Yesaya 46:1-13

  • Mafano a Ababulo sangafanane ndi Mulungu wa Isiraeli (1-13)

    • Yehova amaneneratu zamʼtsogolo (10)

    • Mbalame yodya nyama yochokera kotulukira dzuwa (11)

46  Beli wawerama+ ndipo Nebo wagwada. Mafano awo anyamulidwa ndi nyama, nyama zonyamula katundu.+Mafanowo ali ngati katundu wolemera kwa nyama zotopa.  2  Milungu imeneyi imawerama komanso kugwada pa nthawi imodzi.Singapulumutse katunduyo,*Ndipo nayonso imatengedwa kupita ku ukapolo.  3  “Inu anyumba ya Yakobo ndimvetsereni, komanso inu nonse otsala a mʼnyumba ya Isiraeli,+Inu amene ndakuthandizani kuyambira pamene munabadwa ndiponso kukunyamulani kuyambira pamene munatuluka mʼmimba.+  4  Ngakhale mudzakalambe, ine ndidzakhala chimodzimodzi.+Ngakhale tsitsi lanu lidzachite imvi, ine ndidzapitiriza kukunyamulani. Ndidzakunyamulani, kukuthandizani komanso kukupulumutsani ngati mmene ndakhala ndikuchitira.+  5  Kodi mungandifananitse kapena kundiyerekezera ndi ndani?+Kodi munganene kuti ndine wofanana ndi ndani?+  6  Pali anthu amene amakhuthula golide mʼzikwama zawo.Amayeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kumuweramira ndi kumulambira.*+  7  Iwo amamunyamula pamapewa awo.+Amamutenga nʼkukamuika pamalo ake ndipo mulunguyo amangoima pomwepo. Sasuntha pamene amuikapo.+ Anthuwo amamuitana mofuula, koma sayankha.Sangapulumutse munthu amene ali pamavuto.+  8  Kumbukirani zimenezi ndipo mulimbe mtima. Muziganizire mumtima mwanu, anthu ochimwa inu.  9  Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,Kuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina. Ine ndine Mulungu ndipo palibe aliyense wofanana ndi ine.+ 10  Kutatsala nthawi yaitali, ndimaneneratu zimene zidzachitike,Ndipo kale kwambiri ndinaneneratu zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo.+ Ine ndimanena kuti, ‘Zolinga zanga zidzachitikadi,+Ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+ 11  Ine ndikuitana mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa,*+Ndikuitana munthu kuchokera kudziko lakutali kuti adzachite zolinga zanga.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita. Ndakonza kuti zimenezi zichitike komanso ndidzazichita.+ 12  Ndimvereni inu anthu osamva,*Inu amene muli kutali ndi chilungamo. 13  Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.Chilungamocho sichili kutali,Ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+ Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzamʼpatsa ulemerero wanga.”+

Mawu a M'munsi

Katundu ameneyu ndi mafano amene anyamulitsa nyama.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumugwadira.”
Kapena kuti, “kumʼmawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “a mtima wamphamvu.”