Yeremiya 5:1-31

  • Anthu anakana malangizo a Yehova (1-13)

  • Adzawonongedwa koma sadzawawononga onse (14-19)

  • Yehova anaimba mlandu anthu (20-31)

5  Yendayendani mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Yangʼanani mosamala kwambiri. Fufuzani mʼmabwalo ake kuti muoneNgati mungapeze munthu amene amachita zachilungamo,+Amene amayesetsa kukhala wokhulupirika,Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu.   Ngakhale atalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo!” Adzakhalabe akulumbira mwachinyengo.+   Inu Yehova, kodi si paja maso anu amayangʼana anthu amene ndi okhulupirika?+ Mwawalanga koma sanamve kupweteka.* Ngakhale kuti munatsala pangʼono kuwawononga onse, iwo sanaphunzirepo kanthu.+ Anaumitsa kwambiri nkhope zawo kuposa thanthwe,+Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+   Koma ndinati: “Ndithudi, amenewa ndi anthu onyozeka. Akuchita zinthu mopusa, chifukwa sakudziwa njira ya Yehova,Zimene Mulungu wawo amafuna.   Ndidzapita kwa anthu olemekezeka nʼkulankhula nawo,Chifukwa mosakayikira akuyenera kudziwa njira ya Yehova,Zimene Mulungu wawo amafuna.+ Koma onsewo athyola goli la MulunguNdipo adula zingwe za Mulungu.”   Nʼchifukwa chake mkango wa mʼnkhalango umawaukira,Mmbulu wamʼchipululu ukupitirizabe kuwawononga,Ndipo kambuku amakhala tcheru pamizinda yawo. Aliyense wotuluka mʼmizindayo amakhadzulidwakhadzulidwa. Chifukwa zolakwa zawo ndi zochuluka.Ndipo nthawi zambiri amachita zosakhulupirika.+   Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya,Ndipo amalumbira pa zinthu zimene si Mulungu.+ Ndinkawapatsa zimene ankafunikira,Koma anapitiriza kuchita chigololo,Ndipo ankapita kunyumba ya hule mʼchigulu.   Iwo ali ngati mahatchi amphongo achilakolako champhamvu chofuna kukwera,Aliyense amamemesa* mkazi wa mnzake.+   “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?”+ 10  “Bwerani mudzaukire minda yake ya mpesa nʼkuiwononga,Koma musaiwonongeretu.+ Dulani nthambi zake zingʼonozingʼono,Chifukwa si za Yehova. 11  Chifukwa a mʼnyumba ya Isiraeli ndi a mʼnyumba ya YudaAndichitira zachinyengo kwambiri,” akutero Yehova.+ 12  “Iwo akana Yehova ndipo akupitiriza kunena kuti,‘Iye sadzachita kanthu.*+ Palibe tsoka limene lidzatigwere.Sitidzaona nkhondo kapena njala.’+ 13  Aneneri akulankhula zopanda pake,Ndipo mwa iwo mulibe mawu a Mulungu. Nawonso adzakhala opanda pake ngati mawu awo omwewo.” 14  Choncho izi nʼzimene Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba akunena: “Chifukwa anthu awa akunena zimenezi,Ndichititsa kuti mawu anga akhale ngati moto mʼkamwa mwako,+Koma anthu awa akhala ngati nkhuniNdipo motowo udzawawotcha.”+ 15  “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu kuchokera kutali, inu a mʼnyumba ya Isiraeli,”+ akutero Yehova. “Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali, Ndi mtundu wakale kwambiri,Mtundu umene chilankhulo chake simukuchidziwa,Ndipo simungamve zimene amalankhula.+ 16  Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka.Onse ndi asilikali. 17  Iwo adzadya zokolola zanu ndi zakudya zanu.+ Adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi. Adzadya nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu. Adzadya mitengo yanu ya mpesa ndi mitengo yanu ya mkuyu. Iwo adzawononga ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.” 18  Yehova wanena kuti: “Ngakhale masiku amenewo, sindidzakuwonongani nonse.+ 19  Ndiye akadzafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zinthu zonsezi?’ udzawayankhe kuti, ‘Mofanana ndi mmene munandisiyira nʼkukatumikira mulungu wachilendo mʼdziko lanu, mudzatumikiranso alendo mʼdziko limene si lanu.’”+ 20  Ukanene izi mʼnyumba ya Yakobo,Ndipo ukazilengeze mu Yuda kuti: 21  “Tamverani izi anthu opusa komanso opanda nzeru inu:*+ Iwo ali ndi maso koma sangathe kuona,+Ali ndi makutu koma sangathe kumva.+ 22  ‘Kodi simukuchita nane mantha?’ akutero Yehova.‘Kodi simukunjenjemera pamaso panga? Ine ndi amene ndinaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,Malire amene adzakhalepo mpaka kalekale. Ngakhale kuti mafunde ake amawinduka, sangadutse malirewo.Ndipo ngakhale amachita phokoso, sangapitirire malirewo.+ 23  Koma anthu awa ali ndi mtima wosamvera komanso wopanduka.Achoka panjira yanga ndipo akuyenda mʼnjira yawo.+ 24  Mumtima mwawo sanena kuti: “Tiyeni tsopano tiope Yehova Mulungu wathu,Amene amatigwetsera mvula mʼnyengo yake,Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira,Amene amaonetsetsa kuti tikukolola pa nthawi yake.”*+ 25  Zolakwa zanu ndi zimene zachititsa kuti zinthu zimenezi zisabwere,Ndipo machimo anu akumanitsani zinthu zabwino.+ 26  Chifukwa pakati pa anthu anga pali anthu oipa. Iwo amabisala nʼkumayangʼanitsitsa ngati mmene amachitira wosaka mbalame. Amatchera msampha wakupha Ndipo amagwira anthu. 27  Mofanana ndi chikwere chimene chadzaza mbalame,Nyumba zawo zadzaza chinyengo.+ Nʼchifukwa chake iwo ali amphamvu komanso alemera kwambiri. 28  Iwo anenepa ndipo asalala.Akuchita zinthu zoipa zambiri. Iwo saweruza mlandu wa ana amasiye mwachilungamo,+Pofuna kupeza phindu.Ndipo sachitira chilungamo anthu osauka.’”+ 29  “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa? 30  Chinthu chodabwitsa komanso chochititsa mantha chachitika mʼdziko: 31  Aneneri akulosera zabodza,+Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena. Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “sanafooke.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Mabaibulo ena amati, “Iye kulibe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inu anthu opusa opanda mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmilungu yoikidwiratu.”