Yeremiya 8:1-22

  • Anthu anasankha njira imene anthu ambiri ankaitsatira (1-7)

  • Kodi anthu angakhale ndi nzeru popanda mawu a Yehova? (8-17)

  • Yeremiya analira chifukwa cha kuwonongedwa kwa Yuda (18-22)

    • “Kodi mu Giliyadi mulibe mafuta a basamu?” (22)

8  “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu okhala mu Yerusalemu adzatulutsidwa mʼmanda awo.  Mafupawo adzamwazidwa padzuwa, pamwezi ndi panyenyezi zonse zakumwamba* zimene ankazikonda, kuzitumikira, kuzitsatira, kuzifunafuna ndi kuzigwadira.+ Anthu sadzasonkhanitsa mafupawo pamodzi nʼkuwaika mʼmanda ndipo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+  “Ndipo anthu onse otsala a banja loipali amene adzapulumuke adzaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala ndi moyo, malo onse amene ndidzawabalalitsire,” akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  “Ndipo ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi munthu akagwa sadzukanso? Ngati munthu mmodzi atabwerera, kodi winayo sangabwererenso?   Nʼchifukwa chiyani anthu awa, anthu okhala mu Yerusalemu, ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi? Iwo akupitiriza kuchita zachinyengoNdipo akukana kubwerera.+   Ine ndinatchera khutu ndipo ndinapitiriza kuwamvetsera. Koma zimene iwo ankanena sizinali zoona. Panalibe munthu amene analapa zoipa zimene ankachita, kapena amene anafunsa kuti, ‘Nʼchiyani chimene ndachitachi?’+ Aliyense akungobwerera kunjira imene anthu ambiri akuitsatira, ngati hatchi imene ikuthamangira kunkhondo.   Ngakhale dokowe, mbalame youluka mumlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.Ndipo njiwa, namzeze komanso mbalame zina, zimadziwa nthawi yobwerera kumene zachokera.* Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+   Kodi munganene bwanji kuti: “Ndife anzeru, ndipo tili ndi chilamulo cha Yehova”?* Pamene zoona zake nʼzakuti zolembera zabodza+ za alembi zagwiritsidwa ntchito polemba zachinyengo.   Anthu anzeru achititsidwa manyazi.+ Achita mantha ndipo adzagwidwa. Taonani! Iwo akana mawu a Yehova.Ndipo kodi ali ndi nzeru zotani? 10  Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena,Minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+Chifukwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, aliyense akupeza phindu mwachinyengo.+Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+ 11  Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa mwana wamkazi* wa anthu anga ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+ 12  Kodi iwo amachita manyazi ndi zinthu zonyansa zimene achita? Iwo sachita manyazi ngakhale pangʼono, Ndipo sadziwa nʼkomwe kuchita manyazi.+ Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa. Ndikamadzawapatsa chilango, iwo adzapunthwa,”+ akutero Yehova. 13  “‘Ndikadzawasonkhanitsa, ndidzawawononga,’ akutero Yehova. ‘Mumtengo wa mpesa simudzapezeka mphesa zotsala, mumtengo wa mkuyu simudzapezeka nkhuyu ndipo masamba adzafota. Zinthu zimene ndinawapatsa zidzatayika.’” 14  “Nʼchifukwa chiyani tikungokhala pano? Tiyeni tisonkhane pamodzi ndipo tilowe mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ kuti tikafere kumeneko. Chifukwa Yehova Mulungu wathu adzatiwononga,Ndipo amatipatsa madzi apoizoni kuti timwe,+Chifukwa tachimwira Yehova. 15  Timayembekezera mtendere, koma palibe chabwino chilichonse chimene chachitika.Timayembekezera kuchiritsidwa, koma tikungoona zinthu zochititsa mantha.+ 16  Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani. Dziko lonse lagwedezekaChifukwa cha phokoso la kumemesa* kwa mahatchi ake amphongo. Adani akubwera kudzawononga dziko ndi chilichonse chimene chili mmenemo,Mzinda ndi anthu okhala mmenemo.” 17  “Ine ndikutumiza njoka pakati panu,Njoka zapoizoni zimene simungazinyengerere kuti muziseweretse,Ndipo zidzakulumani ndithu,” akutero Yehova. 18  Chisoni changa nʼchosachiritsika.Mtima wanga ukudwala. 19  Pakumveka mawu olirira thandizo kuchokera kudziko lakutali,Kuchokera kwa mwana wamkazi wa anthu anga. Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni? Kapena kodi mfumu yake mulibe mmenemo?” “Nʼchifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba,Ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?” 20  “Nthawi yokolola yadutsa ndipo nyengo yachilimwe yatha.Koma ife sitinapulumutsidwe!” 21  Ndasweka mtima chifukwa cha kuwonongeka kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+Ndine wachisoni. Ndipo ndili ndi mantha aakulu. 22  Kodi mu Giliyadi mulibe mafuta a basamu?+ Kapena kodi mulibe wochiritsa* mmenemo?+ Nʼchifukwa chiyani mwana wamkazi wa anthu anga sanachiritsidwe?+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi pamagulu onse ankhondo akumwamba.”
Kapena kuti, “nthawi yochoka dera lina kupita dera lina.”
Kapena kuti, “malangizo a Yehova.”
Kapena kuti, “kuchiritsa mwachinyengo fupa lothyoka la mwana wamkazi.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Kapena kuti, “dokotala.”