Yesaya 52:1-15

  • Dzuka, iwe Ziyoni!! (1-12)

    • Mapazi a munthu amene akubweretsa uthenga wabwino ndi okongola (7)

    • Alonda a mu Ziyoni akufuula pamodzi (8)

    • Amene akunyamula ziwiya za Yehova ayenera kukhala oyera (11)

  • Mtumiki wa Yehova adzalemekezedwa (13-15)

    • Maonekedwe ake anasintha (14)

52  Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu+ iwe Ziyoni.+ Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Chifukwa munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa sadzabweranso mwa iwe.+  2  Iwe Yerusalemu dzuka, sansa fumbi ndipo ukhale pampando. Masula zingwe zimene zili mʼkhosi mwako, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* amene unagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina.+  3  Chifukwa Yehova wanena kuti: “Munagulitsidwa popanda ndalama iliyonse,+Ndipo mudzawomboledwa popandanso ndalama.”+  4  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Poyamba anthu anga anapita kukakhala ku Iguputo ngati alendo.+Kenako Asuri anawapondereza popanda chifukwa.  5  Tsopano kodi nditani pamenepa?” akutero Yehova. “Chifukwa anthu anga anatengedwa kwaulere. Amene ankawalamulira ankangokhalira kufuula posonyeza kuti apambana.+Tsiku lililonse ndinkaona kuti dzina langa silikulemekezedwa,”+ akutero Yehova.  6  “Pa chifukwa chimenecho anthu anga adzadziwa dzina langa.+Pa chifukwa chimenecho adzadziwa pa tsiku limenelo kuti ineyo ndi amene ndikulankhula. Ndithu ndi ineyo.”  7  Mapazi a munthu amene akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino ndi okongola kwambiri!+Munthu amene akulengeza za mtendere,+Amene akubweretsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino,Amene akulengeza za chipulumutso,Amene akuuza Ziyoni kuti: “Mulungu wako wakhala Mfumu.”+  8  Tamvera! Alonda ako akufuula. Onse akufuula pamodzi mosangalala,Chifukwa akuona bwinobwino pamene Yehova akusonkhanitsanso anthu okhala mu Ziyoni.  9  Inu mabwinja a mu Yerusalemu+ sangalalani, nonse pamodzi mufuule mosangalala,Chifukwa Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo wawombola Yerusalemu.+ 10  Yehova waika poyera dzanja lake loyera kuti mitundu yonse ione.+Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona zimene Mulungu wathu wachita potipulumutsa.*+ 11  Chokanimo, chokanimo, tulukani mmenemo,+ musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa!+ Chokani pakati pake!+ Khalani oyera,Inu amene mukunyamula ziwiya za Yehova.+ 12  Chifukwa simudzachoka mopanikizika,Ndipo simudzafunika kuthawa,Popeza Yehova azidzayenda patsogolo panu,+Ndipo Mulungu wa Isiraeli azidzalondera kumbuyo kwanu.+ 13  Taona! Mtumiki wanga+ azidzachita zinthu mwanzeru. Adzapatsidwa udindo wapamwambaAdzakwezedwa ndipo adzalemekezedwa kwambiri.+ 14  Panali anthu ambiri amene ankamuyangʼana modabwa,Chifukwa maonekedwe ake anali atasintha kwambiri kuposa a munthu wina aliyense,Ndipo kukongola kwa thupi lake kunali kutatha, sanalinso wokongola kuposa anthu, 15  Mofanana ndi zimenezi iye adzadabwitsa mitundu yambiri ya anthu.+ Mafumu akadzamuona adzatseka pakamwa pawo,*+Chifukwa iwo adzaona zimene sanauzidwepo,Ndipo adzaganizira zimene sanamvepo.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “wachita kuti tipambane.”
Kapena kuti, “adzasowa chonena.”