Yesaya 44:1-28
44 “Tsopano mvetsera, iwe Yakobo mtumiki wanga,Ndi iwe Isiraeli amene ndakusankha.+
2 Yehova, amene anakupanga+Ndiponso amene anakuumba,Amene wakhala akukuthandiza kuyambira uli mʼmimba,* wanena kuti:
‘Usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo,+Ndiponso iwe Yesuruni,*+ amene ndakusankha.
3 Chifukwa ndidzapatsa madzi munthu waludzu*+Ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi oyenda pamalo ouma.
Ndidzatsanulira mzimu wanga pa ana ako*+Komanso madalitso anga pa mbadwa zako.
4 Iwo adzaphuka ngati udzu wobiriwira,+Ndiponso ngati mitengo ya msondodzi mʼmphepete mwa mitsinje yamadzi.
5 Munthu adzati: “Ine ndine wa Yehova.”+
Wina adzadzipatsa dzina la Yakobo,Winanso adzalemba padzanja lake kuti: “Ndine wa Yehova.”
Ndipo adzatenga dzina la Isiraeli.’
6 Yehova, Mfumu ya Isiraeli,+ amene anawawombola,+Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, wanena kuti:
‘Ine ndine woyamba ndi womaliza.+
Ndipo palibenso Mulungu wina kupatulapo ine.+
7 Kodi ndi ndani amene angafanane ndi ine?+
Ayankhe molimba mtima ndi kupereka umboni wake kwa ine.+
Kuyambira nthawi imene ndinakhazikitsa anthu akalekale,Iwo anene zinthu zimene zichitike posachedwapaNdi zimene zidzachitike mʼtsogolo.
8 Musachite mantha,Ndipo musathedwe nzeru chifukwa cha mantha.+
Kodi sindinauziretu aliyense wa inu ndi kulengeza zimenezi?
Inu ndinu mboni zanga.+
Kodi palinso Mulungu wina kupatulapo ine?
Ayi, palibe Thanthwe lina.+ Palibe lina limene ndikulidziwa.’”
9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,Ndipo mafano awo amene amawanyadira ndi opanda phindu.+
Mofanana ndi mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+Choncho anthu amene anawapanga adzachititsidwa manyazi.+
10 Kodi pali aliyense wopusa amene angafike popanga mulungu kapena fano lopangidwa ndi chitsulo chosungunula,*Lomwe ndi lopanda phindu?+
11 Anzake onse adzachititsidwa manyazi,+
Amisiriwo ndi anthu basi.
Onsewo asonkhane pamodzi ndipo akhale pamalo awo.
Adzachita mantha ndipo onsewo adzachititsidwa manyazi.
12 Munthu wosula zitsulo akugwiritsa ntchito chida chake posula chitsulo chimene wachiwotcha pamoto wamakala.
Akuchiwongola ndi hamala,Akuchisula ndi dzanja lake lamphamvu.+
Kenako wamva njala ndipo mphamvu zake zatha.Sanamwe madzi ndipo watopa.
13 Mmisiri wosema mtengo watambasula chingwe choyezera. Walemba mtengowo ndi choko chofiira.
Wausema ndi sompho* ndipo waulemberera ndi chipangizo cholembera mizere yozungulira.
Waupanga kuti uzioneka ngati munthu,+Waukongoletsa ngati munthu,Kuti uzikhala mʼnyumba.*+
14 Pali munthu amene ntchito yake ndi yogwetsa mitengo ya mkungudza.
Iye amasankha mtengo wamtundu winawake, mtengo waukulu kwambiri,Ndipo amausiya kuti ukule nʼkukhwima pakati pa mitengo yamʼnkhalango.+
Iye amadzala mtengo wa paini ndipo mvula imaukulitsa.
15 Kenako mtengowo umakhala nkhuni zoti munthu akolezere moto.
Amatenga mbali ina ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha.Amayatsa moto nʼkuphikapo mkate.
Koma amasemanso mulungu nʼkumamulambira.
Mtengowo amaupanga chifaniziro chosema ndipo amachigwadira.+
16 Hafu ya mtengowo waiwotcha pamoto.Mtengo umene wauwotcha pamotowo wawotchera nyama imene wadya ndipo wakhuta.
Wawothanso moto wake ndipo wanena kuti:
“Eya! Ndamva kutenthera. Ndaona kuwala kwa moto.”
17 Koma mtengo wotsalawo wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake chosema.
Akuchiweramira komanso kuchilambira.
Akupemphera kwa chifanizirocho kuti:
“Ndipulumutseni, chifukwa ndinu mulungu wanga.”+
18 Iwo sadziwa kanthu ndipo palibe chimene amamvetsa,+Chifukwa maso awo ndi otseka ndipo sangaone,Ndipo mitima yawo sizindikira zinthu.
19 Palibe amene amaganiza mumtima mwakeKapena amene akudziwa zinthu, kapenanso amene amamvetsa zinthu kuti adzifunse kuti:
“Hafu ya mtengowu ndasonkhera moto,Ndipo pamakala ake ndaphikapo mkate komanso ndawotcha nyama nʼkudya.
Ndiye kodi wotsalawu ndipangire chinthu chonyansa?+
Kodi zoona ndilambire chinthu chopangidwa ndi mtengo?”*
20 Iye akudya phulusa.
Mtima wake umene wapusitsidwa wamusocheretsa.
Iye sangathe kudzipulumutsa kapena kunena kuti:
“Kodi chinthu chimene chili mʼdzanja langa lamanjachi si chabodza?”
21 “Kumbukira zinthu zimenezi iwe Yakobo ndiponso iwe Isiraeli,Chifukwa ndiwe mtumiki wanga.
Ine ndinakupanga ndipo iweyo ndiwe mtumiki wanga.+
Iwe Isiraeli, ine sindidzakuiwala.+
22 Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo+Ndipo machimo ako adzakhala ngati ndawaphimba ndi mtambo waukulu.
Bwerera kwa ine, ndipo ine ndidzakuwombola.+
23 Fuulani mosangalala kumwamba inu,Chifukwa Yehova wachita zimenezi.
Fuulani posonyeza kupambana, inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.
Mapiri inu, fuulani mosangalala,+Iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse imene ili mmenemo,
Chifukwa Yehova wawombola Yakobo,Ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+
24 Yehova, Wokuwombola+Ndiponso amene anakuumba kuyambira uli mʼmimba, wanena kuti:
“Ine ndine Yehova amene ndinapanga chilichonse.
Ndinatambasula ndekha kumwamba,+Ndipo ndinayala dziko lapansi.+
Kodi ndi ndani amene anali ndi ine?
25 Ndimalepheretsa zizindikiro za anthu olankhula zinthu zopanda pake,*Ndipo ndine amene ndimachititsa olosera kuti azichita zinthu ngati anthu opusa.+Ndine amene ndimasokoneza anthu anzeruNdiponso amene ndimachititsa kuti nzeru zawo zikhale zopusa.+
26 Ndine amene ndimachititsa mawu a mtumiki wanga kuti akwaniritsidweNdiponso amene ndimakwaniritsa mawu onse amene amithenga anga analosera.+Ndine amene ndikunena za Yerusalemu kuti, ‘Muzidzakhala anthu.’+
Ndikunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti, ‘Idzamangidwanso,+Ndipo ndidzakonza malo ake amene anawonongedwa.’+
27 Ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, ‘IphwaNdipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.’+
28 Ndine amene ndikunena za Koresi+ kuti, ‘Iye ndi mʼbusa wanga,Ndipo adzakwaniritsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,’+Amene ndanena zokhudza Yerusalemu kuti, ‘Adzamangidwanso,’
Ndiponso zokhudza kachisi kuti, ‘Maziko ako adzamangidwa.’”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kuyambira usanabadwe.”
^ Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
^ Kapena kuti, “dziko laludzu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”
^ Kapena kuti, “kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”
^ Kapena kuti, “mʼkachisi.”
^ Ena amati kasemasema.
^ Kapena kuti, “mtengo woumawu?”
^ Kapena kuti, “za aneneri abodza.”