Yobu 16:1-22

  • Yankho la Yobu (1-22)

    • “Ndinu otonthoza obweretsa mavuto” (2)

    • Ananena kuti Mulungu wamuponyera mivi (12)

16  Yobu anayankha kuti:   “Ndamvapo zinthu zambiri ngati zimenezi. Nonsenu ndinu otonthoza obweretsa mavuto!+   Kodi simusiya kulankhula mawu opanda pakewa?* Chikukupwetekani nʼchiyani kuti muziyankha chonchi?   Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu. Mukanakhala kuti mukukumana ndi mavuto ngati angawa,*Ndikanalankhula mawu ambiri okudzudzulaniKomanso kukupukusirani mutu.+   Koma sindikanatero, mʼmalomwake ndikanakulimbikitsani ndi mawu amʼkamwa mwanga,Ndipo mawu otonthoza apakamwa panga akanakulimbikitsani.+   Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa,+Ndipo ndikasiya kulankhula, ululu wanga sukutha.   Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+Wawononga onse amene amakhala mʼnyumba yanga.*   Komanso iye wandigwira ndipo anthu ena akuona zimenezi,Moti kuwonda kwangaku ndi umboni wonditsutsa.   Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula ndipo akundisungira chidani.+ Iye akundikukutira mano. Mdani wanga akundiyangʼana mokwiya nʼcholinga choti andivulaze.+ 10  Anthu atsegula kukamwa kwawo kuti andimeze.+Ndipo andimenya mbama pofuna kundichititsa manyazi.Iwo asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+ 11  Mulungu wandipereka kwa tianyamata,Ndipo wandiponya mʼmanja mwa oipa.+ 12  Ine ndinali pa mtendere koma iye wandiphwanya.+Wandigwira kumbuyo kwa khosi nʼkundimenyetsa pansi,Kenako wandiponyera mivi yake. 13  Anthu ake oponya mivi ndi uta andizungulira.+Iye waboola impso zanga+ ndipo sakumva chisoni,Wakhuthulira ndulu yanga pansi. 14  Iye akungokhalira kundiboola ngati khoma.Akundithamangira ngati msilikali. 15  Ndasoka ziguduli kuti ndibise khungu langa,+Ndipo ndakwirira ulemu wanga* mufumbi.+ 16  Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,* 17  Ngakhale kuti manja anga sanachite zachiwawa,Ndipo pemphero langa ndi loyera. 18  Iwe dziko lapansi, usabise magazi anga.+ Alole kuti alire mʼmalo mwa ine. 19  Ngakhale panopa, mboni yanga ili kumwamba,Amene angandichitire umboni ali mʼmwamba. 20  Anzanga akundinyoza+Pamene ndikupemphera kwa Mulungu ndikugwetsa misozi.+ 21  Wina aweruze pakati pa munthu ndi Mulungu,Ngati mmene angaweruzire pakati pa munthu ndi mnzake.+ 22  Chifukwa ndangotsala ndi zaka zochepa,Ndipo ndidzayenda mʼnjira imene sindidzabwereranso.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Kodi simusiya kulongololaku?”
Kapena kuti, “Moyo wanu ukanakhala ngati mmene moyo wanga ulili.”
Kapena kuti, “onse osonkhana nane.”
Kapena kuti, “mphamvu yanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga yanga.”
Kapena kuti, “pali mthunzi wa imfa.”