Yesaya 54:1-17

  • Ziyoni yemwe ndi wosabereka adzakhala ndi ana ambiri (1-17)

    • Yehova, mwamuna wa Ziyoni (5)

    • Ana a Ziyoni azidzaphunzitsidwa ndi Yehova (13)

    • Zida zoti zivulaze Ziyoni sizidzapambana (17)

54  “Fuula mosangalala iwe mkazi amene sunaberekepo mwana.+ Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ sangalala ndipo ufuule mosangalala.+Chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiriKuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”*+ akutero Yehova.  2  “Kulitsa tenti yako.+ Tambasula nsalu za chihema chako chachikulu. Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za tenti yakoNdipo ulimbitse zikhomo zake.+  3  Chifukwa mudzafalikira mbali yakumanja ndi kumanzere. Ana ako adzatenga mitundu ya anthu kukhala yawo,Ndipo adzakhala mʼmizinda imene inasiyidwa yabwinja.+  4  Usachite mantha,+ chifukwa sudzachititsidwa manyazi.+Usachite manyazi, chifukwa sudzakhumudwitsidwa. Iwe udzaiwala manyazi apaubwana wako,Ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako.  5  Chifukwa Wokupanga Wamkulu+ ali ngati mwamuna* wako,+Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Ndipo Woyera wa Isiraeli ndiye Wokuwombola.+ Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.+  6  Yehova anakuitana ngati kuti unali mkazi wosiyidwa komanso amene ali ndi chisoni,*+Ngati mkazi amene anakwatiwa ali mtsikana kenako nʼkusiyidwa,” akutero Mulungu wako.  7  “Ndinakusiya kwa kanthawi kochepa,Koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+  8  Chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+Koma chifukwa cha chikondi changa chokhulupirika chimene sichidzatha ndidzakuchitira chifundo,”+ akutero Yehova, Wokuwombola.+  9  “Kwa ine, zimenezi zili ngati masiku a Nowa.+ Monga mmene ndinalumbirira kuti madzi amʼnthawi ya Nowa sadzamizanso dziko lapansi,+Ndikulumbiranso kuti sindidzakukwiyira kapena kukudzudzula.+ 10  Mapiri akhoza kuchotsedwa,Ndipo zitunda zikhoza kugwedezeka,Koma chikondi changa chokhulupirika sichidzachotsedwa pa iwe,+Ndipo pangano langa lamtendere silidzagwedezeka,”+ akutero Yehova, amene akukuchitira chifundo.+ 11  “Iwe mkazi amene uli pamavuto,+ amene ukukankhidwa ndi mphepo yamkuntho ndiponso amene sunatonthozedwe,+Ine ndikukumanga ndi miyala komanso simenti yolimba,Ndipo ndikumanga maziko ako ndi miyala ya safiro.+ 12  Nsanja za mpanda wa mzinda wako ndidzazimanga ndi miyala ya rube,Mageti ako ndidzawamanga ndi miyala yonyezimira,*Ndipo mpanda wonse wa mzinda wako ndidzaumanga ndi miyala yamtengo wapatali. 13  Ana ako onse azidzaphunzitsidwa ndi Yehova,+Ndipo mtendere wa ana ako udzakhala wochuluka.+ 14  Udzakhazikika molimba mʼchilungamo.+ Palibe amene adzakupondereze,+Sudzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzakuchititse mantha,Chifukwa palibe chilichonse choopsa chimene chidzakuyandikire.+ 15  Ngati aliyense atakuukira,Sadzakhala kuti watumidwa ndi ine. Aliyense amene adzakuukire adzagwa chifukwa cha iwe.+ 16  Ine ndi amene ndinalenga mmisiri,Amene amauzira moto wamakalaNʼkupanga chida chankhondo ndi luso lake. Ine ndinalenganso munthu wowononga kuti aziwononga.+ 17  Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+Ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,Ndipo chilungamo chawo nʼchochokera kwa ine,” akutero Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ali ndi mbuye.”
Kapena kuti, “ali ngati mbuye.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wopwetekedwa mtima.”
Kapena kuti, “miyala yofiira ngati moto.”