Yesaya 21:1-17
21 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu chimene chili ngati nyanja:*+
Ukubwera ngati mphepo yamkuntho imene ikuwomba kumʼmwera,Kuchokera kuchipululu, kuchokera kudziko lochititsa mantha.+
2 Ndauzidwa masomphenya ochititsa mantha akuti:
Mtundu wachinyengo ukuchita zachinyengo,Ndipo mtundu wowononga ukuwononga.
Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+
Ndidzathetsa mavuto onse amene mzindawo unachititsa.+
3 Nʼchifukwa chake ndili pa ululu woopsa.*+
Zopweteka zandigwira,Ngati zowawa za mkazi amene akubereka.
Ndili ndi nkhawa yaikulu moti sindikumva.Ndasokonezeka kwambiri moti sindikuona.
4 Mtima wanga ukuthamanga. Ndikunjenjemera ndi mantha.
Chisisira cha madzulo chimene ndinkachilakalaka chikundichititsa mantha.
5 Yalani patebulo ndipo muike mipando mʼmalo mwake.
Idyani komanso kumwa.+
Nyamukani akalonga inu, dzozani* chishango.
6 Chifukwa izi ndi zimene Yehova anandiuza:
“Pita, ukaike mlonda pamalo ake ndipo ukamuuze kuti azinena zonse zimene waona.”
7 Mlondayo anaona galeta lankhondo lokokedwa ndi mahatchi awiri,Galeta lankhondo lokokedwa ndi abulu,Galeta lankhondo lokokedwa ndi ngamila.
Iye ankayangʼanitsitsa mwatcheru kwambiri.
8 Kenako anafuula mwamphamvu ngati kubangula kwa mkango kuti:
“Inu Yehova, ine ndimaimirira tsiku lonse pansanja ya mlonda,Ndipo usiku uliwonse ndimakhala pamalo anga olonderapo.+
9 Taonani zimene zikubwera:
Kukubwera amuna amene akwera galeta lankhondo limene likukokedwa ndi mahatchi awiri.”+
Kenako iye analankhula kuti:
“Wagwa! Babulo wagwa!+
Zifaniziro zonse zogoba za milungu yake zaphwanyidwa ndipo zili pansi.”+
10 Inu anthu anga amene mwapunthidwa ngati mbewu,Mbewu zapamalo* anga opunthira,+Ndakuuzani zonse zimene ndamva kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli.
11 Uwu ndi uthenga wokhudza Duma:*
Ndikumva winawake akundifunsa mofuula kuchokera ku Seiri kuti:+
“Mlonda, kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti kuche?
Mlonda, kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti kuche?”
12 Mlondayo anayankha kuti:
“Mʼmawa ukubwera, ndipo usiku ukubweranso.
Ngati mukufuna kufunsa, funsani.
Ndipo mubwerenso.”
13 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu:*
Inu amtengatenga a ku Dedani+ oyenda pangamila,Usiku mudzagona mʼnkhalango yamʼchipululu.
14 Mubweretse madzi podzakumana ndi munthu waludzu,Inu anthu okhala ku dziko la Tema,+Ndipo mubweretse chakudya kuti mudzapatse munthu amene akuthawa.
15 Chifukwa iwo athawa malupanga, athawa lupanga limene lasololedwa,Athawa uta umene wakungidwa ndiponso zoopsya zimene zikuchitika kunkhondo.
16 Chifukwa izi ndi zimene Yehova anandiuza: “Chaka chimodzi chisanathe, mofanana ndi zaka za munthu waganyu,* ulemerero wonse wa Kedara+ udzakhala utatha.
17 Padzatsala asilikali ochepa oponya mivi ndi uta a ku Kedara, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena zimenezi.”
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti akunena za chigawo cha Babeloniya wakale.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchiuno mwanga mwadzaza ululu woopsa.”
^ Kapena kuti, “thirani mafuta.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwana wamwamuna wapamalo.”
^ Kutanthauza, “Kukhala Chete.”
^ Zikuoneka kuti akunena chipululu cha Arabiya.
^ Kapena kuti, “zimene zidzawerengedwe mosamala kwambiri ngati mmene munthu waganyu amachitira,” kutanthauza ndendende chaka chimodzi.