Yesaya 56:1-12

  • Mlendo komanso munthu wofulidwa adzadalitsidwa (1-8)

    • Nyumba yopemphereramo anthu onse (7)

  • Alonda akhungu, agalu opanda mawu (9-12)

56  Yehova wanena kuti: “Tsatirani chilungamo+ ndipo chitani zolungama,Chifukwa chipulumutso changa chatsala pangʼono kubweraNdipo chilungamo changa chidzaonekera.+  2  Wosangalala ndi munthu amene amachita zimenezi,Ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,Amene amasunga Sabata ndipo salidetsa+Komanso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.  3  Mlendo amene wayamba kulambira Yehova+ asanene kuti,‘Ndithu Yehova adzandilekanitsa ndi anthu ake.’ Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, ‘Inetu ndine mtengo wouma.’” 4  Izi nʼzimene Yehova wanena kwa anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa. Amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo komanso amene amatsatira pangano langa:  5  “Mʼnyumba mwanga ndiponso mkati mwa mpanda wanga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso ndiponso dzina,Zomwe ndi zabwino kwambiri kuposa ana aamuna ndi aakazi. Ndidzawapatsa dzina limene lidzakhalapo mpaka kalekale,Dzina limene silidzatha.  6  Ndipo alendo amene abwera kwa Yehova kuti amutumikire,Kuti azikonda dzina la Yehova+Ndiponso kuti akhale atumiki ake,Onse amene amasunga Sabata ndipo salidetsaKomanso amene amatsatira pangano langa,  7  Nawonso ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+Ndipo ndidzawachititsa kuti asangalale mʼnyumba yanga yopemphereramo. Nsembe zawo zopsereza zathunthu ndi nsembe zawo zina ndidzazilandira paguwa langa lansembe. Chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+ 8  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ wanena kuti: “Ine ndidzamusonkhanitsira anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+  9  Inu nyama zonse zakutchire,Inu nyama zonse zamʼnkhalango,+ bwerani mudzadye. 10  Alonda ake ndi akhungu+ ndipo palibe amene akudziwa zimene zichitike.+ Onsewo ndi agalu opanda mawu ndipo satha kuuwa.+ Amangokhalira kupuma wefuwefu ndi kugona pansi. Amakonda kugona tulo. 11  Iwo ndi agalu adyera kwambiriNdipo sakhuta. Iwo ndi abusa osamvetsa zinthu.+ Onse apatukira kunjira yawo.Aliyense wa iwo akufunafuna njira yopezera phindu lachinyengo ndipo akunena kuti: 12  “Tabwerani! Dikirani ndikatenge vinyoNdipo timwe mpaka kuledzera.+ Mawa lidzakhalanso ngati lero, mwinanso kuposa pamenepa.”

Mawu a M'munsi