Yesaya 15:1-9

  • Uthenga wokhudza Mowabu (1-9)

15  Uwu ndi uthenga wokhudza Mowabu:+ Chifukwa chakuti wawonongedwa usiku umodzi wokha,Ari+ wa ku Mowabu wakhalitsidwa chete. Chifukwa chakuti wawonongedwa usiku umodzi wokha,Kiri+ wa ku Mowabu wakhalitsidwa chete.   Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni,+Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha zimene zachitikira Nebo+ ndi Medeba.+ Mutu uliwonse aumeta mpala+ ndipo ndevu zonse zametedwa.+   Anthu avala ziguduli mʼmisewu yake. Pamadenga awo komanso mʼmabwalo a mizinda yawo, onse akulira mofuula.Akulira nʼkumapita kumunsi.+   Hesiboni ndi Eleyale+ akulira mofuula.Mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.+ Nʼchifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula. Iwo akunjenjemera kwambiri.   Mtima wanga ukulirira Mowabu. Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Iwo akulira pamene akukwera mtunda wa Luhiti.Panjira yopita ku Horonaimu, iwo akulira kwambiri chifukwa cha tsokalo.+   Madzi a ku Nimurimu aumiratu.Msipu wobiriwira wauma,Udzu watha ndipo palibenso chilichonse chobiriwira chimene chatsala.   Nʼchifukwa chake akunyamula zinthu zimene zatsala pa katundu amene anasunga komanso chuma chawo.Iwo akuwoloka chigwa* cha mitengo ya msondodzi.   Chifukwa kulira kwake kwamveka mʼdziko lonse la Mowabu.+ Kulira kwake kofuula kwamveka mpaka ku Egilaimu.Kulira kwake kofuula kwamveka mpaka ku Beere-elimu.   Madzi onse a ku Dimoni adzaza magazi,Ndipo Mulungu adzamʼbweretsera Dimoni masoka ambiri, Adzatumiza mikango kwa anthu a ku Mowabu amene adzathaweKomanso kwa anthu otsala mʼdzikolo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “khwawa.”