Yobu 17:1-16
17 “Mzimu wanga wasweka, masiku anga atha.Kumanda kukundidikirira.+
2 Anthu onyoza andizungulira,+Ndipo diso langa likuyenera kuyangʼanitsitsa* khalidwe lawo lopanduka.
3 Chonde, landilani chikole changa ndipo muchisunge.
Kodi pali winanso amene angagwirane nane chanza nʼkulonjeza kuti andithandiza?+
4 Mwawapangitsa kuti akhale osazindikira,+Nʼchifukwa chake simunawalemekeze.
5 Anthu amenewa amauza anzawo kuti agawana nawo chuma chawo,Pamene ana awo akulephera kuona bwinobwino chifukwa cha njala.
6 Iye wachititsa kuti anthu azindinyoza,+Mwakuti ndakhala munthu amene anthu akumulavulira kumaso.+
7 Chifukwa cha kuzunzika, maso anga ayamba kuchita mdima.+Manja ndi miyendo yanga zakhala ngati mthunzi.
8 Anthu owongoka mtima akuyangʼana zimenezi modabwa,Ndipo munthu wosalakwa wakhumudwa chifukwa cha anthu oipa.*
9 Wolungama akuyendabe panjira yake,+Ndipo amene ali ndi manja oyera, mphamvu zake zikuwonjezereka.+
10 Komabe, nonsenu mungathe kubwera nʼkuyambiranso kundinena,Chifukwa sindikuonapo aliyense wanzeru pakati panu.+
11 Masiku anga atha,+Zolinga zanga, zolakalaka za mtima wanga, zasokonezeka.+
12 Anzanga akumasintha usiku kuti ukhale masana.Iwo akunena kuti, ‘Chifukwa choti kuli mdima, kuwala kuyenera kuti kwayandikira.’
13 Ngati nditadikira, ku Manda* kudzakhala kunyumba kwanga.+Ndidzayala bedi langa mumdima.+
14 Ndidzaitana dzenje*+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’
Kwa mphutsi ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’
15 Ndiye chiyembekezo changa chili kuti?+
Kodi pali amene akuona kuti ndili ndi chiyembekezo?
16 Chidzapita* ku Manda* otsekedwa ndi zitsulo,Pa nthawi imene tonsefe tidzapitira limodzi kufumbi.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “likuyenera kukhala pa.”
^ Kapena kuti, “ampatuko.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “manda.”
^ Apa akunena chiyembekezo.
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.