Yesaya 10:1-34
10 Tsoka kwa amene akukhazikitsa malamulo oipa,+Amene amangokhalira kulemba malamulo opondereza,
2 Kuti asamvetsere mlandu wa anthu osaukaNdiponso kuti asachitire chilungamo anthu onyozeka amene ali pakati pa anthu anga.+Amalanda katundu wa akazi amasiyeKomanso katundu wa ana amasiye.+
3 Kodi mudzatani pa tsiku lachiweruzo,*+Anthu okuwonongani akadzabwera kuchokera kutali?+
Kodi mudzathawira kwa ndani kuti akuthandizeni+Nanga chuma* chanu mudzachisiya kuti?
4 Palibe chimene mudzachite, koma mudzagwada pakati pa akaidiKapena mudzakhala mʼgulu la anthu ophedwa.
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+
5 Iye wanena kuti: “Eya! Onani Msuri,+Iye ndi ndodo yosonyezera mkwiyo wanga+Ndipo ndigwiritsa ntchito chikwapu chimene chili mʼdzanja lake popereka chilango.
6 Ndidzamutumiza kuti akalimbane ndi mtundu wopanduka,+Kuti akalimbane ndi anthu amene andikwiyitsa.Ndidzamulamula kuti akalande zinthu zambiriNdiponso kuti akapondeponde anthu ngati matope amumsewu.+
7 Koma iye sadzafuna kuchita zimeneziNdipo mtima wake sudzakonza zoti achite zimenezi.Koma chifukwa chakuti mumtima mwake amaganiza zowononga,Zoti awonongeretu mitundu yambiri, osati yochepa,
8 Iye akunena kuti,‘Kodi akalonga anga onse si mafumu?+
9 Kodi Kalino+ sali ngati Karikemisi?+
Kodi Hamati+ sali ngati Aripadi?+
Kodi Samariya+ sali ngati Damasiko?+
10 Dzanja langa lagwira maufumu olambira milungu yopanda phindu,Amene zifaniziro zawo zogoba zinali zambiri kuposa za ku Yerusalemu ndi ku Samariya.+
11 Kodi zimene ndachitira Samariya ndi milungu yake yopanda phindu,+Si zimenenso ndidzachitire Yerusalemu ndi mafano ake?’
12 Yehova akadzamaliza ntchito yake yonse mʼphiri la Ziyoni komanso mu Yerusalemu, adzalanga mfumu ya Asuri chifukwa cha mwano umene uli mumtima mwake ndiponso chifukwa chakuti amayangʼana monyada ndi modzikuza.+
13 Chifukwa iye wanena kuti,‘Ndidzachita zimenezi ndi mphamvu za manja angaNdiponso ndi nzeru zanga chifukwa ndine wanzeru.
Ndidzachotsa malire a mitundu ya anthu+Ndipo ndidzatenga zinthu zawo zamtengo wapatali.+Ngati munthu wamphamvu, ndidzagonjetsa anthu okhala mmenemo.+
14 Mofanana ndi munthu amene akupisa dzanja lake mʼchisa,Dzanja langa lidzalanda zinthu zofunika za anthu a mitundu ina.Ngati mmene munthu amasonkhanitsira mazira amene asiyidwa,Ine ndidzasonkhanitsa zinthu zonse zapadziko lapansi.
Palibe aliyense amene adzakupize mapiko ake kapena kutsegula pakamwa pake kapenanso kulira ngati mbalame.’”
15 Kodi nkhwangwa ingadzikuze pamaso pa munthu amene akuigwiritsa ntchito?
Kodi chochekera matabwa chingadzikweze pamaso pa munthu amene akuchigwiritsa ntchito?
Kodi chikwapu+ chinganyamule munthu amene wachinyamula mʼmwamba,
Kapena kodi ndodo inganyamule mʼmwamba munthu amene si mtengo?
16 Choncho Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwambaAdzachititsa kuti anthu ake* onenepa awonde,+Ndipo pansi pa ulemerero wake adzayatsapo moto.+
17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+Ndipo Woyera wake adzasanduka lawi lamoto.Motowo udzayaka nʼkupsereza udzu wake komanso zitsamba zake zaminga pa tsiku limodzi.
18 Mulungu adzathetseratu ulemerero wa nkhalango yake ndi wa munda wake wa zipatso,Ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuonda.+
19 Mitengo yotsala yamʼnkhalango mwakeIdzakhala yochepa kwambiri moti kamnyamata kadzatha kulemba chiwerengero chake.
20 Tsiku limenelo, otsala a IsiraeliNdi amʼnyumba ya Yakobo amene adzapulumukeSadzadaliranso amene anawamenya,+Koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova,Woyera wa Isiraeli.
21 Otsala okha ndi amene adzabwerere,Otsala a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.+
22 Ngakhale kuti anthu ako iwe Isiraeli,Ali ngati mchenga wakunyanja,Otsala ochepa okha pakati pawo ndi amene adzabwerere.+
Mulungu wakonza zoti anthuwo awonongedwe+Ndipo chilango cholungama chidzawabwerera ngati madzi osefukira.+
23 Zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wakonza zoti awononge anthuwo,Zidzachitika padziko lonselo.+
24 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Anthu anga amene mukukhala mʼZiyoni, musachite mantha chifukwa cha Msuri amene ankakukwapulani ndi chikwapu+ ndiponso kukumenyani ndi ndodo, ngati mmene ankachitira Iguputo.+
25 Chifukwa pakangodutsa kanthawi kochepa, kudzudzulako kudzatha ndipo mkwiyo wanga udzawayakira, moti adzawonongedwa.+
26 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzamʼkwapula ndi chikwapu+ ngati mmene anachitira pamene anagonjetsa Midiyani pathanthwe la Orebi.+ Adzatambasula ndodo yake ndi kuloza panyanja ndipo adzaikweza mʼmwamba ngati mmene anachitira ndi Iguputo.+
27 Tsiku limenelo katundu wake adzachoka paphewa panu,+Ndipo goli lake lidzachoka mʼkhosi mwanu.+Golilo lidzathyoledwa+ chifukwa cha mafuta.”
28 Iye wafika ku Ayati.+Wadutsa ku Migironi.Ndipo katundu wake wamuika ku Mikimasi.+
29 Iwo adutsa powolokera mtsinje.Usiku agona ku Geba.+Rama wanjenjemera ndipo Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, wathawa.+
30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu, lira ndi kufuula kwambiri.
Khala tcheru iwe Laisa,
Iwenso Anatoti womvetsa chisoni!+
31 Madimena wathawa.
Anthu okhala ku Gebimu abisala.
32 Tsiku lomwelo iye akaima ku Nobu.+
Iye akuopseza ndi chibakera phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni,*Phiri limene pali Yerusalemu.
33 Taonani! Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Akudula nthambi ndipo zikugwa ndi mkokomo waukulu.+Mitengo italiitali ikudulidwa,Ndipo imene ili mʼmwamba ikutsitsidwa.
34 Iye wadula ndi nkhwangwa zitsamba zowirira zamʼnkhalango,Ndipo wamphamvu adzawononga Lebanoni.