Yesaya 38:1-22

  • Kudwala kwa Hezekiya komanso kuchira kwake (1-22)

    • Nyimbo yosonyeza kuyamikira (10-20)

38  Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa.+ Ndiyeno mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anapita kukamuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita, chifukwa iweyo ufa ndithu, suchira.’”+  Hezekiya atamva zimenezi, anatembenukira kukhoma nʼkuyamba kupemphera kwa Yehova kuti:  “Yehova ndikukupemphani kuti chonde, mukumbukire+ kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse+ komanso ndachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yesaya kuti:  “Bwerera kwa Hezekiya+ ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa moyo wako,*+  ndipo ndidzapulumutsa iweyo ndi mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Asuri komanso ndidzateteza mzinda uno.+  Chizindikiro chochokera kwa Yehova chosonyeza kuti Yehova adzakwaniritsadi mawu ake,+ ndi ichi:  Ndichititsa kuti mthunzi wa dzuwa umene wadutsa kale pamasitepe* a Ahazi, ubwerere mʼmbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera mʼmbuyo masitepe 10 pamasitepe amene linali litadutsa kale.  Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala nʼkuchira, analemba zotsatirazi. 10  Ine ndinati: “Pakatikati pa moyo wangaNdidzalowa pamageti a Manda.* Zaka zotsala za moyo wanga zidzachotsedwa.” 11  Ndinanena kuti: “Sindidzamuona Ya,* Ya sindidzamuonanso mʼdziko la amoyo.+ Anthu sindidzawaonansoNdikadzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo. 12  Malo anga okhala azulidwa ndi kuchotsedwa kwa ine+Ngati tenti ya abusa. Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu.Mwadula moyo wanga ngati ulusi wa nsalu. Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+ 13  Ndadzitonthoza mpaka mʼmawa. Mofanana ndi mkango, iye akungokhalira kuphwanya mafupa anga onse.Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+ 14  Ndikungokhalira kulira ngati namzeze kapena kamwana ka mbalame.+Ndikungokhalira kubuula ngati njiwa.+ Ndatopa ndi kudikirira thandizo kuchokera kumwamba.+ Choncho ndinati: ‘Inu Yehova ine ndapanikizika kwambiri.Chonde ndithandizeni.’+ 15  Kodi ndinene kuti chiyani? Iye walankhula ndi ine ndipo wachitapo kanthu. Ndidzayenda modzichepetsa zaka zonse za moyo wangaChifukwa cha kupweteka kwa mtima wanga.* 16  ‘Inu Yehova, munthu aliyense amakhala ndi moyo chifukwa cha zinthu zimenezi,*Ndipo mʼzinthu zimenezi, mzimu wanga umapezamo moyo. Inu mudzabwezeretsa thanzi langa nʼkundithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.+ 17  Mʼmalo mopeza mtendere ndinali ndi chisoni chachikulu.Koma chifukwa chakuti mumandikonda kwambiri,Munanditeteza kuti ndisapite kudzenje lachiwonongeko.+ Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.*+ 18  Chifukwa Manda* sangakupatseni ulemerero,+Imfa singakutamandeni.+ Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kuti muwasonyeze kukhulupirika kwanu.+ 19  Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero. Bambo akhoza kuphunzitsa ana ake za kukhulupirika kwanu.+ 20  Inu Yehova, ndipulumutseni,Ndipo ine ndi anthu ena tidzaimba nyimbo zanga ndi zoimbira za zingwe+Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+ 21  Kenako Yesaya anati: “Bweretsani keke ya nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo muziike pachotupa chimene ali nacho kuti achire.”+ 22  Hezekiya anali atafunsa kuti: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova nʼchiyani?”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ako.”
Nʼkutheka kuti masitepe amenewa ankawagwiritsa ntchito ngati chipangizo chodziwira nthawi.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “kupwetekedwa moyo.”
Kutanthauza mawu a Mulungu ndi zochita zake.
Kapena kuti, “Mwachotsa machimo anga onse kuti musawaonenso.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.