Yesaya 43:1-28

  • Yehova akusonkhanitsanso anthu ake (1-7)

  • Milungu ikuyesedwa (8-13)

    • “Inu ndinu mboni zanga” (10, 12)

  • Kumasulidwa kuchoka ku Babulo (14-21)

  • “Tiye tiimbane mlandu” (22-28)

43  Tsopano izi ndi zimene Yehova wanena,Mlengi wako iwe Yakobo, amene anakupanga iwe Isiraeli.+ Iye wanena kuti: “Usachite mantha, chifukwa ine ndakuwombola.+ Ndakuitana pokutchula dzina lako. Iwe ndiwe wanga.   Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe.+Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakukokolola.+ Ukamadzayenda pamoto sudzapsaNdipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.   Chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wako,Woyera wa Isiraeli, Mpulumutsi wako. Ndapereka Iguputo kuti akhale dipo* lako.Ndaperekanso Itiyopiya ndi Seba mʼmalo mwa iwe.   Chifukwa ndinayamba kukuona kuti ndiwe wamtengo wapatali,+Unalemekezedwa ndipo ndimakukonda.+ Choncho ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iweKomanso mitundu ya anthu posinthanitsa ndi moyo wako.   Usachite mantha chifukwa ine ndili ndi iwe.+ Ndidzabweretsa mbadwa* zako kuchokera kumʼmawa,Ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumadzulo.+   Ndidzauza kumpoto kuti, ‘Abwezere kwawo!’+ Ndipo ndidzauza kumʼmwera kuti, ‘Usawakanize. Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali komanso ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+   Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+Ndiponso amene ndinamulenga kuti ndipatsidwe ulemerero,Amene ndinamuumba komanso kumupanga.’+   Bweretsa anthu amene saona ngakhale kuti ali ndi maso,Ndiponso anthu osamva ngakhale kuti ali ndi makutu.+   Mitundu yonse isonkhane pamalo amodzi,Ndipo mitundu ya anthu isonkhanitsidwe pamodzi.+ Ndi ndani pakati pa milungu yawo amene ananena kuti zinthu zimenezi zidzachitika? Kapena kodi angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+ Abweretse mboni zawo kuti tidziwe ngati akunena zoona,Kapena mbonizo zimvetsere nʼkunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+ 10  “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova,“Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha,+Kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira,*Komanso kuti mumvetse kuti ine sindimasintha.+ Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,Ndipo pambuyo panga palibenso wina.+ 11  Ine ndine Yehova.+ Palibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.”+ 12  “Ine ndi amene ndinanena zimene zidzachitike, amene ndinakupulumutsani komanso amene ndinachititsa kuti zimenezi zidziwike,Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo.+ Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+ 13  “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+Ndipo palibe amene angathe kulanda chinthu chilichonse mʼdzanja langa.+ Ndikachita chinthu, ndi ndani amene angaletse?”+ 14  Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Chifukwa cha inu, ndidzatumiza asilikali ku Babulo ndipo adzagwetsa zotsekera mʼmageti,+Komanso Akasidi adzalira chifukwa chopanikizika, ali mʼsitima zawo zapamadzi.+ 15  Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+ 16  Izi nʼzimene Yehova wanena,Yemwe amapanga msewu panyanjaKomanso njira ngakhale pamadzi osefukira,+ 17  Amene amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi,+Gulu lankhondo pamodzi ndi asilikali amphamvu, wanena kuti: “Iwo adzagona pansi ndipo sadzadzukanso.+ Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.” 18  “Musakumbukire zinthu zakale,Ndipo musamangoganizira zinthu zakumbuyo. 19  Taonani! Ndikupanga chinthu chatsopano.+Ngakhale panopa chikuonekera. Kodi simukuchizindikira? Ndidzapanga njira mʼchipululu,+Ndipo mitsinje idzadutsa mʼchipululumo.+ 20  Zilombo zakutchire zidzandilemekeza,Komanso mimbulu ndi nthiwatiwa,Chifukwa ndimapereka madzi,Ndiponso mitsinje mʼchipululu,+Kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe, 21  Ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga,Alengeze za ulemerero wanga.+ 22  Koma iwe Yakobo sunapemphe thandizo kwa ine+Chifukwa chakuti watopa nane, iwe Isiraeli.+ 23  Iwe sunandibweretsere nkhosa kuti zikhale nsembe zako zopsereza zathunthuKapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Ine sindinakukakamize kuti undibweretsere mphatso,Ndipo sindinakutopetse pokulamula kuti undipatse lubani.*+ 24  Iwe sunandigulire bango lonunkhira* ndi ndalama zako,Ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+ Mʼmalomwake, wanditopetsa ndi machimo akoNdipo wandilemetsa ndi zolakwa zako.+ 25  Ineyo ndi amene ndikufafaniza zolakwa zako*+ chifukwa cha dzina langa,+Ndipo machimo ako sindidzawakumbukira.+ 26  Ndikumbutse, tiye tiimbane mlandu.Fotokoza mbali yako kuti usonyeze kuti ndiwe wosalakwa. 27  Kholo lanu loyambirira linachimwa,Ndipo anthu okulankhulirani* andipandukira.+ 28  Choncho ndidzadetsa akalonga apamalo oyera,Ndidzachititsa kuti Yakobo awonongedweNdipo ndidzachititsa kuti Isiraeli amunenere mawu onyoza.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “kundidalira.”
Chimenechi ndi chomera chonunkhira. Mtundu weniweni wa chomerachi sukudziwika.
Kapena kuti, “zochita zako zondipandukira.”
Nʼkutheka kuti akunena aphunzitsi a Chilamulo.