Yesaya 62:1-12

  • Dzina latsopano la Ziyoni (1-12)

62  Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete,+Ndipo chifukwa cha Yerusalemu sindidzakhala pheeMpaka kulungama kwake kutawala kwambiri,+Ndiponso mpaka chipulumutso chake chitakhala ngati muuni woyaka moto.+  2  “Mitundu ya anthu idzaona kulungama kwako mkazi iwe,+Ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.+ Iwe udzapatsidwa dzina latsopano+Limene Yehova adzasankhe.*  3  Udzakhala chisoti chokongola mʼdzanja la Yehova,Ndiponso nduwira yachifumu mʼdzanja la Mulungu wako.  4  Sudzatchedwanso mkazi wosiyidwa,+Ndipo dziko lako silidzatchedwanso labwinja.+ Koma dzina lako lidzakhala Ndimakondwera Naye,+Ndipo dziko lako lidzatchedwa Mkazi Wokwatiwa. Chifukwa Yehova adzasangalala nawe,Ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.  5  Chifukwa mofanana ndi mmene mnyamata amakwatirira namwali,Ana ako aamuna adzakukwatira. Ngati mmene mkwati amasangalalira chifukwa cha mkwatibwi,Mulungu wako adzasangalala chifukwa cha iwe.+  6  Iwe Yerusalemu, ine ndaika alonda pamakoma a mpanda wako. Nthawi zonse, masana onse komanso usiku wonse, iwo asakhale chete. Inu amene mukutchula dzina la Yehova,Musapumule,  7  Ndipo pitirizani kupemphera kwa iye mpaka atakhazikitsa Yerusalemu,Inde, mpaka atamusandutsa chinthu choti anthu padziko lonse azichitamanda.”+  8  Yehova walumbira atakweza dzanja lake lamanja ndiponso mkono wake wamphamvu kuti: “Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu kuti chikhale chakudya chawo,Ndipo alendo sadzamwa vinyo wanu watsopano amene munamupeza movutikira.+  9  Koma anthu amene adzakolole mbewuzo ndi amene adzazidye ndipo adzatamanda Yehova.Amene adzakolole mphesa ndi amene adzamwe vinyoyo mʼmabwalo anga oyera.”+ 10  Dutsani mʼmageti, dutsani mʼmageti. Lambulani njira kuti anthu adutse.+ Konzani msewu, konzani msewu waukulu. Muchotsemo miyala.+ Anthu a mitundu yosiyanasiyana muwakwezere chizindikiro+ 11  Taonani! Yehova walengeza mpaka kumalekezero a dziko lapansi kuti: “Mwana wamkazi wa Ziyoni* mumuuze kuti,‘Taona! Chipulumutso chako chikubwera.+ Taona! Mphoto yake ili ndi iyeyo,Ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.’”+ 12  Iwo adzatchedwa anthu oyera, anthu amene Yehova anawawombola,+Ndipo iwe udzatchedwa Mzinda Umene Mulungu Anaufunafuna, Mzinda Umene Sanausiyiretu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pakamwa pa Yehova padzasankhe.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.