Yesaya 3:1-26

  • Atsogoleri a Yuda akusocheretsa anthu (1-15)

  • Kuweruzidwa kwa ana aakazi a Ziyoni amene amakopa amuna (16-26)

3  Tamverani! Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Akuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo,Monga mkate ndi madzi.+   Akuchotsanso mwamuna wamphamvu, munthu wankhondo,Woweruza, mneneri,+ woombeza, mkulu,   Mtsogoleri wa anthu 50,+ munthu wolemekezeka, mlangizi,Katswiri wa matsenga komanso munthu waluso lodziwa kuseweretsa njoka.+   Ndidzaika anyamata kuti akhale akalonga awoNdipo anthu ankhanza* adzawalamulira.   Anthu azidzaponderezana,Aliyense adzapondereza mnzake.+ Mnyamata adzamenya munthu wachikulire,Ndipo munthu wonyozeka adzalimbana ndi munthu wolemekezeka.+   Aliyense adzagwira mʼbale wake mʼnyumba mwa bambo ake nʼkumuuza kuti: “Iwe uli ndi nsalu, ndiye ukhale wolamulira wathu. Uzilamulira mulu wa bwinjawu.”   Tsiku limenelo iye adzakana nʼkunena kuti: “Ine sindikufuna kukhala womanga* zilonda zanu.Mʼnyumba mwanga mulibe chakudya kapena zovala. Musandiike kuti ndikhale wolamulira anthuwa.”   Yerusalemu wapunthwaNdipo Yuda wagwa,Chifukwa zonena ndi zochita zawo zikutsutsana ndi Yehova.Iwo achita zinthu zomupandukira pamaso pake polemekezeka.*+   Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,Ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo mofanana ndi anthu a ku Sodomu.+Iwo sanayese nʼkomwe kulibisa. Tsoka kwa iwo, chifukwa akudzibweretsera mavuto. 10  Uzani anthu olungama kuti zidzawayendera bwino,Iwo adzalandira mphoto chifukwa cha zimene akuchita.*+ 11  Tsoka kwa munthu woipa! Iye adzakumana ndi mavuto aakulu,Chifukwa zimene anachitira ena ndi manja ake, nayenso adzamuchitira zomwezo. 12  Amene amayangʼanira anthu anga akamagwira ntchito, akuwachitira nkhanza,Ndipo akazi ndi amene akuwalamulira. Inu anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani,Ndipo achititsa kuti musadziwe njira yoyenera kutsatira.+ 13  Yehova wakhala pamalo ake kuti aimbe anthu mlandu,Waimirira kuti aweruze mitundu ya anthu. 14  Yehova adzaweruza akulu komanso akalonga a anthu ake. “Inuyo mwawotcha munda wa mpesa,Ndipo zinthu zimene munaba kwa anthu osauka zili mʼnyumba zanu.+ 15  Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya anthu angaKomanso kukhulitsa nkhope za anthu osauka padothi?”+ akutero Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 16  Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti ana aakazi a Ziyoni ndi onyada,Akuyenda mwamatama,*Amakopa amuna ndi maso awo, nʼkumayenda modzigomera,Komanso amapanga phokoso chifukwa cha zodzikongoletsera zimene amavala mʼmiyendo yawo, 17  Yehova adzachititsa zipere mʼmutu mwa ana aakazi a Ziyoni,Ndipo Yehova adzachititsa kuti mʼmutu mwawo mukhale mpala.+ 18  Tsiku limenelo Yehova adzachotsa zodzikongoletsera zawo zonse.Adzachotsa zibangili za mʼmiyendo, zinthu zomanga kumutu, zodzikongoletsera zooneka ngati mwezi,+ 19  Ndolo, zibangili za mʼmanja, nsalu zofunda kumutu, 20  Maduku, matcheni ovala mʼmiyendo, malamba a pachifuwa,Zoikamo mafuta onunkhira,* zithumwa,* 21  Mphete zovala mʼzala, mphete zovala pamphuno, 22  Mikanjo yovala pa nthawi zapadera, malaya ovala pamwamba, mikanjo yabwino kwambiri, tizikwama, 23  Magalasi amʼmanja odziyangʼanira,+ zovala,Nduwira ndi nsalu zofunda kumutu. 24  Mʼmalo mwa mafuta onunkhira a basamu+ padzangokhala fungo loipa.Mʼmalo mwa lamba padzakhala chingwe.Mʼmalo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala.+Mʼmalo mwa chovala chamtengo wapatali adzavala chiguduli,+Ndipo padzakhala chipsera* mʼmalo mwa kukongola. 25  Amuna ako adzaphedwa ndi lupanga,Ndipo amuna ako amphamvu adzaphedwa pa nkhondo.+ 26  Malo olowera mumzinda adzalira ndipo adzamva chisoni,+Mzindawo udzakhala padothi penipeni ndipo udzakhala wopanda chilichonse.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “osachedwa kusintha maganizo.”
Kapena kuti, “wochiritsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmaso ake olemekezeka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzadya zipatso za zochita zawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atasolola makosi awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba zimene mumakhala moyo.”
Kapena kuti, “zigoba zodzikongoletsera.”
Chimenechi ndi chizindikiro chimene ankachiika pathupi la kapolo kapena mkaidi.