Yesaya 24:1-23

  • Yehova adzachotsa anthu onse mʼdziko (1-23)

    • Yehova ndi Mfumu mu Ziyoni (23)

24  Taonani! Yehova akuchotsa anthu onse mʼdziko nʼkulisiya lopanda kanthu.+ Iye wawononga* dzikolo,+ nʼkubalalitsa anthu okhala mmenemo.+  2  Zidzachitika mofanana kwa aliyense: Kwa anthu ndi kwa wansembe,Kwa wantchito ndi kwa mbuye wake,Kwa wantchito wamkazi ndi kwa mbuye wake wamkazi,Kwa wogula ndi kwa wogulitsa,Kwa wobwereketsa ndi kwa wobwereka,Kwa wobwereketsa ndalama ndi kwa wobwereka ndalama.+  3  Anthu onse adzachotsedwa mʼdzikolo.Katundu yense wamʼdzikolo adzatengedwa,+Chifukwa Yehova ndi amene wanena mawu amenewa.  4  Dzikolo likulira*+ ndipo likuwonongeka. Nthaka ya dziko lapansi yafota ndipo ikutha. Anthu otchuka amʼdzikolo afota.  5  Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo,+Chifukwa anyalanyalaza malamulo,+Asintha malamulo+Ndipo aphwanya pangano limene linayenera kukhalapo mpaka kalekale.*+  6  Nʼchifukwa chake temberero lameza dzikolo,+Ndipo anthu okhala mʼdzikolo apezeka ndi mlandu. Nʼchifukwa chake anthu okhala mʼdzikolo achepamo,Ndipo anthu amene atsalamo ndi ochepa kwambiri.+  7  Vinyo watsopano akulira* ndipo mtengo wa mpesa wafota,+Anthu onse amene amasangalala mumtima mwawo akulira.+  8  Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi maseche zasiya kumveka.Phokoso la anthu amene akusangalala latha.Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi zeze sizikumvekanso.+  9  Anthu akumwa vinyo popanda nyimbo,Ndipo amene akumwa mowa akuumva kuwawa. 10  Tauni imene anthu ake anachokamo yawonongedwa.+Nyumba iliyonse yatsekedwa kuti munthu asalowemo. 11  Anthu akulilira vinyo mʼmisewu. Kusangalala konse kwatha.Chisangalalo cha dzikolo chachoka.+ 12  Mzinda wasanduka bwinja.Geti laphwanyidwa ndipo langokhala mulu wazinyalala.+ 13  Izi ndi zimene zidzachitike mʼdzikolo, pakati pa anthu a mitundu ina: Adzakhala ngati zipatso zotsala mumtengo wa maolivi utagwedezedwa,+Ndiponso ngati mphesa zokunkha zimene zatsala anthu atamaliza kukolola.+ 14  Iwo adzafuula mwamphamvu,Adzafuula mosangalala. Adzalengeza za ulemelero wa Yehova kuchokera kunyanja.*+ 15  Nʼchifukwa chake iwo adzalemekeze Yehova mʼchigawo cha kuwala.*+Mʼzilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ 16  Tikumva nyimbo zikuimbidwa kuchokera kumalekezero a dziko kuti: “Ulemelero upite kwa Wolungamayo.”+ Koma ine ndikuti: “Ndatheratu! Ndatheratu ine! Mayo ine! Anthu akupusitsa anzawo komanso kuwachitira zachinyengo.Iwo akupitirizabe kuchitira anzawo zachinyengo ndi kuwapusitsa.”+ 17  Mantha, dzenje ndi msampha zikudikira iwe, munthu wokhala mʼdzikoli.+ 18  Aliyense wothawa phokoso la chinthu chochititsa mantha adzagwera mʼdzenje,Ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzagwidwa mumsampha.+ Chifukwa zotsekera madzi akumwamba zidzatsegulidwa,Ndipo maziko a dziko adzagwedezeka. 19  Dzikolo langʼambika pakati.Dzikolo lagwedezeka.Dzikolo likunjenjemera mwamphamvu.+ 20  Dzikolo likudzandira ngati munthu woledzera.Likugwedezekera uku ndi uku ngati chisimba* chimene chikugwedezeka ndi mphepo. Dzikolo lalemedwa ndi zolakwa zake,+Ndipo lidzagwa moti silidzadzukanso. 21  Tsiku limenelo Yehova adzapereka chiweruzo kwa gulu lankhondo lakumwambaNdi kwa mafumu apadziko lapansi. 22  Iwo adzasonkhanitsidwa pamodziNgati akaidi amene akuwasonkhanitsira mʼdzenje,Ndipo adzatsekeredwa mʼndende,Pambuyo pa masiku ochuluka adzakumbukiridwanso. 23  Mwezi wathunthu udzachita manyazi,Ndipo dzuwa lowala lidzachita manyazi,+Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wakhala Mfumu+ mʼphiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu,Ulemerelo wake waonekera pamaso pa achikulire a anthu ake.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wagadabuza.”
Mabaibulo ena amati, “lauma.”
Kapena kuti, “pangano lakalekale.”
Mabaibulo ena amati, “wauma.”
Kapena kuti, “kumadzulo.”
Kapena kuti, “kumʼmawa.”
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “achikulire ake.”