Yesaya 25:1-12

  • Anthu a Mulungu adzadalitsidwa kwambiri (1-12)

    • Phwando la Yehova la vinyo wabwino kwambiri (6)

    • Imfa sidzakhalaponso (8)

25  Inu Yehova ndinu Mulungu wanga. Ndikukukwezani ndi kutamanda dzina lanuChifukwa mwachita zinthu zodabwitsa,+Zinthu zimene munali ndi cholinga choti muzichite kuyambira kalekale,+Mwazichita mokhulupirika+ komanso modalirika.   Mwasandutsa mzinda kukhala mulu wamiyalaTauni yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mwaisandutsa bwinja lokhalokha. Mzinda wachitetezo champhamvu wa anthu achilendo mwauthetsaNdipo sudzamangidwanso.   Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani.Mzinda wa mitundu yankhanza udzakuopani.+   Chifukwa inu mwakhala malo otetezeka kwa munthu wonyozekaMalo otetezeka kwa munthu wosauka pamene akukumana ndi mavuto.+Mwakhala malo obisalirapo mvula yamkunthoNdiponso mthunzi wobisalirapo kutentha kwa dzuwa.+ Mwakhala wotero pamene anthu ankhanza akuwomba anzawo ngati mvula yamkuntho imene ikuwomba khoma.   Mofanana ndi kutentha mʼdziko lopanda madzi,Mumathetsa phokoso la anthu achilendo. Mofanana ndi kutentha kumene kumatha kunja kukachita mitambo,Nayonso nyimbo ya anthu ankhanza yaletsedwa.   Mʼphiri ili,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakonzera anthu a mitundu yonse,Phwando la zakudya zabwino kwambiri,+Phwando la vinyo wabwino kwambiri,*Phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta amʼmafupa,Ndiponso la vinyo wabwino kwambiri, wosefedwa bwino.   Mʼphiri limeneli iye adzachotsa* chophimba chimene chikuphimba anthu a mitundu yonseNdi nsalu imene yakuta mitundu yonse ya anthu.   Iye adzameza* imfa kwamuyaya+Ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.+ Adzachotsa kunyozeka kwa anthu ake padziko lonse lapansi,Chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi.   Pa tsiku limenelo anthu akewo adzanena kuti: “Taonani! Uyu ndi Mulungu wathu.+ Chiyembekezo chathu chinali mwa iye+Ndipo iye watipulumutsa.+ Uyu ndi Yehova. Chiyembekezo chathu chinali mwa iye. Tiyeni tisangalale ndi kukondwera chifukwa watipulumutsa.”+ 10  Dzanja la Yehova lidzateteza* phiri limeneli,+Ndipo Mowabu adzapondedwapondedwa mʼdziko lake lomwe+Ngati udzu umene wapondedwapondedwa nʼkukhala mulu wa manyowa. 11  Iye adzamenya mzindawo ndi manja akeNgati mmene munthu amamenyera madzi ndi manja ake akamasambira.Adzathetsa kunyada kwa mzindawo+Poumenya mwaluso ndi manja ake. 12  Ndipo mizinda yotetezeka yokhala ndi mipanda italiitali yolimba kwambiri,Adzaigwetsera pansi.Adzaigumula nʼkuigwetsera pansi, pafumbi penipeni.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “vinyo yemwe nsenga zake zadikha pansi chifukwa chokhalitsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzameza.”
Kapena kuti, “adzathetsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakhazikika pa.”