Yesaya 32:1-20

  • Mfumu ndi akalonga adzalamulira mwachilungamo chenicheni (1-8)

  • Chenjezo kwa akazi ochita zinthu motayirira (9-14)

  • Adzadalitsidwa akadzalandira mzimu (15-20)

32  Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+Ndipo akalonga adzalamuliranso mwachilungamo.   Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo,Malo obisalirapo* mvula yamkuntho,Ngati mitsinje yamadzi mʼdziko lopanda madzi,+Ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu mʼdziko louma.   Pa nthawiyo maso a anthu amene akutha kuona sadzatsekeka,Ndipo makutu a anthu amene amamva adzamvetsera mwatcheru.   Mtima wa anthu opupuluma udzaganizira mofatsa kuti udziwe zinthu,Ndipo ngakhale lilime la anthu achibwibwi lidzalankhula bwinobwino komanso zinthu zomveka.+   Munthu wopusa sadzatchedwanso wopatsa,Ndipo munthu wopanda khalidwe sadzatchedwa wolemekezeka,   Chifukwa munthu wopusa adzalankhula zinthu zopanda nzeru,Ndipo mtima wake udzaganiza zochita zinthu zopweteka ena.+Iye adzachita zimenezi kuti alimbikitse mpatuko* komanso kuti azinenera Yehova zinthu zoipa,Kuti achititse munthu wanjala kukhala wopanda chakudyaNdiponso munthu waludzu kukhala wopanda chilichonse choti amwe.   Munthu wamakhalidwe oipa, njira zake nʼzoipa.+Iye amalimbikitsa anthu kuchita khalidwe lochititsa manyaziNʼcholinga choti asokoneze munthu wozunzika ndi wosauka pogwiritsa ntchito mabodza,+Ngakhale pamene munthuyo akunena zoona.   Koma munthu wopatsa amakhala ndi zolinga zochita zinthu mowolowa manja,Ndipo nthawi zonse zochita zake zimasonyeza kuti ndi wopatsa.   “Inu akazi ochita zinthu motayirira, nyamukani ndipo mvetserani mawu anga! Inu ana aakazi osasamala,+ mvetserani zimene ndikunena! 10  Pakangodutsa chaka chimodzi, inu amene mumachita zinthu mosasamala mudzadzidzimuka,Chifukwa sipadzakhala mphesa zilizonse zimene zasonkhanitsidwa ngakhale nyengo yokolola mphesa itatha.+ 11  Njenjemerani, inu akazi ochita zinthu motayirira! Dzidzimukani, inu ochita zinthu mosasamala! Vulani nʼkukhala maliseche,Ndipo muvale ziguduli mʼchiuno mwanu.+ 12  Dzimenyeni pachifuwa pomva chisoniChifukwa cha kuwonongeka kwa minda yachonde ndi minda ya mpesa. 13  Panthaka ya anthu anga padzamera zitsamba zaminga.Zidzamera panyumba zonse zimene kale zinali zodzaza ndi chisangalalo,Inde, pamzinda umene kale unali wodzaza ndi chikondwerero.+ 14  Chifukwa nsanja yokhala ndi mpanda wolimba yasiyidwa.Mzinda waphokoso wasiyidwa.+ Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka chipululu mpaka kalekale.Zasanduka malo amene abulu amʼtchire akusangalalako,Komanso malo odyetserako ziweto,+ 15  Mpaka mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+Ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso,Komanso munda wa zipatsowo utayamba kuoneka ngati nkhalango.+ 16  Zikadzatero, mʼchipululumo mudzakhala chilungamo,Ndipo mʼmunda wa zipatsowo mudzakhalanso chilungamo.+ 17  Zotsatira za chilungamo chenicheni zidzakhala mtendere,+Ndipo chilungamo chenicheni chidzabweretsa bata komanso chitetezo chosatha.+ 18  Anthu anga adzakhala pamalo amtendere,Adzakhala pamalo otetezeka komanso pamalo abata ndi ampumulo.+ 19  Koma matalala adzawononga nkhalango yonse,Ndipo mzinda wonse udzasalazidwa. 20  Osangalala ndinu amene mukudzala mbewu mʼmphepete mwa madzi onse,Amene mukumasula ngʼombe yamphongo ndi bulu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo othawirapo.”
Kapena kuti, “kuti achite zinthu zosayenera.”