Yesaya 36:1-22

  • Senakeribu anapita kukachita nkhondo ndi Yuda (1-3)

  • Rabisake ananyoza Yehova (4-22)

36  Mʼchaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri+ anabwera kudzaukira mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.+  Kenako mfumu ya Asuri inatumiza Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali. Iwo anakaima pafupi ndi ngalande yochokera kudziwe lakumtunda,+ limene lili pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+  Kenako Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyangʼanira banja lachifumu, Sebina+ mlembi ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kukakumana naye.  Choncho Rabisake anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+  Iwe ukunena kuti, ‘Ine ndili ndi pulani komanso mphamvu zoti zindithandize pankhondo.’ Koma zimenezi nʼzabodza. Kodi ukudalira ndani kuti undipandukire?+  Ukudalira thandizo la Iguputo, bango lophwanyika loti munthu ataligwira kuti alitsamire, lingamucheke mʼmanja. Ndi mmene zilili ndi Farao mfumu ya Iguputo kwa onse omudalira.+  Ngati mungandiuze kuti, ‘Tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi iyeyo si amene Hezekiya wamuchotsera malo ake okwezeka ndi maguwa ake ansembe+ nʼkuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada patsogolo pa guwa lansembe iliʼ?”’+  Ndiye ubetcherane ndi mbuye wanga, mfumu ya Asuri+ ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti tione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.  Kodi ungathe bwanji kuthamangitsa bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga, pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta ndi okwera pamahatchi? 10  Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza kuti, ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo ndipo ukaliwononge.’” 11  Atamva zimenezi, Eliyakimu, Sebina+ ndi Yowa anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu mʼchilankhulo cha Chiaramu*+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe mʼchilankhulo cha Ayuda, kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 12  Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti uthengawu ndidzauze mbuye wanu ndi inuyo basi? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, amene adzadye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi ndi inuyo?” 13  Kenako Rabisake anaimirira nʼkulankhula mokweza mʼchilankhulo cha Ayuda+ kuti: “Imvani mawu a mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri.+ 14  Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akupusitseni, chifukwa sangathe kukupulumutsani.+ 15  Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Ndithu Yehova atipulumutsa ndipo mzindawu superekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.” 16  Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Tiyeni tigwirizane zamtendere ndipo ingonenani kuti mwagonja. Mukatero, aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu komanso azimwa madzi apachitsime chake, 17  mpaka ine nditabwera kudzakutengani nʼkupita nanu kudziko lofanana ndi lanulo,+ dziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate ndi minda ya mpesa. 18  Musalole kuti Hezekiya akupusitseni ponena kuti, ‘Yehova atipulumutsa.’ Kodi pali mulungu aliyense amene wakwanitsa kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwa mfumu ya Asuri?+ 19  Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi+ ili kuti? Nanga milungu ya Sefaravaimu+ ili kuti? Kodi yapulumutsa Samariya mʼmanja mwanga?+ 20  Ndi mulungu uti pa milungu yonse ya mayiko amenewa, amene wapulumutsa dziko lake mʼmanja mwanga, kuti Yehova athe kupulumutsa Yerusalemu mʼmanja mwanga?”’”+ 21  Koma anthuwo anangokhala chete, osamuyankha chilichonse, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musakamuyankhe.”+ 22  Ndiyeno Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira banja lachifumu,* Sebina+ mlembi ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuuza zomwe Rabisake ananena.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “mkulu wa operekera zakumwa.”
Kapena kuti, “mʼchilankhulo cha Asiriya.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”