Yesaya 57:1-21

  • Wolungama komanso anthu okhulupirika awonongedwa (1, 2)

  • Uhule wauzimu wa Isiraeli waonekera (3-13)

  • Uthenga wotonthoza wopita kwa anthu onyozeka (14-21)

    • Anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde (20)

    • Oipa alibe mtendere (21)

57  Wolungama wawonongedwa,Koma palibe amene zikumukhudza. Anthu okhulupirika akufa,+Popanda wozindikira kuti munthu wolungama wafaChifukwa cha tsoka.*  2  Iye amalowa mumtendere. Onse amene amayenda mowongoka amapita kukapuma mʼmanda.*  3  “Koma inu bwerani pafupi,Inu ana a mayi wamatsenga,Inu ana a munthu wachigololo ndi hule:  4  Kodi mukumuseka ndani? Kodi mukuyasamulira ndani pakamwa panu ndi kumutulutsira lilime? Kodi inu si ana a machimo,Ana a chinyengo,+  5  Amene mukukhala ndi chilakolako champhamvu chogonana pakati pa mitengo ikuluikulu,+Pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+Kodi si inu amene mumapha ana mʼzigwa,*+Pakati pa matanthwe?  6  Gawo lako lili pamodzi ndi miyala yosalala yamʼchigwa.*+ Inde, gawo lako ndi limeneli. Ndipo umapereka nsembe zachakumwa, ndiponso mphatso kwa zinthu zimenezi.+ Kodi ine ndikhutire* ndi zinthu zimenezi?  7  Bedi lako unaliika pamwamba pa phiri lalitali ndi lokwezeka.+Ndipo unapita kumeneko kukapereka nsembe.+  8  Unaika chizindikiro chachikumbutso chako kuseri kwa chitseko ndi kuseri kwa felemu. Iwe unandisiya ndipo unavula.Unakwera mtunda nʼkukulitsa bedi lako. Ndipo unachita nawo pangano. Unkakonda kugona nawo pabedi lawo,+Ndipo unkayangʼanitsitsa chiwalo cha mwamuna.*  9  Iwe unatsetserekera kwa Meleki* utatenga mafuta,Ndiponso utatenga mafuta ochuluka onunkhira. Unatumiza nthumwi zako kutali kwambiri,Moti mpaka unatsikira mʼManda.* 10  Watopa chifukwa chotsatira njira zako zambiri,Koma sunanene kuti, ‘Nʼzopanda phindu!’ Unapeza mphamvu zina. Nʼchifukwa chake sunafooke.* 11  Kodi unkaopa komanso kuchita mantha ndi ndaniKuti uyambe kunama?+ Ine sunandikumbukire.+ Palibe chimene unaganizira mumtima mwako.+ Kodi si paja ine ndinakhala chete ndipo sindinachitepo kanthu pa zochita zako?+ Choncho iweyo sunkandiopa. 12  Ineyo ndidzanena za ‘chilungamoʼ chako+ ndi ntchito zako,+Ndipo sizidzakupindulira.+ 13  Ukamafuula popempha thandizo,Mafano amene unasonkhanitsa sadzakupulumutsa.+ Mphepo idzaulutsa mafano onsewoNdipo mpweya udzawakankhira kutali,Koma munthu amene amathawira kwa ine adzalandira dzikoNdipo adzatenga phiri langa loyera kukhala lake.+ 14  Ndiyeno wina adzanena kuti, ‘Konzani msewu! Konzani msewu! Konzani njira!+ Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’” 15  Chifukwa Wapamwamba ndi Wokwezeka,Amene adzakhalepo mpaka kalekale+ ndiponso dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti: “Ine ndimakhala pamalo apamwamba komanso oyera,+Koma ndimakhalanso ndi anthu opsinjika ndiponso amene ali ndi mtima wodzichepetsa,Kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozekaNdiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+ 16  Chifukwa ine sindidzatsutsana nawo mpaka kalekaleKapena kukhala wokwiya nthawi zonse.+Popeza mzimu wa munthu ukhoza kufooka chifukwa cha ine,+Ngakhale zinthu zopuma zimene ine ndinapanga. 17  Ine ndinakwiya chifukwa cha machimo amene ankachita pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+Choncho ndinamulanga, ndinabisa nkhope yanga ndipo ndinakwiya. Koma iye anapitiriza kuyenda ngati wopanduka,+ ankangotsatira zofuna za mtima wake. 18  Ine ndaona njira zake,Koma ndidzamuchiritsa+ nʼkumutsogolera,+Ndipo ndidzayambiranso kumutonthoza,+ iyeyo ndi anthu ake amene akulira.”+ 19  “Ndikulenga chipatso cha milomo. Mtendere wosatha udzaperekedwa kwa amene ali kutaliNdiponso kwa amene ali pafupi+ ndipo ndidzamʼchiritsa,” akutero Yehova. 20  “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde, imene singathe kukhala bata,Ndipo madzi ake akuvundula zomera zamʼnyanjamo ndiponso matope. 21  Oipa alibe mtendere,”+ akutero Mulungu wanga.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Ndipo tsoka wasiyana nalo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pabedi.”
Kapena kuti, “mʼmakhwawa.”
Kapena kuti, “ndidzitonthoze.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa.”
Nʼkutheka kuti akunena za kulambira mafano.
Mabaibulo ena amati, “mfumu.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “sunatope.”