Yesaya 33:1-24
33 Tsoka kwa iwe amene umawononga ena koma iwe sunawonongedwe,+Iwe amene umachitira ena zachinyengo pamene iwe sunachitiridwe zachinyengo.
Ukadzangomaliza kuwononga ena, iwenso udzawonongedwa.+
Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwenso udzachitiridwa zachinyengo.
2 Inu Yehova, tikomereni mtima.+
Chiyembekezo chathu chili pa inu.
Tilimbitseni ndi dzanja lanu+ mʼmawa uliwonse.Mukhale chipulumutso chathu pa nthawi yamavuto.+
3 Mitundu ya anthu yathawa itamva phokoso lalikulu.
Inu mukanyamuka, mitundu ya anthu imamwazikana.+
4 Mofanana ndi dzombe lanjala limene limawononga chilichonse, zinthu zimene inu munalanda anthu ena zidzalandidwaAnthu adzathamanga ngati chigulu cha dzombe kudzazitenga.
5 Yehova adzakwezedwa,Chifukwa amakhala pamalo apamwamba.
Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.
6 Mʼmasiku anu, iye adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.Chimene amaona kuti ndi chamtengo wapataliNdi chipulumutso chake chachikulu,+ nzeru, kudziwa zinthu komanso kuopa Yehova.+
7 Taonani! Anthu awo otchuka akulira mofuula mʼmisewu.Amithenga amtendere akulira mopwetekedwa mtima.
8 Mʼmisewu ikuluikulu mulibe aliyense.Palibe munthu aliyense amene akuyenda mʼnjira.
Iye* waphwanya pangano,Wakana mizindaNdipo sakusamala za munthu aliyense.+
9 Dzikolo likulira* ndipo lafota.
Lebanoni wachita manyazi+ ndipo wawola.
Sharoni wakhala ngati chipululuNdipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+
10 Yehova wanena kuti: “Tsopano ndinyamuka,Tsopano ndidzikweza.+Tsopano ndidziika pamwamba.
11 Munali ndi pakati pa udzu wouma ndipo mwabereka mapesi.
Mzimu wanu udzakupserezani ngati moto.+
12 Mitundu ya anthu idzakhala ngati zinthu zimene zimatsalira laimu akawotchedwa.
Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa.+
13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita.
Ndipo inu amene muli pafupi, vomerezani kuti ndine wamphamvu.
14 Anthu ochimwa mu Ziyoni akuchita mantha.+Anthu ampatuko akunjenjemera kwambiri. Akufunsa kuti:
‘Ndi ndani wa ife amene angakhale pamene pali moto wowononga?+
Ndi ndani wa ife amene angakhale pafupi ndi moto umene sungazimitsike?’
15 Ndi amene amayenda mʼchilungamo nthawi zonse,+Amene amalankhula zoona,+Amene amakana kupeza phindu pochita zinthu mosaona mtima komanso mwachinyengo,Amene manja ake amakana chiphuphu, mʼmalo mochilandira,+Amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi,Ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zinthu zoipa.
16 Iye adzakhala pamalo okwera.Malo ake othawirako otetezeka* adzakhala mʼmatanthwe movuta kufikamo.Iye adzapatsidwa chakudyaNdipo madzi ake sadzatha.”+
17 Maso ako adzaona ulemerero wa mfumu.Adzaona dziko lakutali.
18 Mumtima mwako udzaganizira mozama za chinthu choopsa kuti:
“Kodi mlembi ali kuti?
Kodi ali kuti amene ankapereka msonkho uja?+
Kodi amene ankawerenga nsanja uja ali kuti?”
19 Anthu achipongwe simudzawaonanso,Anthu amene chilankhulo chawo nʼchovuta kumva,*Anthu achibwibwi amene simungamvetse zimene akulankhula.+
20 Taonani Ziyoni, mzinda umene timachitiramo zikondwerero zathu.+
Maso anu adzaona kuti Yerusalemu ndi malo okhalamo abata,Tenti imene sidzachotsedwa.+
Zikhomo zake sizidzazulidwaNdipo zingwe zake sizidzadulidwa.
21 Koma kumeneko, Yehova WolemekezekaAdzakhala malo a mitsinje ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife.Malo amene sitima zankhondo sizidzapitakoKomanso amene sitima zikuluzikulu sizidzadutsako.
22 Chifukwa Yehova ndi Woweruza wathu,+Yehova ndi Wotipatsa Malamulo,+Yehova ndi Mfumu yathu.+Iye ndi amene adzatipulumutse.+
23 Zingwe zanu zidzakhala zosamanga.Sizidzalimbitsa mtengo wautali wapasitima kapena kutambasula chinsalu chake.
Pa nthawi imeneyo adzagawana zinthu zambirimbiri zimene analanda adani awo.Ngakhale anthu olumala adzatenga katundu wambiri amene alanda adani awo.+
24 Ndipo palibe munthu wokhala mʼdzikolo amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala.”+
Anthu okhala mʼdzikolo adzakhululukidwa machimo awo.+