Yeremiya 36:1-32

  • Yeremiya ankanena mawu oti alembedwe mumpukutu (1-7)

  • Baruki anawerenga mpukutu mokweza (8-19)

  • Yehoyakimu anawotcha mpukutu (20-26)

  • Uthengawo unalembedwanso mumpukutu watsopano (27-32)

36  Ndiyeno mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti:  “Tenga mpukutu ndipo ulembemo mawu onse amene ndakuuza okhudza chilango chimene ndidzapereke kwa Isiraeli, Yuda+ ndi mitundu yonse ya anthu.+ Ulembe mawu onse amene ndakuuza kuchokera nthawi imene ndinalankhula nawe mʼmasiku a Yosiya mpaka lero.+  Mwina anthu a mʼnyumba ya Yuda akamva za masoka onse amene ndikufuna kuwagwetsera, adzabwerera nʼkusiya njira zawo zoipa. Akatero, ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndi machimo awo.”+  Ndiyeno Yeremiya anaitana Baruki+ mwana wa Neriya nʼkumuuza mawu onse amene Yehova anamuuza ndipo Baruki analemba mawuwo mumpukutu.+  Kenako Yeremiya anauza Baruki kuti: “Ine anditsekera ndipo sindingathe kukalowa mʼnyumba ya Yehova.  Choncho iweyo ndi amene ukuyenera kupita kukawerenga mokweza mawu a Yehova amene ali mumpukutu umene ndakuuza kuti ulembe. Ukawerenge mokweza pamaso pa anthu onse mʼnyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya. Ukakatero ukakhala kuti wawerengera anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera mʼmizinda yawo.  Mwina Yehova adzamva pempho lawo lakuti awakomere mtima ndipo aliyense adzabwerera nʼkusiya njira yake yoipa, popeza Yehova wanena kuti adzasonyeza anthu awa mkwiyo wake ndi ukali wake waukulu.”  Choncho Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamulamula, kuti apite kunyumba ya Yehova kukawerenga mokweza mawu a Yehova amene analembedwa mumpukutumo.+  Ndiyeno mʼchaka cha 5 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mʼmwezi wa 9, anthu onse a mu Yerusalemu ndi anthu onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera mʼmizinda ya Yuda analengeza kuti asala kudya pamaso pa Yehova.+ 10  Kenako Baruki anawerenga mokweza mpukutu womwe unali ndi mawu a Yeremiya mʼnyumba ya Yehova. Anachita zimenezi mʼchipinda cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba,* mʼbwalo limene linali mʼmwamba, pakhomo la geti latsopano la nyumba ya Yehova,+ anthu onse akumva. 11  Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova amene anali mumpukutumo, 12  anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda cha mlembi. Akalonga onse anali atakhala* pansi kumeneko ndipo kunali Elisama+ mlembi, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse. 13  Mikaya anawauza mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga mpukutuwo mokweza anthu onse akumva. 14  Zitatero, akalonga onse anatumiza Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusa, kukaitana Baruki kuti: “Bwera kuno ndipo utenge mpukutu umene unawerenga mokweza pamaso pa anthu onse.” Choncho Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo nʼkupita nawo kwa iwo. 15  Akalongawo anamuuza kuti: “Khala pansi ndipo utiwerengere mokweza.” Choncho Baruki anawawerengera mpukutuwo. 16  Ndiyeno atamva mawu onsewa anayangʼanana mwamantha, ndipo anauza Baruki kuti: “Ndithu, tikuyenera kukauza mfumu mawu amenewa.” 17  Kenako anafunsa Baruki kuti: “Tiuze, zatheka bwanji kuti ulembe mawu onsewa. Kodi amachita kukuuza?” 18  Baruki anawayankha kuti: “Yeremiya amandiuza mawu onsewa, ine nʼkumalemba mumpukutuwu ndi inki.” 19  Akalongawo anauza Baruki kuti: “Iweyo ndi Yeremiya pitani mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene muli.”+ 20  Kenako akalongawo anapita kwa mfumu mʼbwalo la mkati nʼkusiya mpukutuwo mʼchipinda cha Elisama mlembi ndipo anauza mfumu zonse zimene anamva. 21  Mfumu itamva zimenezi inatuma Yehudi+ kuti akatenge mpukutuwo ndipo iye anakautenga mʼchipinda cha Elisama mlembi. Yehudi anayamba kuwerenga mokweza mpukutuwo pamaso pa mfumu ndi akalonga onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo. 22  Pa nthawiyi nʼkuti mfumu ili mʼnyumba imene inkakhala mʼnyengo yozizira ndipo inkawotha moto wamʼmbaula. Umenewu unali mwezi wa 9.* 23  Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena 4 za mpukutuwo, mfumu inkadula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi nʼkuponya chidutswacho pamoto umene unali mʼmbaula uja. Inachita izi mpaka mpukutu wonsewo unathera pamotopo. 24  Iwo sanachite mantha ndipo mfumu ndi atumiki ake onse amene ankamvetsera mawuwa sanangʼambe zovala zawo. 25  Ngakhale kuti Elinatani,+ Delaya+ ndi Gemariya+ anachonderera mfumu kuti isawotche mpukutuwo, mfumuyo sinawamvere. 26  Komanso mfumu inalamula Yerameeli mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti akagwire Baruki mlembi ndi mneneri Yeremiya, koma Yehova anawabisa.+ 27  Mfumu itawotcha mpukutu umene unali ndi mawu amene Baruki analemba atauzidwa ndi Yeremiya, Yehova analankhulanso ndi Yeremiya+ kuti: 28  “Tenga mpukutu wina ndipo ulembemo mawu onse amene anali mumpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wawotcha.+ 29  Ponena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wawotcha mpukutuwu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani walemba mumpukutuwu kuti: “Mfumu ya Babulo idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndipo simudzapezeka nyama ndi munthu wokhalamo”?’+ 30  Choncho ponena za chilango chimene adzapatse Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sipadzapezeka mwana wake aliyense wokhala pampando wachifumu wa Davide+ ndipo mtembo wake udzakhala padzuwa lotentha masana ndipo usiku udzakhala panja pozizira.+ 31  Ine ndidzaimba mlandu Yehoyakimu, ana ake* ndi atumiki ake chifukwa cha zolakwa zawo. Anthu amenewa komanso anthu amene akukhala mu Yerusalemu ndi mu Yuda ndidzawagwetsera masoka onse amene ndanena+ chifukwa sanamvere.’”’”+ 32  Kenako Yeremiya anatenga mpukutu wina nʼkupatsa Baruki mlembi,+ mwana wa Neriya. Baruki analembamo mawu onse amene Yeremiya anamuuza, amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda inawotcha.+ Mumpukutumo anawonjezeramo mawu ena ambiri ochokera kwa Mulungu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mlembi.”
Kapena kuti, “Nduna zonse za panyumba ya mfumu zinali zitakhala.”
Mweziwu unkayamba cha pakati pa November mpaka pakati pa December. Onani Zakumapeto B15.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”