Yesaya 31:1-9

  • Thandizo lenileni limachokera kwa Mulungu, osati kwa anthu (1-9)

    • Mahatchi a ku Iguputo ndi zinyama (3)

31  Tsoka kwa anthu amene amapita ku Iguputo kukapempha thandizo,+Amene amadalira mahatchi,+Amene amadalira magaleta ankhondo chifukwa chakuti ndi ambiri,Komanso mahatchi ankhondo* chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri. Koma sayangʼana kwa Woyera wa Isiraeli,Ndipo safunafuna Yehova.  2  Koma iyenso ndi wanzeru ndipo adzabweretsa tsoka,Komanso sadzabweza mawu ake. Iye adzaukira nyumba ya anthu ochita zoipaKomanso amene amathandiza anthu ochita zoipa.+  3  Koma Aiguputowo ndi anthu wamba ndipo si Mulungu.Mahatchi awo ndi zinyama, osati mzimu.+ Yehova akadzatambasula dzanja lake,Aliyense amene amapereka thandizo adzapunthwaNdipo aliyense amene akuthandizidwa adzagwa.Onsewo adzawonongedwa nthawi imodzi.  4  Chifukwa izi ndi zimene Yehova wandiuza: “Mkango umalira moopseza, mkango wamphamvu umalira poteteza nyama imene wagwira.Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse,Suchita mantha ukamva mawu awoKapena kutekeseka chifukwa cha phokoso lawo.Mofanana ndi zimenezi, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatsika kuti achite nkhondoPoteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake lalingʼono.  5  Mofanana ndi mbalame imene imauluka kuti iteteze ana ake, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza mzinda wa Yerusalemu.+ Iye adzauteteza nʼkuupulumutsa. Adzaonetsetsa kuti usawonongedwe ndipo adzaulanditsa.” 6  “Aisiraeli inu, bwererani kwa Mulungu amene mwamupandukira mopanda manyazi.+ 7  Chifukwa pa tsiku limenelo, aliyense wa inu adzataya milungu yake yasiliva yomwe ndi yachabechabe komanso milungu yake yagolide yopanda phindu, imene manja anu anapanga nʼkukuchimwitsani.  8  Msuri adzaphedwa ndi lupanga, koma osati la munthu.Lupanga lidzamudya, koma osati la munthu.+ Iye adzathawa chifukwa cha lupangaloNdipo anyamata ake adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo.  9  Thanthwe lake lidzachoka chifukwa cha mantha,Ndipo akalonga ake adzachita mantha chifukwa cha chizindikiro,” akutero Yehova,Amene kuwala kwake kuli mu Ziyoni* ndiponso amene ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anthu okwera pamahatchi.”
Kapena kuti, “moto wake uli mu Ziyoni.”