Yesaya 12:1-6

  • Nyimbo yosonyeza kuyamikira (1-6)

    • “Ya, Yehova ndi mphamvu zanga” (2)

12  Pa tsiku limenelo ndithu udzanena kuti: “Ndikukuthokozani, inu YehovaChifukwa ngakhale munandikwiyira,Mkwiyo wanu unachepa pangʼonopangʼono ndipo munanditonthoza.+   Taonani! Mulungu ndi chipulumutso changa.+ Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+Chifukwa Ya,* Yehova, ndi mphamvu zanga komanso nyonga zanga,Ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+   Mudzatunga madzi mosangalalaPa akasupe achipulumutso.+   Pa tsiku limenelo mudzanena kuti: “Yamikani Yehova, itanani pa dzina lake,Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+ Lengezani kuti dzina lake ndi lokwezeka.+   Imbani nyimbo zotamanda Yehova,+ chifukwa wachita zinthu zodabwitsa.+ Lengezani zimenezi padziko lonse lapansi.   Fuulani mwachisangalalo inu okhala mu Ziyoni,*Chifukwa Woyera wa Isiraeli amene ali pakati panu ndi wamkulu.”

Mawu a M'munsi

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mʼchilankhulo choyambirira, “iwe mkazi wokhala mu Ziyoni.” Apa anthu onse okhala mu Ziyoni akuwatenga ngati mkazi.