanga. Iye wanena kuti:  ‘Ine ndichiritsa anthu amumzindawu nʼkuwapatsa thanzi labwino.+ Ndiwachiritsa nʼkuwapatsa mtendere wambiri ndi choonadi chochuluka.+  Anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anatengedwa kupita kudziko lina ndidzawabwezeretsa+ ndipo adzakhalanso ngati mmene analili poyamba.+  Ndidzawayeretsa ku zolakwa zonse zimene anandichimwira+ ndipo ndidzawakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nʼkuphwanya nazo malamulo anga.+  Mzindawu udzakhala ndi dzina limene lidzandisangalatse, udzachititsa kuti nditamandidwe ndiponso kulandira ulemerero pakati pa mitundu yonse yapadziko lapansi, imene idzamve za zinthu zabwino zimene ndinachitira anthu anga.+ Anthu a mitundu inawo adzachita mantha ndipo adzanjenjemera+ chifukwa cha zinthu zonse zabwino komanso mtendere umene ndidzabweretse pa mzindawu.’”+ 10  “Yehova wanena kuti: ‘Pamalo ano amene mudzanene kuti ndi bwinja, opanda anthu kapena ziweto, mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu imene yawonongeka, moti mulibe anthu ndipo simukukhala aliyense ngakhale ziweto, mʼmalo amenewa mudzamveka 11  phokoso la chikondwerero ndi chisangalalo.+ Mudzamvekanso mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi komanso mawu a anthu amene akunena kuti: “Yamikani Yehova wa magulu ankhondo akumwamba chifukwa Yehova ndi wabwino+ ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale!”’+ ‘Anthuwo adzabweretsa nsembe zoyamikira kunyumba ya Yehova,+ chifukwa ndidzabwezeretsa anthu amʼdzikoli, amene anatengedwa kupita kudziko lina, kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’ akutero Yehova.” 12  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Mʼdziko labwinja lino, lopanda anthu kapena ziweto komanso mʼmizinda yake yonse, mudzakhalanso malo odyetserako ziweto kumene abusa azidzapumitsirako ziweto zawo.’+ 13  ‘Mʼmizinda yamʼmadera amapiri, mʼmizinda yamʼchigwa, mʼmizinda yakumʼmwera, mʼdziko la Benjamini, mʼmadera ozungulira Yerusalemu+ ndi mʼmizinda ya Yuda,+ ziweto zidzadutsanso pansi pa dzanja la munthu amene akuziwerenga,’ akutero Yehova.” 14  “‘Taonani! Masiku akubwera pamene ndidzakwaniritsa lonjezo langa labwino lokhudza nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda,’ akutero Yehova.+ 15  ‘Mʼmasiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira+ yolungama* ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo mʼdzikoli.+ 16  Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu azidzatchulidwa kuti, Yehova Ndi Chilungamo Chathu.’”+ 17  “Yehova wanena kuti, ‘Mʼnyumba ya Davide simudzalephera kupezeka munthu woti akhale pampando wachifumu wa nyumba ya Isiraeli.+ 18  Ndipo pakati pa Alevi omwe ndi ansembe sipadzalephera kupezeka mwamuna wonditumikira woti azipereka nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zambewu komanso nsembe zina.’” 19  Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 20  “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale masana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti masana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+ 21  ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wake wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi pangano langa ndi atumiki anga Alevi omwe ndi ansembe.+ 22  Ine ndidzachulukitsa mbadwa* za Davide mtumiki wanga ndi Alevi amene akunditumikira. Ndidzazichulukitsa mofanana ndi kuchuluka kwa nyenyezi zonse zakumwamba* zimene sizingawerengedwe ndiponso mofanana ndi mchenga umene sungayezedwe.’” 23  Kenako Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 24  “Kodi sunamve zimene anthu awa akunena kuti, ‘Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, adzawakanansoʼ? Adani akuchitira anthu anga zinthu zopanda ulemu ndipo sakuwaonanso ngati mtundu wa anthu. 25  Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale masana ndi usiku,+ malamulo akumwamba ndi dziko lapansi,+ 26  sindidzakananso mbadwa* za Yakobo ndi za Davide mtumiki wanga, kuti pakati pa mbadwa* zake ndisatengepo olamulira ana a Abulahamu,* Isaki ndi Yakobo. Chifukwa ndidzasonkhanitsa anthu onse amene anatengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wolowa mʼmalo wolungama.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchuluka kwa magulu ankhondo akumwamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya Abulahamu.”