Yesaya 47:1-15

  • Kugwa kwa Babulo (1-15)

    • Anthu okhulupirira nyenyezi ndi osathandiza (13-15)

47  Tsika ukhale pafumbiIwe namwali, mwana wamkazi wa Babulo.*+ Ukhale padothi pomwe palibe mpando wachifumu,+Iwe mwana wamkazi wa Akasidi,Chifukwa anthu sadzakutchulanso kuti ndiwe wolekereredwa ndiponso wosasatitsidwa.  2  Tenga mphero upere ufa. Vula nsalu yako yophimba kumutu. Vula chovala chako ndipo miyendo yako ionekere. Uwoloke mitsinje.  3  Anthu adzaona maliseche ako. Manyazi ako adzaonekera. Ine ndidzabwezera+ ndipo palibe amene adzanditsekereze.*  4  “Amene akutiwombolaDzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.Iye ndi Woyera wa Isiraeli.”+  5  Iwe mwana wamkazi wa Akasidi,+Khala pansi mwakachetechete ndipo ulowe mumdima.Anthu sadzakutchulanso kuti Dona* wa Maufumu.+  6  Ine ndinakwiyira anthu anga.+ Ndinalola kuti cholowa changa chidetsedwe+Ndipo ndinawapereka mʼmanja mwako.+ Koma iwe sunawachitire chifundo.+ Ngakhale munthu wokalamba unamusenzetsa goli lolemera kwambiri.+  7  Iwe unanena kuti: “Nthawi zonse ine ndidzakhala Dona* mpaka kalekale.”+ Sunaganizire zinthu zimenezi mumtima mwako.Sunaganizire kuti zidzatha bwanji.  8  Tsopano imva izi, iwe amene umakonda zosangalatsa,+Amene umakhala motetezeka, iwe amene umanena mumtima mwako kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.+ Sindidzakhala wamasiye Ndipo ana anga sadzafa.”+  9  Koma zinthu ziwiri izi zidzakugwera modzidzimutsa tsiku limodzi:+ Ana ako adzafa ndiponso udzakhala wamasiye. Zinthu zonsezi zidzakugwera ndithu,+Chifukwa* wachita zanyanga zochuluka komanso chifukwa cha zamatsenga zako zonse zamphamvu.+ 10  Iwe unkadalira zoipa zimene unkachita. Unkanena kuti: “Palibe amene akundiona.” Nzeru zako komanso kudziwa zinthu ndi zimene zinakusocheretsa,Ndipo mumtima mwako umanena kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.” 11  Koma tsoka lidzakugweraNdipo matsenga ako onse sadzatha kuliletsa.* Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwapewa. Chiwonongeko chimene sunkachiyembekezera chidzakupeza modzidzimutsa.+ 12  Choncho pitiriza kuchita zanyanga komanso zamatsenga zako zambirimbirizo,+Zimene wazivutikira kuyambira uli mwana. Mwina zingakuthandize,Mwina zichititsa kuti anthu achite mantha. 13  Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu amene amalambira zinthu zakumwamba,* amene amayangʼanitsitsa nyenyezi,+Amene amakudziwitsa zimene zikuchitikireMwezi watsopano ukaoneka,Auze abwere adzakupulumutse. 14  Iwotu ali ngati mapesi. Moto udzawawotcha. Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya moto walawilawi. Moto umenewu suli ngati moto wamakala woti anthu nʼkumawotha,Si moto woti anthu nʼkuuyandikira. 15  Umu ndi mmene amatsenga ako adzakhalireAmene wakhala ukuvutikira nawo limodzi kuyambira uli mwana. Iwo adzabalalika, aliyense kulowera njira yake* Ndipo sipadzakhala aliyense woti akupulumutse.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mabaibulo ena amati, “amene ndidzamusonyeze chifundo.”
Kapena kuti, “Mfumukazi.”
Kapena kuti, “Mfumukazi.”
Mabaibulo ena amati, “Ngakhale.”
Kapena kuti, “Ndipo sudzatha kulichitira matsenga kuti lisakugwere.”
Mabaibulo ena amati, “Anthu okhulupirira nyenyezi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chigawo chake.”