Yesaya 50:1-11

  • Kuchimwa kwa Isiraeli kunayambitsa mavuto (1-3)

  • Mtumiki womvera wa Yehova (4-11)

    • Lilime ndi khutu la anthu ophunzitsidwa bwino (4)

50  Yehova wanena kuti: “Kodi kalata yothetsera ukwati+ wa mayi anu amene ndinawathamangitsa ili kuti? Kapena kodi ndakugulitsani kwa munthu uti amene ndinali naye ngongole? Inutu munagulitsidwa chifukwa cha zolakwa zanu,+Ndipo mayi anu anathamangitsidwa chifukwa cha machimo anu.+   Ndiye nʼchifukwa chiyani nditabwera sindinapeze aliyense? Nʼchifukwa chiyani nditaitana palibe amene anayankha?+ Kodi dzanja langa lafupika kwambiri moti silingathe kuwombola,Kapena kodi ine ndilibe mphamvu zopulumutsira?+ Inetu ndimaumitsa nyanja pongoidzudzula chabe.+Mitsinje ndimaisandutsa chipululu.+ Nsomba zake zimawola chifukwa chakuti mulibe madziNdipo zimafa chifukwa cha ludzu.   Kumwamba ndimakuveka mdima+Ndipo chiguduli ndimachisandutsa chophimba chake.”   Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino*+Kuti ndidziwe mmene ndingayankhire* munthu amene watopa, ndi mawu oyenera.+ Iye amandidzutsa mʼmawa uliwonse.Amandidzutsa kuti ndimvetsere* ngati mmene ophunzira amachitira.+   Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watsegula khutu langa,Ndipo ine sindinamupandukire.+ Sindinatembenukire kwina.+   Msana wanga ndinaupereka kwa anthu amene ankandimenyaNdipo masaya anga ndinawapereka kwa anthu amene ankandizula ndevu. Sindinabise nkhope yanga kuti asaichitire zinthu zochititsa manyazi komanso kuti asailavulire.+   Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza.+ Nʼchifukwa chake sindidzamva kuti ndanyozeka. Nʼchifukwa chake ndalimbitsa nkhope yanga ngati mwala wa nsangalabwi,+Ndipo ndikudziwa kuti sindidzachititsidwa manyazi.   Amene amanena kuti ndine wolungama ali pafupi. Ndi ndani angandiimbe* mlandu?+ Tiyeni tikaonane pabwalo lamilandu. Kodi ndi ndani amene akufuna kundiimba mlandu? Abwere pafupi ndi ine.   Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza. Ndi ndani amene adzanene kuti ndine wolakwa? Onse adzatha ngati chovala. Njenjete* idzawadya. 10  Ndi ndani pakati panu amene amaopa YehovaNdiponso kumvetsera mawu a mtumiki wake?+ Ndi ndani amene amayenda mumdima wandiweyani, popanda kuwala kulikonse? Iye akhulupirire dzina la Yehova ndipo adalire Mulungu wake. 11  “Inu nonse amene mukuyatsa moto,Amene mukuchititsa kuti uzithetheka,Yendani mʼkuwala kwa moto wanuwo,Pakati pa moto umene ukuthethekawo. Izi ndi zimene mudzalandire kuchokera mʼdzanja langa: Mudzagona pansi mukumva ululu woopsa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lilime lophunzitsidwa bwino.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amadzutsa khutu langa kuti limvetsere.”
Mabaibulo ena amati, “ndingalimbikitsire.”
Kapena kuti, “angalimbane nane pa.”
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.