Yesaya 4:1-6

  • Akazi 7 mwamuna mmodzi (1)

  • Chinthu chimene Yehova adzachiphukitse chidzakhala chaulemerero (2-6)

4  Tsiku limenelo, akazi 7 adzagwira mwamuna mmodzi+ nʼkumuuza kuti: “Ife tizidya chakudya chathuNdipo tizidzipezera tokha zovala.Inuyo mungotilola kuti tizitchedwa ndi dzina lanuKuti tichotse kunyozeka kwathu.”*+ 2  Tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse chidzakhala chokongola komanso chaulemerero. Zipatso za mʼdzikolo zidzakhala zonyaditsa ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+ 3  Aliyense amene adzatsale mu Ziyoni ndiponso amene adzasiyidwe mu Yerusalemu adzatchedwa woyera, anthu onse a mu Yerusalemu amene analembedwa mayina kuti akhale ndi moyo.+ 4  Yehova akadzatsuka nyansi* za ana aakazi a Ziyoni+ ndiponso akadzatsuka magazi amene Yerusalemu anakhetsa, pogwiritsa ntchito mzimu wa chiweruzo komanso mzimu woyaka moto,+ 5  malo onse a paphiri la Ziyoni ndi malo onse a mu Yerusalemu ochitirapo misonkhano, Yehova adzawapangira mtambo ndi utsi kuti ziziwathandiza masana. Adzawapangiranso moto wowala walawilawi kuti uziwathandiza usiku,+ ndipo pamwamba pa malo onse aulemererowo padzakhala chotchinga. 6  Padzakhalanso msasa kuti uzipereka mthunzi woteteza ku dzuwa masana,+ ndiponso kuti ukhale malo othawirapo komanso achitetezo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mvula.+

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi manyazi omwe munthu amakhala nawo chifukwa choti sanakwatiwe komanso alibe ana.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndowe.”