Yesaya 39:1-8

  • Amithenga ochokera ku Babulo (1-8)

39  Pa nthawi imeneyo, Merodaki-baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babulo, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya+ chifukwa anamva kuti amadwala ndipo wachira.+  Hezekiya analandira anthuwo mwansangala* ndipo anawaonetsa nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu, mafuta ena amtengo wapatali, nyumba yake yosungiramo zida zonse zankhondo ndiponso chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse mʼnyumba* yake ndi mu ufumu wake wonse.  Kenako mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya nʼkuifunsa kuti: “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, nanga anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+  Atatero Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani mʼnyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili mʼnyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”  Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imva zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena,  ‘Tamvera, masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili mʼnyumba mwako ndiponso zonse zimene makolo ako akhala akusunga mpaka lero, anthu adzazitenga nʼkupita nazo ku Babulo. Palibe chidzatsale,’+ watero Yehova.+  ‘Ena mwa ana ako, amene iweyo udzabereke, adzatengedwa ndipo adzakhala nduna zapanyumba ya mfumu ya ku Babulo.’”+  Hezekiya atamva zimenezi anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwanenawa ndi abwino.” Anapitiriza kuti: “Chifukwa mʼmasiku anga mukhala bata* ndi mtendere.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anasangalala.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “choonadi.”