Yobu 13:1-28

  • Yankho la Yobu likupitirira (1-28)

    • ‘Ndikanakonda kulankhula ndi Mulungu’ (3)

    • “Nonsenu ndinu madokotala osathandiza” (4)

    • “Ine ndikudziwa kuti sindinalakwe” (18)

    • Anafunsa chifukwa chake Mulungu akumuona ngati mdani wake (24)

13  “Inde, maso anga aona zonsezi,Khutu langa lamva komanso lazimvetsa.   Zimene inu mukuzidziwa, inenso ndikuzidziwa.Si ine munthu wamba poyerekezera ndi inu.   Ine ndikanakonda kulankhula ndi Wamphamvuyonse,Ndikulakalaka nditalankhula ndi Mulungu zokhudza mlandu wangawu.+   Koma inu mukundinamizira mabodza.Nonsenu ndinu madokotala osathandiza.+   Zikanakhala bwino mukanangokhala chete,Zimenezi zikanasonyeza kuti ndinu anzeru.+   Mvetserani mfundo zanga,Ndipo tcherani khutu pamene ndikufotokoza mlandu wanga.   Kodi mukulankhula zopanda chilungamo mʼmalo mwa Mulungu?Ndipo kodi mukulankhula zachinyengo mʼmalo mwa iye?   Kodi mukhala kumbali yake?*Kodi mungakhale kumbali ya Mulungu woona pamlandu wake?   Kodi zingakuyendereni bwino ngati atakufufuzani?+ Kodi mungamupusitse ngati mmene mungapusitsire munthu? 10  Iye adzakudzudzulani ndithu,Mukadzayesa kuchita mwachinsinsi zinthu zokondera.+ 11  Kodi kulemekezeka kwake sikudzakuchititsani mantha?Ndipo kodi sadzakuchititsani kuti mumuope? 12  Mawu anu anzeru* nʼchimodzimodzi ndi miyambi yosathandiza ngati phulusa.Mawu anu odziteteza ndi osathandiza ngati zishango zadothi. 13  Khalani chete pamaso panga, kuti ineyo ndilankhule. Kenako chilichonse chimene chingabwere kwa ine, chibwere. 14  Nʼchifukwa chiyani ndikuika moyo wanga pachiswe,*Komanso kunyamula moyo wanga mʼmanja? 15  Ngakhale Mulungu atandipha, ndipitirizabe kumukhulupirira,+Ndisonyeza pamaso pake kuti ndine wosalakwa.* 16  Ndikatero iye adzakhala chipulumutso changa,+Chifukwa munthu woipa* sangafike pamaso pake.+ 17  Mvetserani mawu anga mosamala,Mvetserani mwatcheru zimene ndikunena. 18  Onani, tsopano ndakonzeka kubweretsa mlandu wanga kuti uweruzidwe.Ine ndikudziwa kuti sindinalakwe. 19  Ndi ndani amene angatsutsane nane? Ngati nditapanda kulankhula, ndikhoza kufa.* 20  Inu Mulungu, mundichitire zinthu ziwiri zokha,*Kuti ndisabisale pamaso panu: 21  Chotsani dzanja lanu lolemera nʼkuliika kutali kwambiri ndi ine,Ndipo musapitirize kundiopseza.+ 22  Muitane ndipo ine ndivomera,Kapena ndilankhule ndipo inu mundiyankhe. 23  Kodi ndinalakwa chiyani, nanga machimo anga ndi ati? Ndiuzeni zimene ndinalakwa komanso tchimo langa. 24  Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,+Nʼkumandiona ngati mdani wanu?+ 25  Kodi mukufuna kuopseza tsamba louluzika ndi mphepoKapena kuthamangitsa udzu wouma? 26  Inu mukupitiriza kulemba milandu yoopsa yokhudza ine,Ndipo mukundilanga chifukwa cha machimo amene ndinachita ndili mnyamata. 27  Mwaika mapazi anga mʼmatangadza,Mumayangʼanitsitsa njira zanga zonse,Ndipo mumatsatira paliponse pamene phazi langa laponda. 28  Choncho munthu* amaola ngati chinthu chimene chayamba kuwonongeka,Ngati chovala chimene chadyedwa ndi njenjete.”*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Kodi mumukondera iyeyo?”
Kapena kuti, “osaiwalika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nʼchifukwa chiyani ndikunyamula mnofu wanga ndi mano.”
Kapena kuti, “Ndingaikire kumbuyo njira zanga.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mabaibulo ena amati, “Ngati alipo, ine ndikhala chete nʼkufa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Zinthu ziwiri zokha musandichitire.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “iye,” mwina kutanthauza Yobu.
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.