Yobu 15:1-35

  • Mawu achiwiri a Elifazi (1-35)

    • Ananena kuti Yobu saopa Mulungu (4)

    • Ananena kuti Yobu ndi wodzikuza (7-9)

    • ‘Mulungu sakhulupirira angelo ake’ (15)

    • ‘Munthu amene amavutika ndi woipa’ (20-24)

15  Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:   “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu opanda pake,*Kapena angadzaze mimba yake ndi mphepo yakumʼmawa?   Kungodzudzula ndi mawu okha nʼkopanda ntchito,Ndipo kulankhula kokha nʼkosathandiza.   Chifukwa iweyo ukupangitsa kuti anthu asamaope kwambiri Mulungu,Ndipo ukupangitsa kuti asamaganizire mozama za Mulungu.   Zolakwa zako nʼzimene zikukupangitsa kuti uzilankhula choncho,*Ndipo wasankha kulankhula mwa ukathyali.   Pakamwa pako mʼpamene pakusonyeza kuti ndiwe wolakwa, osati ine,Ndipo milomo yako ikukutsutsa.+   Kodi munthu woyambirira kubadwa unali iwe?Kapena kodi unabadwa mapiri asanakhaleko?   Kodi umamvetsera nkhani zachinsinsi za Mulungu?Kapena kodi umaona kuti wanzeru ndiwe wekha?   Ukudziwa chiyani chimene ife sitikudziwa?+ Ndipo nʼchiyani chimene umamvetsa chimene ifeyo sitingachimvetse? 10  Pakati pathu pali aimvi ndi okalamba,+Amuna omwe ndi achikulire kuposa bambo ako. 11  Kodi mawu otonthoza ochokera kwa Mulungu sakukukwanira?Kapena kodi kulankhula nawe mawu odekha sikunakukwanire? 12  Nʼchifukwa chiyani mtima wako ukudzikweza?Ndipo nʼchifukwa chiyani ukutiyangʼana mokwiya? 13  Chifukwa wakwiyira Mulungu,Nʼchifukwa chake ukulankhula mwa njira imeneyi. 14  Kodi munthu ndi ndani kuti akhale woyera?Kapena aliyense wobadwa kwa mkazi kuti akhale wolungama?+ 15  Iyetu sakhulupirira angelo ake,Ndipo ngakhale kumwamba si koyera mʼmaso mwake.+ 16  Nanga angakhulupirire bwanji munthu wonyansa amene amachita zoipa zokhazokha,+Munthu yemwe amamwa zinthu zopanda chilungamo ngati madzi? 17  Ine ndikuuza ndipo undimvetsere! Ndikufotokozera zimene ndaona, 18  Zimene anthu anzeru amanena,Zinthu zimene anamva kuchokera kwa makolo awo ndipo sanazibise.+ 19  Dziko linaperekedwa kwa iwowo basi,Ndipo palibe mlendo amene anadutsa pakati pawo. 20  Munthu woipa amazunzidwa masiku onse a moyo wake,Pa zaka zonse zimene zinasungidwira wolamulira wankhanza. 21  Amamva phokoso lochititsa mantha mʼmakutu ake,+Pa nthawi yamtendere achifwamba amamuukira. 22  Iye sakhulupirira kuti adzatuluka mumdima,+Ndipo akudikira kuti aphedwe ndi lupanga. 23  Amayendayenda pofunafuna chakudya ndipo amafunsa kuti: ‘Kodi chili kuti?’ Iye akudziwa bwino kuti tsiku lamdima layandikira. 24  Chisoni komanso mavuto zikungokhalira kumuchititsa mantha.Zipitiriza kumuchititsa mantha ngati mfumu yamphamvu imene yakonzekera kuyambitsa nkhondo. 25  Chifukwa amakweza dzanja lake kuti atsutsane ndi Mulungu,Ndipo amafuna kusonyeza kuti ndi wamphamvu kuposa Wamphamvuyonse. 26  Iye amalimbana ndi Mulungu mwamakani,Atatenga chishango chake cholimba komanso chochindikala. 27  Nkhope yake yanenepa,Ndipo mimba yake yakula chifukwa chonenepa.* 28  Iye amakhala mʼmizinda imene idzawonongedwe,Mʼnyumba zimene simudzakhala aliyense,Zimene zidzakhale milu ya miyala. 29  Iye sadzalemera ndipo chuma chake sichidzachuluka.Zinthu zake sizidzafalikira padziko. 30  Iye sangathe kuthawa mdima,Moto udzaumitsa nthambi yake,*Ndipo adzaphedwa ndi mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu.+ 31  Iye asasochere nʼkukhulupirira zinthu zopanda pake,Chifukwa zimene adzapeze zidzakhala zopanda pake. 32  Zimenezi zimuchitikira posachedwapa,Ndipo nthambi zake sizidzakula mosangalala.+ 33  Iye adzakhala ngati mtengo wa mpesa umene mphesa zake zimagwa zisanapse,Komanso ngati mtengo wa maolivi umene umayoyola maluwa ake. 34  Chifukwa msonkhano wa anthu oipa* ndi wopanda phindu,+Ndipo moto udzanyeketsa matenti a anthu aziphuphu. 35  Iwo amatenga pakati pamavuto nʼkubereka zinthu zoipa,Ndipo mimba yawo imatulusa zachinyengo.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “angayankhe ndi nzeru zokhala ngati mphepo.”
Kapena kuti, “Zolakwa zako zimaphunzitsa pakamwa pako.”
Kunenepa kumeneku kukuimira kuti munthuyu zinthu zikumuyendera bwino, amachita zinthu mosadziletsa komanso ndi wodzikuza.
Chimene ndi chiyembekezo chilichonse choti adzachira.
Kapena kuti, “ampatuko.”