Yeremiya 6:1-30

  • Nthawi yoti Yerusalemu azunguliridwe yayandikira (1-9)

  • Yehova anakwiyira Yerusalemu (10-21)

    • Akunena kuti, “Mtendere!” pamene kulibe mtendere (14)

  • Anaukiridwa mwankhanza ndi anthu akumpoto (22-26)

  • Yeremiya anasandutsidwa woyenga zitsulo (27-30)

6  Bisalani inu ana a Benjamini, thawani mu Yerusalemu. Imbani lipenga la nyanga+ ya nkhosa ku Tekowa.+Yatsani chizindikiro cha moto ku Beti-hakeremu, Chifukwa tsoka likubwera kuchokera kumpoto ndipo ndi lalikulu kwambiri.+   Mwana wamkazi wa Ziyoni* akufanana ndi mkazi wokongola komanso wosasatitsidwa.+   Abusa ndi magulu awo a ziweto adzabwera. Iwo adzamanga matenti awo mozungulira Yerusalemu,+Aliyense wa iwo nʼkumadyetsa ziweto zake.+   “Konzekerani* kukachita nkhondo ndi Yerusalemu Nyamukani, tiyeni tikamuukire dzuwa lili paliwombo!” “Koma tachita tsoka chifukwa nthawi yatithera,Ndipo kunja kwayamba kuda!”   “Nyamukani, tiyeni tikamuukire usikuNdipo tikawononge nsanja zake zokhala ndi mipanda yolimba.”+   Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Dulani mitengo kuti timange malo okwera oti timenyerepo nkhondo* ndi Yerusalemu.+ Yerusalemu ndi mzinda umene ukuyenera kuimbidwa mlandu.Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+   Mofanana ndi chitsime chimene chimatulutsa madzi ozizira,Yerusalemu amatulutsanso zinthu zoipa. Mkati mwake mukumveka phokoso la chiwawa komanso kuponderezana.+Nthawi zonse ndimaona matenda ndi miliri mumzindawo.   Iwe Yerusalemu, mvera chenjezo langa, ukapanda kumvera, ndikusiya chifukwa chonyansidwa nawe.+Ndidzakusandutsa bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+   Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Adani adzakunkha otsalira onse a Isiraeli ngati mmene amakunkhira mphesa zomaliza pa mtengo wa mpesa. Kwezanso dzanja lako ngati munthu amene akuthyola mphesa panthambi za mtengo wa mpesa.” 10  “Kodi ndilankhule ndi ndani nʼkumuchenjeza? Ndi ndani adzamvetsere? Taonani! Makutu awo ndi otseka,* choncho sangathe kumva.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala chinthu chimene akunyansidwa nacho+Ndipo sakusangalala nawo. 11  Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,Ndipo ndatopa ndi kuusunga.”+ “Tsanulirani mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu,+Pa gulu la anyamata amene asonkhana pamodzi. Onse adzagwidwa, mwamuna limodzi ndi mkazi wake,Anthu achikulire limodzi ndi anthu okalamba.+ 12  Nyumba zawo limodzi ndi minda yawo komanso akazi awo,Zidzaperekedwa kwa anthu ena.+ Chifukwa ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga anthu okhala mʼdzikolo,” akutero Yehova. 13  “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+ 14  Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa anthu anga* ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+ 15  Kodi iwo amachita manyazi ndi zinthu zonyansa zimene achita? Iwo sachita manyazi ngakhale pangʼono, Ndipo sadziwa nʼkomwe kuchita manyazi.+ Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa. Ndikamadzawapatsa chilango, iwo adzapunthwa,” akutero Yehova. 16  Yehova wanena kuti: “Imani pamphambano kuti muone. Funsani zokhudza njira zakale,Funsani kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino nʼkuyenda mmenemo,+Kuti mupeze mpumulo.” Koma iwo akunena kuti: “Ife sitiyenda mʼnjira imeneyo.”+ 17  “Ine ndinaika alonda+ amene ankanena kuti,‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’”+ Koma iwo ananena kuti: “Ife sitidzamvera.”+ 18  “Choncho tamverani, inu mitundu ya anthu, Kuti mudziwe anthu inu,Zimene zidzachitikire anthu a ku Yerusalemu. 19  Tamverani, inu anthu okhala padziko lapansi! Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+Chifukwa cha maganizo awo oipa.Iwo sanamvere mawu angaNdipo anakana chilamulo changa.”* 20  “Kodi lubani* wochokera ku ShebaKomanso bango lonunkhira lochokera kudziko lakutali zimene mukundibweretsera, zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zanu zopsereza zathunthu nʼzosavomerezeka,Ndipo nsembe zanu zina zonse zimene mukupereka sizikundisangalatsa.”+ 21  Choncho Yehova wanena kuti: “Tsopano ndikuikira anthu awa zinthu zopunthwitsa,Ndipo iwo adzapunthwa ndi zinthu zimenezi,Abambo limodzi ndi ana,Munthu ndi mnzake woyandikana naye,Onse adzawonongedwa.”+ 22  Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko lakumpoto.Ndipo mtundu wamphamvu udzadzutsidwa kuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+ 23  Iwo adzagwira uta ndi nthungo. Amenewa ndi anthu ankhanza ndipo sadzasonyeza chifundo. Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanjaNdipo adzabwera pamahatchi.+ Iwo afola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ngati mwamuna wankhondo kuti amenyane nawe, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.” 24  Ife tamva uthenga wokhudza zimenezi. Manja athu alobodoka.+Tagwidwa ndi nkhawa,Ndipo tikumva ululu ngati mkazi amene akubereka.+ 25  Musatuluke kupita kunja,Ndipo musayende mumsewu,Chifukwa mdani ali ndi lupanga.Zochititsa mantha zili paliponse. 26  Iwe mwana wamkazi wa anthu anga,Vala chiguduli+ ndipo ugubuduke mʼphulusa. Lira ngati kuti ukulira maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ulire mowawidwa mtima,+Chifukwa wowononga adzatiukira modzidzimutsa.+ 27  “Ndakusandutsa* woyenga zitsulo pakati pa anthu anga,Ndakusandutsa wofufuza mosamala.Choncho uzionetsetsa ndiponso kufufuza njira zawo. 28  Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+Amayenda uku ndi uku nʼkumanena miseche.+ Iwo ali ngati kopa* ndi chitsulo,Onsewo ndi anthu achinyengo. 29  Zipangizo zopemerera moto zapsa ndi moto. Ndipo pamotopo patuluka mtovu. Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu,+Ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+ 30  Ndithu, anthu adzawatchula kuti siliva wokanidwa,Chifukwa Yehova wawakana.”+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dziyeretseni.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Makutu awo sanawachite mdulidwe.”
Kapena kuti, “mwachinyengo fupa lothyoka la anthu anga.”
Kapena kuti, “Ndipo anakana malangizo anga.”
Apa akunena Yeremiya.
Kapena kuti, “mkuwa.”