Yesaya 22:1-25
22 Uwu ndi uthenga wokhudza Chigwa cha Masomphenya:*+
Kodi chachitika nʼchiyani kuti anthu ako onse akwere pamadenga?
2 Iwe unali mzinda wodzaza ndi chipwirikiti,Mzinda waphokoso komanso tauni yonyada.
Anthu ako amene aphedwa, sanaphedwe ndi lupangaKapena kufera kunkhondo.+
3 Olamulira ako onse ankhanza athawira limodzi.+
Anagwidwa kuti akhale akaidi popanda kugwiritsa ntchito uta.
Onse amene anapezeka anagwidwa kuti akhale akaidi,+Ngakhale kuti anathawira kutali.
4 Nʼchifukwa chake ndanena kuti: “Musandiyangʼanitsitse,Ine ndilira mopwetekedwa mtima.+
Musaumirire kunditonthozaPamene ndikulira chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
5 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,Wabweretsa tsiku lachisokonezo, lakugonjetsedwa ndiponso lothetsa nzeru+MʼChigwa cha Masomphenya.
Kumeneko mpanda ukugwetsedwa+Ndipo kufuula kopempha thandizo kukumveka mʼphiri.
6 Anthu a ku Elamu+ atenga kachikwama koikamo miviNdipo akwera magaleta ankhondo ndi mahatchi,Anthu a ku Kiri+ achotsa chophimbira* chishango.
7 Mʼzigwa zako zabwino kwambiriMudzadzaza magaleta ankhondo,Ndipo mahatchi adzaima mʼmalo awo pageti,
8 Chophimba* cha Yuda chidzachotsedwa.
Pa tsiku limenelo mudzayangʼana kumalo osungirako zida zankhondo amene ali ku Nyumba ya Nkhalango,+
9 ndipo mudzaona mingʼalu yambiri ya Mzinda wa Davide.+ Mudzatunga madzi mʼdziwe lakumunsi.+
10 Mudzawerenga nyumba za ku Yerusalemu ndipo mudzagwetsa nyumba kuti mulimbitsire mpanda wake.
11 Mudzakumba dziwe pakati pa makoma awiri, losungiramo madzi a dziwe lakale. Koma simudzadalira Wolipanga Wamkulu ndipo simudzaganizira za amene analipanga kale kwambiri.
12 Pa tsiku limenelo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,Adzalamula anthu kuti alire ndi kugwetsa misozi,+Komanso kuti amete mipala ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalomwake mukukondwera ndi kusangalala,Mukupha ngʼombe ndi nkhosa,Mukudya nyama ndi kumwa vinyo.+
Inu mukuti, ‘Tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tifa.’”+
14 Kenako Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anandiuza kuti: “‘Tchimo ili silidzakhululukidwa mpaka anthu inu mutafa,’+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pita kwa Sebina,+ kapitawo woyangʼanira nyumba ya mfumu, ndipo ukamuuze kuti,
16 ‘Kodi kuno kuli wachibale wako aliyense, ndipo kodi mʼbale wako anaikidwa kuno kuti iweyo udzigobere manda kunoko?’ Iye wagoba manda ake pamalo okwera. Akudzigobera malo opumulirako* mʼthanthwe.
17 ‘Tamvera munthu iwe! Yehova adzakuponya pansi mwamphamvu komanso adzakugwira mwamphamvu.
18 Ndithu iye adzakukulunga mwamphamvu ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu ngati akuponya mpira. Iweyo udzafera kumeneko ndipo magaleta ako ankhondo aulemerero adzakhala kumeneko. Zidzakhala zochititsa manyazi ku nyumba ya mbuye wako.
19 Ndidzakuchotsa pampando wako ndipo ndidzakuchotsa pa udindo wako.
20 Pa tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu,+ mwana wa Hilikiya.
21 Iyeyo ndidzamuveka mkanjo wako ndipo lamba wako ndidzamumanga mwamphamvu mʼchiuno mwake.+ Ulamuliro wako ndidzaupereka mʼmanja mwake ndipo iye adzakhala tate wa anthu okhala mu Yerusalemu ndi amʼnyumba ya Yuda.
22 Ndidzaika kiyi wa nyumba ya Davide+ paphewa pake. Iye adzatsegula ndipo palibe amene adzatseke, adzatseka ndipo palibe amene adzatsegule.
23 Ndidzamukhomerera ngati chikhomo pamalo okhalitsa. Iye adzakhala ngati mpando wachifumu waulemerero kunyumba ya bambo ake.
24 Anthu adzapachika pa iyeyo ulemerero* wonse wa nyumba ya bambo ake, mbadwa komanso ana,* ziwiya zonse zingʼonozingʼono, ziwiya zolowa ndiponso mitsuko yonse ikuluikulu.’
25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo chikhomo chimene chinakhomedwa pamalo okhalitsa chidzachotsedwa.+ Chidzadulidwa ndipo chidzagwa pansi. Katundu amene anapachikidwa pamenepo adzagwa pansi nʼkuwonongeka, chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi.’”