Yesaya 8:1-22

  • Kuukiridwa ndi Asuri (1-8)

    • Maheri-salala-hasi-bazi (1-4)

  • Musachite mantha⁠—“Mulungu ali nafe” (9-17)

  • Yesaya ndi ana ake anali ngati zizindikiro (18)

  • Muzifufuza chilamulo, osati kufunsira kwa ziwanda (19-22)

8  Yehova anandiuza kuti: “Tenga cholembapo chachikulu+ ndipo ulembepo ndi cholembera wamba* kuti, ‘Maheri-salala-hasi-bazi.’* 2  Ndipo ndikufuna kuti mboni zokhulupirika zitsimikizire mochita kulemba.* Mbonizo zikhale wansembe Uriya+ ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.” 3  Kenako ndinagona ndi mneneri wamkazi* ndipo anakhala woyembekezera. Pambuyo pake anabereka mwana wamwamuna.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Umupatse dzina lakuti Maheri-salala-hasi-bazi, 4  chifukwa mwanayo asanadziwe kuitana kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya zidzatengedwa nʼkupita nazo kwa mfumu ya Asuri.”+ 5  Yehova anandiuzanso kuti:  6  “Popeza anthu awa akana madzi a ku Silowa*+ amene amayenda pangʼonopangʼono,Ndipo akusangalala ndi Rezini ndiponso mwana wa Remaliya,+  7  Yehova adzawabweretseramadzi ambiri komanso amphamvu a mu Mtsinje*Omwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse. Mfumuyo idzadzaza timitsinje take tonseNʼkusefukira mʼmphepete mwake monse  8  Ndipo idzakokolola chilichonse mu Yuda. Idzadutsa nʼkusefukira, moti idzafika mpaka mʼkhosi.+Idzatambasula mapiko ake mpaka mʼlifupi mwa dziko lako,Iwe Emanueli.”*+  9  Inu mitundu ya anthu, vulazani anthu, koma inuyo muphwanyidwaphwanyidwa. Tamverani, inu nonse ochokera kumalekezero a dziko lapansi, Konzekerani kumenya nkhondo, koma muphwanyidwaphwanyidwa.+ Konzekerani kumenya nkhondo, koma muphwanyidwaphwanyidwa. 10  Konzani pulani, koma idzalephereka. Nenani zimene mukufuna, koma sizidzachitika,Chifukwa Mulungu ali nafe.*+ 11  Dzanja lamphamvu la Yehova linali pa ine, ndipo pofuna kundichenjeza kuti ndisayende panjira ya anthu awa, iye anati: 12  “Zimene anthu awa akumanena kuti ndi chiwembu, iwe usamanene kuti ndi chiwembu. Usamaope zimene iwo amaopa,Usamanjenjemere nazo. 13  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,+Ndi amene uyenera kumuopa,Ndipo ndi amene uyenera kumulemekeza.”+ 14  Iye adzakhala ngati malo opatulika,Koma kwa nyumba zonse ziwiri za Isiraeli,Adzakhala ngati mwala wopunthwitsa+Ndiponso ngati thanthwe lokhumudwitsa.Adzakhala ngati msampha komanso khwekhweKwa anthu okhala mu Yerusalemu. 15  Anthu ambiri pakati pawo adzapunthwa nʼkugwa ndipo adzathyoka.Iwo adzakodwa nʼkugwidwa. 16  Kulunga mawu olembedwa otsimikizira zimenezi.*Mata malamulo* pakati pa ophunzira anga. 17  Ine ndipitiriza kuyembekezera* Yehova,+ amene wabisira nkhope yake nyumba ya Yakobo,+ ndithu ndiziyembekezera iyeyo. 18  Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa+ tili ngati zizindikiro+ ndiponso ngati zodabwitsa mu Isiraeli, zochokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, amene amakhala mʼphiri la Ziyoni. 19  Ndipo atakuuzani kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu kapena anthu olosera zamʼtsogolo, omwe amalira ngati mbalame ndiponso kulankhula motsitsa mawu,” kodi mungavomere? Kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake? Kodi akuyenera kufunsira kwa anthu akufa pofuna kuthandiza anthu amoyo?+ 20  Mʼmalomwake, iwo azifufuza zimene chilamulo komanso maumboni olembedwa akunena! Iwo akamalankhula zosemphana ndi mawu amenewa, ndiye kuti ali mumdima.*+ 21  Ndipo aliyense adzadutsa mʼdzikolo akuzunzika ndiponso ali ndi njala.+ Chifukwa chakuti ali ndi njala komanso wakwiya, adzatukwana mfumu yake ndi Mulungu wake ndipo azidzayangʼana kumwamba. 22  Kenako adzayangʼana padziko lapansi ndipo adzangoonapo kuzunzika, mdima, kusowa mtengo wogwira, nthawi zovuta, mdima wandiweyani ndipo sadzaonapo kuwala.

Mawu a M'munsi

Dzina limeneli likusonyeza kuti anthu adzabwera mofulumira kudzalanda dziko la adani.
Mʼchilankhulo choyambirira, “cholembera cha munthu wochokera kufumbi.”
Kapena kuti, “zichitire umboni.”
Ameneyu anali mkazi wa Yesaya.
Silowa inali ngalande ya madzi.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
MʼChiheberi mawu akuti “Mulungu ali nafe” ndi tanthauzo la dzina lakuti Emanueli. Onani Yes. 7:14; 8:8.
Kapena kuti, “umboni wotsimikizira zimenezi.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “kuyembekezera mwachidwi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzaona mʼmbandakucha.”