Yeremiya 41:1-18

  • Gedaliya anaphedwa ndi Isimaeli (1-10)

  • Yohanani anathamangitsa Isimaeli (11-18)

41  Mʼmwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10. Isimaeli anali wa mʼbanja lachifumu* ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Pamene ankadyera limodzi chakudya ku Mizipa,  Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna 10 amene anali naye ananyamuka nʼkupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani. Choncho Isimaeli anapha munthu amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.  Isimaeli anaphanso Ayuda onse amene anali ndi Gedaliya ku Mizipa komanso asilikali a Akasidi amene anali kumeneko.  Pa tsiku lachiwiri kuchokera pamene Gedaliya anaphedwa, munthu aliyense asanadziwe zimenezi,  kunabwera amuna 80 ochokera ku Sekemu,+ ku Silo+ ndi ku Samariya.+ Iwo anabwera atameta ndevu, atangʼamba zovala zawo ndiponso atadzichekacheka.+ Amunawa anabwera atanyamula nsembe yambewu komanso lubani+ kuti adzazipereke kunyumba ya Yehova.  Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ananyamuka ku Mizipa akulira kuti akakumane nawo. Atakumana nawo anawauza kuti: “Tiyeni kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu.”  Koma anthuwo atafika mumzinda, Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna amene anali naye anawapha nʼkuwaponya mʼchitsime.  Koma pakati pa anthuwo panali amuna 10 amene anauza Isimaeli kuti: “Usatiphe chifukwa tili ndi nkhokwe za tirigu, barele, mafuta ndi uchi zimene tinazibisa mʼmunda.” Choncho Isimaeli anawasiya ndipo sanawaphe ngati mmene anachitira ndi abale awo.  Isimaeli anaponya mitembo yonse ya amuna amene anawapha mʼchitsime chachikulu kwambiri. Mfumu Asa ndi imene inakumba chitsime chimenechi pamene Basa mfumu ya Isiraeli+ inamuopseza. Chitsime chimenechi ndi chimene Isimaeli mwana wa Netaniya anaponyamo mitembo ya anthu amene anawapha. 10  Isimaeli anagwira anthu ena onse amene anali ku Mizipa,+ kuphatikizapo ana aakazi a mfumu ndi anthu ena onse amene anatsala ku Mizipa omwe Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawapereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu kuti aziwayangʼanira. Isimaeli mwana wa Netaniya anawagwira ndipo ananyamuka kuti awolokere nawo kudziko la Aamoni.+ 11  Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye atamva zoipa zonse zimene Isimaeli mwana wa Netaniya anachita, 12  anatenga asilikali onse nʼkupita kukamenyana ndi Isimaeli mwana wa Netaniya ndipo anamupeza pafupi ndi madzi ambiri a ku Gibiyoni.* 13  Anthu onse amene anali ndi Isimaeli anasangalala kwambiri ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye. 14  Ndiyeno anthu onse amene Isimaeli anawagwira ku Mizipa+ anathawa nʼkubwerera limodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya. 15  Koma Isimaeli mwana wa Netaniya limodzi ndi amuna 8, anathawa ataona Yohanani ndipo anapita kwa Aamoni. 16  Ndiyeno Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye anatenga anthu onse amene anatsala ku Mizipa. Anthu amenewa ndi amene anawapulumutsa mʼmanja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Anapulumutsa amuna, asilikali, akazi, ana ndi nduna zapanyumba ya mfumu ndipo anabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni. 17  Iwo anakakhala kumalo ogona alendo a Chimamu pafupi ndi Betelehemu+ nʼcholinga choti apitirize ulendo wopita ku Iguputo.+ 18  Anachita zimenezi chifukwa cha Akasidi. Iwo ankaopa Akasidiwo chifukwa chakuti Isimaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira mʼdzikolo.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anali mbewu ya ufumu.”
Mabaibulo ena amati, “chidziwe chachikulu ku Gibiyoni.”